Ndandanda ya Mlungu wa February 9
MLUNGU WOYAMBIRA FEBRUARY 9
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl-CN mutu 14 ndime 1-12
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Genesis 25-28
Na. 1: Genesis 25:1-18
Na. 2: Mphunzitsi Waluso Anatumikira Anthu Ena (lr-CN mutu 6)
Na. 3: Chifukwa Chake Anthu Sangathetse Mavuto Ngakhale Atayesetsa (rs-CN tsa. 63 ndime 5 mpaka tsa. 64 ndime 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 8: Kapepala Katsopano Koitanira Anthu ku Misonkhano ya Mpingo. Nkhani yofotokoza zimene zili m’kapepalaka komanso mmene tingakagwiritsire ntchito. Kapepalaka kaziperekedwa kwa anthu onse ochita chidwi ndi uthenga wathu. Chitani chitsanzo cha mmene tingagawirire kapepalaka kunyumba ndi nyumba komanso paulendo wobwereza.
Mph. 10: Zokumana Nazo Poyambitsa Maphunziro a Baibulo. Fotokozani mmene zinayendera mwezi watha pampingo wanu, tsiku limene munasankha kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba. Alimbikitseni onse kuti azilowa nawo muutumiki patsiku lapadera limeneli.
Mph. 12: “Ntchito Yapadera Yoitanira Anthu ku Chikumbutso.” Kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Gawirani kapepala kamodzi kwa aliyense pamsonkhanowo ndipo kambiranani zimene zili m’kapepalako. Chitani chitsanzo cha mmene tingagawirire kapepalako.