Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/08 tsamba 7
  • Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
  • Timitu
  • KUWERENGA BAIBULO KWA MLUNGU NDI MLUNGU
Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
km 4/08 tsamba 7

Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu

Mafunso otsatirawa mudzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira April 28, 2008. Woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza nkhani zomwe zakambidwa m’kati mwa milungu ya March 3 mpaka April 28, 2008. Kubwerezaku kudzakhala kwa mphindi 30.

LUSO LA KULANKHULA

1. N’chifukwa chiyani kuli kofunika kugwiritsa ntchito mfundo za m’nkhani imene tapatsidwa, ndipo tingachite zimenezi motani? [be-CN tsa. 234 ndime 1 mpaka tsa. 235 ndime 1]

2. N’chifukwa chiyani mafunso ali ofunika kwambiri pophunzitsa? [be-CN tsa. 236 ndime 1 mpaka 5]

3. Kodi mafunso amathandiza bwanji omvera kuganiza pa nkhani imene tikukambirana? [be-CN tsa. 237 ndime 3 mpaka tsa. 238 ndime 1]

4. Kodi n’chifukwa chiyani kugwiritsa ntchito mafunso mwaluso pophunzitsa kuli kofunika kuti munthu afotokoze zakukhosi kwake? [be-CN tsa. 238 ndime 3 mpaka 5]

5. Kodi phindu logwiritsa ntchito mawu ofananitsa zinthu pophunzitsa ndi lotani? (Gen. 22:17; Yer. 13:11) [be-CN tsa. 240 ndime 1-3]

NKHANI NA. 1

6. Kodi n’chifukwa chiyani kuli kofunika kutsogolera anthu achidwi ku gulu la Yehova, ndipo tingachite bwanji zimenezi? [od-CN tsa. 99 ndime 2 mpaka tsa. 100 ndime 1]

7. Kodi mzimu woyera umathandiza bwanji atumiki a Mulungu masiku ano? (Yoh. 14:25, 26) [be-CN tsa. 19 ndime 2 mpaka 3]

8. Kodi kuwerenga kuli ndi phindu lalikulu kwambiri lotani? [be-CN tsa. 21 ndime 3]

9. Kodi kuphunzira kumaphatikizapo chiyani? [be-CN tsa. 27 ndime 3 mpaka tsa. 28 ndime 1]

10. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala ndi chidwi chothandiza anthu a m’gawo lathu amene amalankhula chinenero china? [od-CN tsa. 104 ndime 2]

KUWERENGA BAIBULO KWA MLUNGU NDI MLUNGU

11. N’chifukwa chiyani Yesu anawongolera munthu amene anatchula iyeyo kuti “Mphunzitsi Wabwino”? (Maliko 10:17, 18) [w08-CN 2/15 “Mawu a Yehova Ndi Amoyo—Mfundo Zazikulu za M’buku la Maliko”]

12. Kodi Yesu anagwiritsa ntchito mtengo wa mkuyu pofotokoza mfundo yotani yokhudza mtundu wa Isiraeli? (Maliko 11:12-14, 20, 21) [w03-CN 5/15 tsa. 26 ndime 2 ndi 3]

13. Kodi mawu amene mngelo Gabrieli anauza Mariya akuti ‘adzakhala ndi pathupi’ mzimu woyera utafika pa iye ndi mphamvu ya Mulungu itamuphimba, amatanthauza chiyani? (Luka 1:30, 31, 34, 35) [w08-CN 3/15 “Mawu a Yehova Ndi Amoyo—Mfundo Zazikulu za M’buku la Luka”; it-2 tsa. 56 ndime 2]

14. Kodi ophunzira a Yesu anachitadi zinthu “zosaloleka pa sabata”? (Luka 6:1, 2) [gt-CN 31]

15. Kodi tingaphunzirepo chiyani pa malangizo amene Yesu anapatsa Marita? (Luka 10:40-42) [w99-CN 9/1 tsa. 31]

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena