Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu March: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo. April ndi May: Tidzagawira magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Mukamachita maulendo obwereza kwa anthu achidwi, ngakhalenso amene anafika pa Chikumbutso kapenanso pa misonkhano ina koma safika pa misonkhano ya mpingo nthawi zonse, yesetsani kuwagawira buku latsopano la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? ndi cholinga choyambitsa phunziro la Baibulo. June: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Ngati eninyumba ali nalo kale bukuli, ofalitsa angagawire buku lina lililonse la masamba 192 lomwe masamba ake amasintha mtundu kapena buku lina lililonse limene linasindikizidwa chisanafike chaka cha 1992.
◼ Mipingo izipereka kwa ofalitsa magazini atsopano a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! akangofika. Zimenezi zidzathandiza kuti ofalitsa athe kudziwiratu bwino nkhani zimene zili m’magaziniwo asanawagawire mu utumiki wa kumunda.
◼ Ndandanda ya misonkhano yachigawo ya chaka chino sidzaikidwa mu Utumiki wa Ufumu, koma idzaikidwa mu Nsanja ya Olonda ya March 1, 2009. Tonse tikulimbikitsidwa kusunga magazini imeneyi. Komanso akulu ayenera kulengeza ku mpingo masiku ndi malo a msonkhano wachigawo umene mpingo wawo udzapita.