Ndandanda ya Mlungu wa September 2
MLUNGU WOYAMBIRA SEPTEMBER 2
Nyimbo Na. 71 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 28 ndime 8-15 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 1 Akorinto 1–9 (Mph. 10)
Na. 1: 1 Akorinto 4:18–5:1-13 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Munthu Akamaona Kuti Akudziwa Kwambiri Anthu Kapena Malo Enaake Atsopano, Kodi Ndi Umboni Wakuti Munthu Akafa Amakabadwanso Kwinakwake?—rs tsa. 174 ndime 3-tsa. 176 ndime 1 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Mkhristu Angatani Kuti Akhalebe Wosangalala Ngakhale Kuti Akudwala?—Afil. 4:6, 7 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Zimene Munganene Pogawira Magazini mu September. Nkhani yokambirana. Kwa masekondi 30 mpaka 60, fotokozani chifukwa chake magaziniwo angakhale othandiza m’gawo lanu. Kenako, pogwiritsa ntchito nkhani zoyambirira za mu Nsanja ya Olonda, pemphani omvera kuti anene funso lochititsa chidwi ndiponso lemba limene angawerenge pogawira magaziniwo. Chitaninso chimodzimodzi ndi nkhani zoyambirira m’magazini ya Galamukani! Ngati nthawi ilipo mungachitenso zimenezi ndi nkhani ina imodzi m’magazini ya Nsanja ya Olonda kapena Galamukani! Chitani chitsanzo chosonyeza mmene mungagawirire magazini iliyonse.
Mph. 10: Zosowa za pampingo.
Mph. 10: Tsanzirani Chitsanzo cha Baranaba. Nkhani yokambirana. Pemphani omvera kuti afotokoze mmene chitsanzo cha Baranaba chingatithandizire pa ntchito yathu yolalikira.
Nyimbo Na. 65 ndi Pemphero