Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu June: Gawirani timapepala totsatirati: Sangalalani ndi Moyo Wabanja, Kodi Ndani Kwenikweni Akulamulira Dziko? ndi kakuti Kodi Mukufuna Kudziwa Choonadi? Mukapeza munthu wachidwi, musonyezeni mmene timaphunzirira Baibulo pogwiritsa ntchito buku lakuti Baibulo Limaphunzitsa Chiyani kapena kabuku kakuti Mverani Mulungu kapenanso kakuti Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha. July ndi August: Kabuku kakuti Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu kapena timabuku totsatirati: Kodi Mulungu Amatisamaliradi? Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira kapena kakuti Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu!, September: Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!
◼ Dziwani kuti, mu Utumiki Wathu wa Ufumu mupitiriza kukhala ndandanda ya misonkhano ya mlungu uliwonse. Komabe, mpingo suyenera kuchita misonkhano ya mpingo mlungu wa msonkhano wachigawo. Izi zizithandiza kuti abale azikhala ndi nthawi yokwanira yokonzekera msonkhano. Mabanja akulimbikitsidwa kuti azikambirana nkhani za misonkhano ya mlungu umenewo pa Kulambira kwa Pabanja.
◼ Pa msonkhano uliwonse, timafunika kuchita zinthu mwadongosolo komanso kuwonetsetsa kuti malo athu ndi aukhondo. Choncho si bwino kuti pa msonkhano wachigawo pazipezeka anthu ogulitsa malonda. Akalinde ayenera kuwadziwitsiratu mwaulemu kuti sakuyenera kugulitsa malonda awo pa msonkhano. Ngati akufuna kuyala malonda awo, ayenera kuchita zimenezi kutali ndi malo a msonkhano.