Ndandanda ya Mlungu wa November 23
MLUNGU WOYAMBIRA NOVEMBER 23
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl-CN mutu 30, ndime 1-7
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Deuteronomo 28-31
Na. 1: Deuteronomo 30:1-14
Na. 2: Chifukwa Chake Tifunikira Kugwira Ntchito (lr-CN mutu 42)
Na. 3: Kodi Malemba Amanena Chiyani za Chiyembekezo cha “Khamu Lalikulu”? (rs-CN tsa. 209 ndime 3-5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 5: Konzekerani Kugawira Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Tchulani nkhani zimene mukuona kuti anthu a m’dera lanu angazikonde. Chitaninso chitsanzo chosonyeza mmene wofalitsa wozolowera kulalikira angathandizire wofalitsa watsopano kukonzekera ntchito yogawira magazini.
Mph. 25: “Kukhazikitsa Gawo la Chinenero China.” Kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Mukatha kukambirana ndime 4, wofalitsa mmodzi achite chitsanzo chosonyeza njira imene yafotokozedwa m’ndimeyi.