Ndandanda ya Mlungu wa July 13
MLUNGU WOYAMBIRA JULY 13
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl-CN mutu 22 ndime 9-14
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Levitiko 21-24
Na. 1: Levitiko 22:17-33
Na. 2: Kodi Amene Amachita Zinthu Zoipa Angasinthe? (lr-CN mutu 25)
Na. 3: Kodi Akhristu Oona Amachita Chiyani Kuti Athandize Osauka?
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph.5: Zilengezo.
Mph.20: “Kodi Mwakonzekera Phwando Lauzimu?” Ikambidwe ndi mlembi wampingo. Tchulani malo amene mpingo wanu ukachitire msonkhano wachigawo. Kambiranani bokosi lakuti, “Zofunika Kukumbukira pa Msonkhano Wachigawo.”
Mph.10: “Kugulitsa Malonda pa Misonkhano Yathu Yachigawo.” Nkhani ndi kukambirana ndi omvera. Tsindikani kufunika kobweretsa chakudya chamasana chopepuka m’malo mochoka pamalo a msonkhano kupita kukagula chakudya kwa ogulitsa chakudya m’misewu ndi ku malesitilanti apafupi ndi malo a msonkhanowo.