Ndandanda ya Mlungu wa September 14
MLUNGU WOYAMBIRA SEPTEMBER 14
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl-CN mutu 26 ndime 1-7
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Numeri 26-29
Na. 1: Numeri 27:1-14
Na. 2: Kodi Kuphunzitsa Ana Kalingaliridwe ka Yehova Kumatanthauza Chiyani, Ndipo N’kofunika Bwanji? (Aef. 6:4)
Na. 3: Yesu Angatiteteze (lr-CN mutu 33)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 10: Kupanga Maulendo Obwereza. Nkhani yokambirana ndi omvera yochokera m’buku la Gulu. Kambiranani ndime zitatu kuyambira pa kamutu ka patsamba 97. Chitani chitsanzo chosonyeza mmene tingapangire ulendo wobwereza kwa munthu amene walandira mabuku omwe tikugawira.
Mph. 10: Kuyambitsa Maphunziro a Baibulo. Fotokozani kapena funsani ofalitsa kuti afotokoze zimene anakumana nazo patsiku lapadera loyambitsa maphunziro a Baibulo. Pogwiritsa ntchito mabuku ogawira a mwezi wa September, chitani chitsanzo cha mmene tingayambitsire phunziro la Baibulo paulendo woyamba.
Mph. 10: “Kodi Mungayankhe Bwanji?” Kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.