Ndandanda ya Mlungu wa November 9
MLUNGU WOYAMBIRA NOVEMBER 9
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl-CN mutu 29 ndime 1-12
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Deuteronomo 19-22
Na. 1: Deuteronomo 22:1-19
Na. 2: Zimene Tingachite Kuti Tikondweretse Mulungu (lr-CN mutu 40)
Na. 3: Kodi a 144,000 Ndi Ayuda Okha? (rs-CN tsa. 208 ndime 4–tsa. 209 ndime 2)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 10: Udindo Wathu Pogawira Mabuku ndi Magazini. Nkhani yokambirana ndi omvera kuchokera m’buku la Gulu, patsamba 133, ndime 1 mpaka 3. Tsindikani mfundo yakuti wofalitsa aliyense ali ndi udindo wogwiritsira ntchito zinthu za Ufumu mwanzeru.
Mph. 20: “Kodi Tizichita Ulendo Wobwereza Pakatha Nthawi Yaitali Bwanji?” Nkhani yokambirana mwa mafunso ndi mayankho. Chitani chitsanzo chosonyeza wofalitsa akuchita ulendo wobwereza n’cholinga choyambitsa phunziro la Baibulo.