Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira April 14
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno. Pogwiritsa ntchito mfundo zimene zili pa tsamba 8, kapena ulaliki wina uliwonse umene ungakhale woyenera m’gawo lanu, sonyezani zitsanzo za zimene tinganene pogawira Nsanja ya Olonda ya April 1 ndi Galamukani! ya April.
Mph.15: “Sonyezani Kuti Ndinu Oyamikira.”a Ngati nthawi ilipo, pemphani omvera kuti apereke ndemanga pa malemba osagwidwa mawu.
Mph.20: “Limbikitsani Oferedwa.”b Pemphani omvera kuti afotokoze zinthu zosangalatsa zimene anapeza polimbikitsa munthu wina amene wokondedwa wake anamwalira.
Mlungu Woyambira April 21
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Werengani lipoti la maakaunti ndi mawu oyamikira zopereka olembedwa pa sitetimenti yochokera ku ofesi ya nthambi. Kumbutsani omvera kuti adzabweretse magazini a Nsanja ya Olonda ya May 1 ndi Galamukani! ya May ku Msonkhano wa Utumiki wa mlungu wotsatira, ndiponso kuti akakonzekere kudzakambirana ulaliki woyenererana ndi gawo lanu.
Mph.10: Zosowa za pampingo.
Mph.25: “Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova wa 2008.”c Ikambidwe ndi mlembi wa mpingo. Limbikitsani onse kuti ayambe mwamsanga kukonzekera msonkhano.
Mlungu Woyambira April 28
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kuti apereke malipoti a utumiki wakumunda a mwezi wa April. Mukafotokoza mwachidule zimene zili mu Nsanja ya Olonda ya May 1 ndi Galamukani! ya May, pemphani omvera kuti atchule nkhani zimene zingakhale zogwira mtima kwa anthu a m’gawo lanu ndipo afotokoze zifukwa zake. Apempheni kuti afotokoze mmene angachitire pogawira magaziniwo mwa kugwiritsa ntchito nkhani zimene angasankhe. Kodi angafunse funso lotani kuti ayambitse makambirano? Kodi ndi lemba liti m’nkhaniyo limene angagwiritse ntchito? Kodi angaligwiritse ntchito bwanji kuti ligwirizane ndi yankho la funsolo? Pogwiritsa ntchito chitsanzo chimene omvera angasankhe, kapena zitsanzo zimene zili mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno, sonyezani zimene mungachite pogawira magazini iliyonse.
Mph.15: Bokosi la Mafunso. Nkhani yokambirana ndi omvera.
Mph.20: “Tsatirani Mapazi Ake Mosamalitsa.”d Ngati nthawi ilipo, pemphani omvera kuti apereke ndemanga pa malemba osagwidwa mawu.
Mlungu Woyambira May 5
Mph.10: Zilengezo za pampingo.
Mph.15: Yehova Sadzakusiyani Konse. Nkhani yolimbikitsa yochokera mu Nsanja ya Olonda ya October 15, 2005, masamba 8 mpaka 11.
Mph.20: “Khalani Mtumiki Wopita Patsogolo.”e Pokambirana ndime 3, phatikizanipo ndemanga za m’buku la Sukulu ya Utumiki, masamba 6 mpaka 8, pamutu wakuti “Mmene Mungapindulire Mokwanira.”
[Mawu a M’munsi]
a Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
b Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
c Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
d Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
e Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.