Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira September 8
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Pemphani omvera kuti afotokoze nkhani za m’magazini atsopano zimene anthu m’gawo lanu achita nazo chidwi kwambiri. Apempheni kuti atchule mafunso ndi malemba amene agwiritsa ntchito poyamba kukambirana nkhanizo. Chitani zitsanzo zosonyeza zimene tingachite pogawira magaziniwo.
Mph.15: Thandizani Ophunzira Baibulo Kukhala Aphunzitsi. Nkhani yotengedwa mu Nsanja ya Olonda ya January 15, 2007, masamba 29-30, ndime 14-20. Phatikizanipo chitsanzo chachidule chosonyeza wofalitsa akufotokozera wophunzira Baibulo watsopano mmene msonkhano wa nkhani ya onse ndi Phunziro la Nsanja ya Olonda zimachitikira, ndi kumupempha kuti adzapezekepo.
Mph.20: Kulimbana ndi Maganizo Olakwika Muutumiki. Nkhani yotengedwa m’zofalitsa zathu yokambidwa ndi mkulu, yosonyeza mmene maganizo olakwika a anthu angakhudzire utumiki wathu. Fotokozani zimene tingachite kuti tithetse maganizo olakwikawo. Nthawi zina khalidwe lathu tikakhala muutumiki kapena tikamachita zinthu zina pamoyo wathu, lingathandize kwambiri kuthetsa maganizo olakwika a anthu otiona ndi kutsegula mitima yawo kuti alandire choonadi. Choncho m’pofunika kuti nthawi zonse tizisamala ndi zimene timalankhula ndi kuchita. (1 Pet. 2:12; 3:1, 2) Fotokozani zochitika za kwanuko kapena zimene munawerenga m’zofalitsa zathu zosonyeza mmene tingathetsere maganizo olakwika.
Mlungu Woyambira September 15
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Musankhe zilengezo zina mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno.
Mph.20: Kodi Tinachita Bwanji Chaka Chathachi? Nkhani ndi kukambirana ndi omvera. Ikambidwe ndi woyang’anira utumiki kapena mkulu wina woyenerera. Fotokozani zimene mpingo wanu unachita muutumiki chaka chautumiki chathachi, makamaka zinthu zabwino zimene munachita. Uyamikireni mpingowo. Konzani zakuti wofalitsa mmodzi kapena awiri adzasimbe zinthu zolimbikitsa zimene anakumana nazo. Tchulani mfundo imodzi kapena ziwiri zimene mpingo wanu uyenera kugwirirapo ntchito chaka talowachi, ndipo kambiranani zimene zingakuthandizeni kuwongolera.
Mph.15: Kodi Ndingafotokoze Bwanji Zimene Ndimakhulupirira Zokhudza Chilengedwe? Nkhani yotengedwa m’zofalitsa zathu. Pemphani omvera kuti anene zimene achita pofotokoza chifukwa chake amakhulupirira chilengedwe kwa anzawo akusukulu, kuntchito, kapena kwina kulikonse. Mungathe kukonzekeretsa pasadakhale munthu mmodzi kapena awiri kuti iwonso adzafotokoze zimenezi.
Mlungu Woyambira September 22
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Werengani lipoti la maakaunti ndi mawu oyamikira zopereka olembedwa pa sitetimenti. Kambiranani kalata yochokera ku nthambi imene ili patsamba 1.
Mph.20: Mudzalandira Mphoto Chifukwa cha Ntchito Yanu. Nkhani yotengedwa mu Nsanja ya Olonda ya April 15, 2005, kuyambira patsamba 28, ndime 5 mpaka kumapeto kwa tsamba 29. Funsani wofalitsa mmodzi kapena awiri achangu kuti afotokoze mwachidule mmene Yehova anawathandizira kupeza zofunika pamoyo kapena kuwalimbikitsa.
Mph.15: Konzekerani Kugawira Magazini ya Nsanja ya Olonda ya October 1 ndi Galamukani! ya October. Mwachidule, fotokozani mfundo za m’magaziniwa, ndipo funsani omvera kuti atchule nkhani zimene zingachititse chidwi anthu a m’gawo lanu. Kodi ndi mafunso komanso malemba ati amene angagwiritsidwe ntchito poyamba kukambirana nkhanizo? Khalani ndi chitsanzo chosonyeza mmene tingagwiritsire ntchito ulaliki wa mu Utumiki Wathu wa Ufumu. Mkulu mmodzi achite chitsanzo chachidule cha ulaliki umene wakonzekera pa nkhani imene ikugwirizana ndi gawo lanu.
Mlungu Woyambira September 29
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kuti apereke malipoti awo a utumiki wa kumunda a mwezi wa September. Konzani pasadakhale kuti wofalitsa mmodzi kapena awiri adzafotokoze zinthu zolimbikitsa zimene anakumana nazo polalikira mwamwayi panthawi ya msonkhano wachigawo, patchuthi, kapena panthawi ina.
Mph.15: Zosowa za pampingo.
Mph.20: “Tidzakhala ndi Ntchito Yapadera Yogawira Kapepala Kuyambira pa October 20 Mpaka pa November 16.”a Ngati timapepala tilipo, patsani aliyense kapepala kamodzi. Pokambirana ndime 2, fotokozani mwachidule zimene zili m’kapepalako. Pokambirana ndime 4, chitani chitsanzo cha mmene tingagawire kapepalako. Pokambirana ndime 5, chitani chitsanzo chosonyeza wofalitsa akugwiritsa ntchito kapepalako kuyambitsa phunziro la Baibulo paulendo wobwereza.
Mlungu Woyambira October 6
Mph.10: Zilengezo za pampingo.
Mph.15: Bokosi la Mafunso. Kukambirana ndi omvera. Phatikizanipo mfundo za mu Nsanja ya Olonda ya June 15, 2005, masamba 20-22, ndime 10-16.
Mph.20: “Phunzitsani Ena Kukonda Yehova.”b Ngati nthawi ilipo, pemphani omvera kuti apereke ndemanga pa malemba osagwidwa mawu.
[Mawu a M’munsi]
a Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
b Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.