Ndandanda ya Mlungu wa June 10
MLUNGU WOYAMBIRA JUNE 10
Nyimbo Na. 131 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 24 ndime 10-15 (Mph. 30.)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Machitidwe 1–4 (Mph. 10)
Na. 1: Machitidwe 1:15–26 ndi 2:1-4 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Anthu Adzasangalala Ndi Madalitso Otani M’tsogolo Chifukwa cha Dipo?—rs tsa. 126 ndime 1 mpaka 4 (Mph. 5)
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Maganizo a Anthu Ambiri Angayerekezeredwe Ndi Mphweya Wapoizoni?—Aef. 2:1, 2 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: N’chifukwa Chiyani Kuyang’ana Omvera N’kofunika? Nkhani yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki tsamba 124, ndime 1, mpaka tsamba 125, ndime 4. Chitani chitsanzo chachidule chosonyeza wofalitsa akulalikira, koma sakuyang’ana munthu amene akumulalikirayo. Kenako wofalitsayo achitenso chitsanzo china ndipo aziyang’ana munthu amene akumulalikirayo.
Mph. 10: Kodi Tinachita Zotani? Nkhani yokambirana yokambidwa ndi mlembi. Fotokozani zimene mpingo unachita pa nthawi ya Chikumbutso ndipo yamikirani mpingowo chifukwa chogwira ntchito mwakhama. Pemphani omvera kuti afotokoze zinthu zosangalatsa zimene anakumana nazo pamene ankagawira timapepala toitanira anthu ku Chikumbutso, kapena pamene ankachita upainiya wothandiza.
Mph. 10: “Kodi Mumakhala Wokonzeka Kusintha?” Mafunso ndi mayankho.
Nyimbo Na. 74 ndi Pemphero