Ndandanda ya Mlungu wa October 25
MLUNGU WOYAMBIRA OCTOBER 25
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 1 Mbiri 12-15
Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 8: Zilengezo. “Zimene Mungachite Ngati Mukufuna Mabuku Achinenero China Mwamsanga.” Nkhani.
Mph. 12: Umodzi Wathu wa Padziko Lonse Umalemekeza Yehova. Nkhani yochokera m’buku la Gulu, tsamba 165, ndime 2, mpaka kamutu ka patsamba 168. Pemphani omvera ena kuti afotokoze nkhani zimene anawerenga m’mabuku athu zosonyeza kuti umodzi wathu ndiponso chikondi zinathandiza ena kuchitira umboni.
Mph. 15: Kuchirikiza Dongosolo la Kagulu ka Utumiki Wakumunda. Nkhani ndi kukambirana. Kuyambira January 1, 2009, ofalitsa onse anagawiridwa ku timagulu ta utumiki wakumunda. Mkulu amene amayang’anira kagulu amatchedwa kuti “woyang’anira kagulu.” Ngati pampingo pali akulu ochepa ndipo mtumiki wothandiza ayenera kuchita mbali imeneyi, amatchedwa kuti “mtumiki wa kagulu.” Kodi ofalitsa angatsatire motani dongosolo limene lakonzedwa ndi amene akutsogolera kagulu ka utumiki wakumunda? (Aheb. 13:17) Ngati n’kotheka, amene akutsogolera kaguluko angathandize aliyense amene akufuna wina woyenda naye. Ndi bwino kuti ofalitsa ozolowera kulalikira azipezeka pa misonkhano imeneyi n’cholinga choti azithandiza ofalitsa atsopano amene sanazolowere kulalikira. Abale ndi alongo amene amakhala okonzeka kuyenda ndi ofalitsa osiyanasiyana, angathe kuthandiza anthu ambiri. (Miy. 27:17; Aroma 15:1, 2) Tonse tiyenera kuyesetsa kufika pamisonkhano imeneyi panthawi yake. Kulemekeza dongosolo la Mulungu limeneli ndiponso kuganizira antchito anzathu kungatithandize kutsatira malangizo amenewa.—Afil. 2:4.