Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 9/07 tsamba 2
  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira September 10
  • Mlungu Woyambira September 17
  • Mlungu Woyambira September 24
  • Mlungu Woyambira October 1
Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
km 9/07 tsamba 2

Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Mlungu Woyambira September 10

Nyimbo Na. 225

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Gwiritsani ntchito mfundo zimene zili pa tsamba 4 kapena mfundo zina zothandiza m’gawo lanu, posonyeza zitsanzo za mmene tingagawirire Nsanja ya Olonda ya September 15 ndi Galamukani! ya September. M’zitsanzo zonsezo, agawire magazini onse awiri pamodzi ngakhale kuti agwiritsa ntchito magazini imodzi pokambirana. (Ngati mpingo wanu sunalandire magazini tatchulawa gwiritsirani ntchito zitsanzo za mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)

Mph. 15: Bokosi la Mafunso. Kukambirana ndi omvetsera. Ikambidwe ndi mkulu. Ngati nthawi ilipo, werengani ndi kukambirana malemba osagwidwa mawu.

Mph. 20: “Tsatirani Chitsanzo cha Yesu.”a Pemphani Omvetsera kuti afotokoze mmene apindulira ndi zitsanzo zabwino za anthu ena.

Nyimbo Na. 130 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira September 17

Nyimbo Na. 60

Mph. 10: Zilengezo za pampingo.

Mph. 15: Kodi Tinachita Bwanji Chaka Chatha? Woyang’anira utumiki afotokoze zimene zinachitika m’chaka cha utumiki chapitachi, makamaka zinthu zabwino zimene mpingo wanu unachita mu utumiki. Ndipo ayamikire zinthu zimenezo. Atchule chinthu chimodzi kapena ziwiri zimene mpingo ungayese kuwongolera m’chaka cha utumiki chatsopano. Atchule zimene apainiya akuchita ndipo awayamikire pa ntchito yawo yabwino. Atchule zinthu zabwino zimene zachitika chifukwa choyesayesa kuthandiza anthu amene anasiya kulalikira.

Mph. 20: Gulu Logwirizana la Abale. Nkhani ndi kukambirana ndi omvetsera mutu 16 wa buku la Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova.

Nyimbo Na. 74 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira September 24

Nyimbo Na. 162

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Werengani lipoti la maakaunti ndi mawu oyamikira zopereka olembedwa pasitetimenti.

Mph. 15: Zosowa za pampingo.

Mph. 20: Gwiritsani Ntchito Kapepala ka Kodi Mukufuna Kudziŵa Zambiri za Baibulo? Kuyambitsa Maphunziro a Baibulo mu October. Tidzagawira magazini ya Nsanja ya Olonda ndi ya Galamukani! mu October. Anthu akasonyeza chidwi, kapepala ka Kodi Mukufuna Kudziŵa Zambiri za Baibulo? kangagwiritsidwe ntchito kuyambitsa maphunziro a Baibulo. Pemphani akalinde kupereka kapepala kameneka kamodzi kwa aliyense amene wabwera, ngati timapepala tokwanira tilipo. Ndipo kambiranani kapepalaka mwachidule. Fotokozani kuti tingakambirane zonse kapena mbali zina za m’kapepalaka ndi mwininyumba paulendo woyamba kapena paulendo wobwereza. Gwiritsani ntchito mfundo zimene zili pa tsamba 4 kapena mfundo zina zothandiza m’gawo lanu, posonyeza zitsanzo za mmene tingagawirire Nsanja ya Olonda ya October 1 ndi Galamukani! ya October. M’chitsanzo chimodzi, mwininyumba akane kulandira magazini ndipo wofalitsa angomugawira kapepalaka. M’chitsanzo chinacho, mwininyumba alandire magazini ndipo wofalitsa amugawirenso kapepalaka. Ndipo wofalitsayo akambirane naye tsamba 5 kenako n’kumusonyeza kabokosi patsamba 6 kosonyeza buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani, ndipo anene kuti adzabweranso ndi bukuli. (Ngati mpingo wanu sunalandire magazini tatchulawa gwiritsirani ntchito zitsanzo za mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)

Nyimbo Na. 222 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira October 1

Nyimbo Na. 88

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Musankhe zilengezo zina mu Utumiki Wathu wa Ufumu. Kumbutsani ofalitsa kuti apereke malipoti awo a utumiki wa kumunda a mwezi wa September.

Mph. 15: Kalata Yochokera ku Nthambi. Nkhani ndi kukambirana ndi omvetsera kalata yomwe ili pa tsamba loyamba la Utumiki Wathu wa Ufumu uno. Pemphani omvetsera kuti afotokoze zimene akumana nazo poitanira anthu ku Msonkhano Wachigawo Wakuti “Tsatirani Khristu!”

Mph. 20: “Tiziyesetsa Kuwonjezera Utumiki Wathu.”b Abale ndi alongo amene akuyesa kuwonjezera utumiki wawo aperekepo ndemanga, ndipo apempheni kufotokoza zimene akuchita kuti apitirizebe kuchita zimenezi. Konzekeranitu pasadakhale kuti munthu mmodzi kapena awiri adzapereke ndemanga.

Nyimbo Na. 102 ndi pemphero lomaliza.

[Mawu a M’munsi]

a Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.

b Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena