Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 6/10 tsamba 3
  • Ndandanda ya Mlungu wa June 28

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndandanda ya Mlungu wa June 28
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
  • Timitu
  • MLUNGU WOYAMBIRA JUNE 28
Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
km 6/10 tsamba 3

Ndandanda ya Mlungu wa June 28

MLUNGU WOYAMBIRA JUNE 28

Nyimbo Na. 31

□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:

lv mutu 8 ndime 19-26, ndi bokosi la patsamba 94 ndi 96.

□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:

Kuwerenga Baibulo: 1 Mafumu 3-6

Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu

□ Msonkhano wa Utumiki:

Nyimbo Na. 4

Mph. 5: Zilengezo.

Mph. 15: Konzekerani Kugawira Magazini a July. Kukambirana ndi omvera. Kambiranani kwa mphindi imodzi kapena ziwiri nkhani zimene zili m’magaziniwo. Ndiyeno sankhani nkhani ziwiri kapena zitatu ndipo pemphani omvera kuti atchule mafunso ndi malemba okhudza nkhanizo amene angagwiritse ntchito pogawira magaziniwo. Chitani chitsanzo cha mmene angagawirire magazini iliyonse. Pomaliza chitani chitsanzo cha mmene tingayambitsire phunziro la Baibulo pa ulendo wobwereza.—Onani km 8/07 tsa. 3.

Mph. 15: Aphunzitseni Ali Aang’ono. Nkhani yokambirana ndi omvera. Timoteyo ankadziwika kuti anali mlaliki wolimbikira ndiponso waluso. (Afil. 2:20-22) China chimene chinam’thandiza kuti azichita zimenezi chinali chakuti mayi ake komanso agogo ake aakazi ankamupatsa malangizo auzimu kuyambira ali wamng’ono. (2 Tim. 1:5; 3:15) Malemba otsatirawa angathandize makolo kuti aphunzitse ana awo kulalikira mwaluso. (1) Muyambe kuyenda nawo mu ulaliki akadali aang’ono ndipo aphunzitseni kulalikira malinga ndi zaka zawo ndiponso zimene angathe kuchita. (Miy 22:6) (2) Muyambe ndinu kusonyeza kuti mumakonda kwambiri utumiki. (Afil. 1:9, 10) (3) Pa nthawi ya kulambira kwa pabanja ndiponso pazochitika zina muziwalimbikitsa kukonda ntchito yolalikira. (Deut. 6:6, 7) (4) Zolankhula ndi zochita zanu zizisonyeza kuti mumakonda utumiki. (Afil. 3:8; 4:8; 1 Tim. 1:12) (5) Khalani ndi chizolowezi cholowa mu utumiki nthawi zonse ndi banja lanu. (Mac. 5:41, 42) (6) Muzicheza ndi anthu amene amalimbikira ntchito yolalikira. (Miy. 13:20) Pemphani omvera kuti afotokoze zimene makolo awo ankachita zimene zinawathandiza kuti azikonda ndiponso azisangalala ndi utumiki.

Nyimbo Na. 41

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena