Ndandanda ya Mlungu wa December 30
MLUNGU WOYAMBIRA DECEMBER 30
Nyimbo Na. 52 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 5 ndime 13-18 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Chivumbulutso 15–22 (Mph. 10)
Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu (Mph. 20)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: “Athandizeni Kuti ‘Akhazikike M’chikhulupiriro.’” Nkhani. Pomaliza, chitani chitsanzo chachidule chosonyeza mmene tingayambitsire phunziro la Baibulo Loweruka loyambirira m’mwezi wa January. Limbikitsani onse kuti adzayambitse nawo maphunziro a Baibulo.
Mph. 10: Thandizani Ana Anu Aang’ono Kukhala Ofalitsa. Nkhani yochokera m’buku la Gulu patsamba 81 ndime 4 mpaka tsamba 82 ndime 1. Funsani kholo lachitsanzo chabwino lomwe lili ndi mwana amene ndi wofalitsa wosabatizidwa. Kodi linamuthandiza bwanji kukhala wofalitsa wosabatizidwa?
Mph. 10: Sitikhala Tokha mu Utumiki. (2 Maf. 6:16) Nkhani yokambirana yochokera mu Buku Lapachaka la 2013 tsamba 47 ndime 3 mpaka tsamba 48 ndime 2. Pemphani omvera kuti afotokoze zimene tikuphunzirapo.
Nyimbo Na. 119 ndi Pemphero