Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 5/08 tsamba 2
  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira May 12
  • Mlungu Woyambira May 19
  • Mlungu Woyambira May 26
  • Mlungu Woyambira June 2
Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
km 5/08 tsamba 2

Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Mlungu Woyambira May 12

Nyimbo Na. 134

Mph.10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno. Pogwiritsa ntchito mfundo zimene zili pa tsamba 4, kapena ulaliki wina uliwonse umene ungakhale woyenera m’gawo lanu, chitani zitsanzo zosonyeza zimene tinganene pogawira Nsanja ya Olonda ya May 1 ndi Galamukani! ya May.

Mph.15: Tingapirire Mayesero Alionse. Nkhani yochokera mu Nsanja ya Olonda ya June 15, 2005, masamba 30 ndi 31. Sankhani ofalitsa angapo kuti afotokoze mmene Yehova wawathandizira kupirira mayesero.

Mph.20: Kodi Mungachite Upainiya M’miyezi Ikubwerayi? Nkhani yokambirana ndi omvera. Kambiranani masamba 112 ndi 113 m’buku la Gulu, pamene afotokoza zofunika kuti munthu ayenerere kukhala mpainiya wothandiza. Pemphani anthu apantchito amene anachita upainiya wothandiza ali pa tchuthi kuti afotokoze madalitso amene anapeza. Pemphani ana a sukulu amene anachita upainiya wothandiza ali pa tchuthi kuti afotokoze mmene anthu ena anawalimbikitsira ndiponso kuwathandiza. Kodi upainiyawo unawathandiza bwanji kupita patsogolo mwauzimu? Kodi ndi madalitso otani amene anapeza? Limbikitsani onse oyenerera kuti adzachite upainiya wothandiza m’miyezi ikubwerayi.

Nyimbo Na. 187

Mlungu Woyambira May 19

Nyimbo Na. 47

Mph.10: Zilengezo za pampingo. Kambiranani Bokosi la Mafunso.

Mph.15: Zosowa za pampingo.

Mph.20: “Mungathe Kukhala Olemera.”a Fotokozani ziyeneretso za upainiya wokhazikika zomwe zili pa masamba 113 ndi 114 m’buku la Gulu. Amene akufuna kuyamba upainiya pa September 1 ayenera kupereka mwamsanga fomu yofunsira upainiya.

Nyimbo Na. 206

Mlungu Woyambira May 26

Nyimbo Na. 103

Mph.10: Zilengezo za pampingo. Werengani lipoti la maakaunti ndi mawu oyamikira zopereka. Kumbutsani ofalitsa kuti apereke malipoti a utumiki wakumunda a mwezi wa May. Pogwiritsa ntchito mfundo zimene zili pa tsamba 4, kapena ulaliki wina uliwonse umene ungakhale woyenera m’gawo lanu, chitani zitsanzo zosonyeza zimene tinganene pogawira Nsanja ya Olonda ya June 1 ndi Galamukani! ya June.

Mph.15: “Senzani Goli Langa.”b Ngati nthawi ilipo, pemphani omvera kuti apereke ndemanga pa malemba osagwidwa mawu.

Mph.20: Gawirani buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani m’mwezi wa June. Nkhani ndi zitsanzo. Kambiranani maulaliki ena a mu mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 2006. Phatikizanipo chitsanzo cha mbali ziwiri. Mbali yoyamba, sonyezani zimene tinganene pogawira bukulo, ndipo mbali yachiwiri, sonyezani mmene tingapangire ulendo wobwereza ndi cholinga choyambitsa phunziro la Baibulo.

Nyimbo Na. 169

Mlungu Woyambira June 2

Nyimbo Na. 221

Mph.10: Zilengezo za pampingo.

Mph.20: Anthu Okhulupirika Amalandira Madalitso Ambiri. (Miy. 28:20) Nkhani ndiponso kukambirana ndi omvera. Ikambidwe ndi mlembi. Fotokozani mwachidule mmene Yehova wadalitsira mpingo wanu chifukwa chochita khama powonjezera utumiki miyezi ya March, April ndi May, ndipo yamikirani mpingowo. Lengezani chiwerengero cha amene anachita upainiya wothandiza, maphunziro a Baibulo atsopano amene anayambitsidwa, ndiponso fotokozani zinthu zina zabwino zimene anthu anachita mu utumiki. Pemphani omvera kuti afotokoze zimene anakumana nazo panthawi ya Chikumbutso ndi pogawira timapepala toitanira anthu kumwambowu. Ngati munakumana ndi zinthu zina zapadera muutumiki wa kumunda, mungachite chitsanzo chosonyeza zomwe zinachitikazo. Funsani ofalitsa awiri kapena atatu kuti afotokoze mwachidule madalitso amene anapeza pochita upainiya wothandiza.

Mph.15: “Khalani ‘Okonzekera Ntchito Iliyonse Yabwino.’”c Pemphani omvera kuti afotokoze mmene amakonzekerera ulaliki wa khomo ndi khomo ndiponso nthawi imene amakonzekera.

Nyimbo Na. 44

[Mawu a M’munsi]

a Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.

b Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.

c Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena