Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 6/13 tsamba 7
  • Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
km 6/13 tsamba 7

Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu

Mafunso otsatirawa tidzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira June 24, 2013. Taika tsiku limene likusonyeza mlungu umene mfundoyo idzakambidwe n’cholinga choti muthe kufufuza pamene mukukonzekera sukulu mlungu uliwonse.

1. Kodi Yesu ankatanthauza chiyani pa Yohane 3:14, 15 pamene ananena kuti: “Monga mmene Mose anakwezera njoka m’mwamba m’chipululu, momwemonso Mwana wa munthu ayenera kukwezedwa m’mwamba”? [May 6, w04 8/1 tsa. 25 ndime 6; it-1-E tsa. 505]

2. Kodi otsatira a Khristu amalandira liti mphoto ya moyo, kapena kuti kulowa m’moyo wokwanira? (Yoh. 6:53) [May 13, w03 9/15 tsa. 31 ndime 3]

3. Perekani chitsanzo chosonyeza mmene Yesu anaphunzitsira anthu opanda ungwiro zinthu zokhudza Atate wake? (Yoh. 8:28) [May 20, w11 4/1 tsa. 7 ndime 3]

4. Kodi tikuphunzirapo chiyani pa zimene Yesu anachita ‘pogwetsa misozi’ Lazaro, yemwe anali mnzake kwambiri atamwalira? (Yoh. 11:35) [May 20, w08 5/1 tsa. 24 ndime 3-5]

5. Kodi Yesu anapereka phunziro lotani kwa ophunzira ake pamene anasambitsa mapazi awo? (Yoh. 13:4, 5) [May 27, w12 11/15 tsa. 10 ndime 1-3; w99 3/1 tsa. 31 ndime 1]

6. Kodi mzimu wa Mulungu ungatitsogolere bwanji? (Yoh. 14:26) [May 27, w11 12/15 tsa. 14-15 ndime 9]

7. Mawu akuti “izi” amene akupezeka pa Yohane 21:15 akuimira chiyani, ndipo tikuphunzirapo chiyani? [June 3, w08 4/15 tsa. 32 ndime 11]

8. Mogwirizana ndi Machitidwe 2:44-47 ndi Machitidwe 4:34, 35, kodi Akhristufe tiyenera kukhala ndi mtima wotani? [June 10, w08 5/15 tsa. 30 ndime 5]

9. Mogwirizana ndi zimene lemba la Machitidwe 7:59 likunena, kodi Sitefano ankapemphera kwa Yesu? [June 17, w08 5/15 tsa. 31 ndime 2]

10. Kodi tingatsanzire bwanji Baranaba, ndipo tingapindule bwanji chifukwa chotsatira chitsanzo chake chimenechi? (Mac. 9:26, 27) [June 24, bt tsa. 65 ndime 19]

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena