Ndandanda ya Mlungu wa June 21
MLUNGU WOYAMBIRA JUNE 21
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 1 Mafumu 1-2
Na. 1: 1 Mafumu 1:1-14
Na. 2: Kodi Kugwiritsa Ntchito Zifaniziro Polambira Kungakhudze Bwanji Tsogolo Lathu? (rs tsa. 438 ndime 3-6)
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Kumvera Mulungu Kumapindulitsa Mwakuthupi Ndiponso Mwauzimu?
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 15: Mabuku Ogawira mu July. Kukambirana ndi omvera. Fotokozani mwachidule zimene zili m’mabukuwo, ndipo chitani chitsanzo chimodzi kapena ziwiri.
Mph. 15: “Nthawi Zonse Khalani Wokonzeka Kuyambitsa Phunziro la Baibulo.” Kukambirana mwa mafunso ndi mayankho. Chitani chitsanzo chosonyeza mmene tingagwiritsire ntchito kapepala ka Kudziwa Choonadi poyambitsa phunziro la Baibulo pa ulendo wobwereza kwa munthu amene munamupatsa buku limene ligawiridwe mu July.