Ndandanda ya Mlungu wa June 14
MLUNGU WOYAMBIRA JUNE 14
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 2 Samueli 22-24
Na. 1: 2 Samueli 22:1-20
Na. 2: Kodi Chilamulo Chinakhala Motani Namkungwi Wotsogolera kwa Khristu? (Agal. 3:24)
Na. 3: Kodi Tiyenera Kuona Bwanji Chifaniziro Chilichonse Chimene Tinkalambira M’mbuyomu? (rs tsa. 437 ndime 5–tsa. 438 ndime 2)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 10: Kodi Tinachita Zotani pa Nyengo ya Chikumbutso? Nkhani yokambirana ndi omvera. Yamikirani mpingo chifukwa cha zimene unachita mu utumiki pa nyengo ya Chikumbutso, ndipo tchulani zimene zachitika chifukwa cha ntchitoyi. Pemphani omvera kufotokoza zimene anakumana nazo pamene amachita upainiya wothandiza.
Mph. 10: Mphunzitsi Wabwino Amathandiza Wophunzira Wake Kugwiritsira Ntchito Zimene Akuphunzira. Nkhani yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki, tsamba 60.
Mph. 10: “Kodi Diso Lanu Limalunjika Pachinthu Chimodzi?” Nkhani ya mafunso ndi mayankho.