Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 6/07 tsamba 2
  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira June 11
  • Mlungu Woyambira June 18
  • Mlungu Woyambira June 25
  • Mlungu Woyambira July 2
Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
km 6/07 tsamba 2

Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Mlungu Woyambira June 11

Nyimbo Na. 153

Mph.10: Zilengezo za pampingo. Gwiritsani ntchito mfundo zimene zili pa tsamba 4 kapena mfundo zina zothandiza m’gawo lanu, posonyeza zitsanzo za mmene tingagawire Nsanja ya Olonda ya June 15 ndi Galamukani! ya June. (Ngati mpingo wanu sunalandire magazini tatchulawa gwiritsirani ntchito zitsanzo za mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)

Mph.15: Okonzeka Mokwanira Kukhala Aphunzitsi a Mawu a Mulungu. Nkhani yochokera mu Nsanja ya Olonda ya February 15, 2002, masamba 24 mpaka 28. Akhristu ena amazengereza kuuza munthu wachidwi kuti ayambe kuphunzira naye Baibulo chifukwa chodziona kuti ndi osayenerera kupangitsa phunziro. Koma Yehova ndiye amatiyeneretsa kukhala atumiki. Ndipo amachita zimenezi mwa kugwiritsa ntchito Mawu ake, mzimu wake woyera, ndi gulu lake. Cholinga chathu sikungogawira mabuku koma tiyenera kuyesetsa kuphunzitsa anthu. (Mat. 28:19, 20) Chotero, limbikitsani ofalitsa kuti nthawi zonse azikhala ndi cholinga choyambitsa maphunziro a Baibulo.

Mph.20: Chitani Zonse ku Ulemerero wa Mulungu. Nkhani yokambirana ndi omvetsera yochokera m’buku la Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova, mutu 13.

Nyimbo Na. 144 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira June 18

Nyimbo Na. 217

Mph.10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno.

Mph.15: Kodi Mukukumbukira? Nkhani yokambirana ndi omvetsera yochokera mu Nsanja ya Olonda ya April 15, 2007, tsamba 19.

Mph.20: “Ndife Osangalala Kutumikira Yehova Modzipereka.”a Pemphani omvetsera kuti afotokoze malemba osagwidwa mawu ngati nthawi ingakuloleni.

Nyimbo Na. 82 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira June 25

Nyimbo Na. 15

Mph.10: Zilengezo za pampingo. Werengani lipoti la maakaunti ndi mawu oyamikira zopereka olembedwa pasitetimenti. Gwiritsani ntchito mfundo zimene zili pa tsamba 4 kapena mfundo zina zothandiza m’gawo lanu, posonyeza zitsanzo za mmene tingagawire Nsanja ya Olonda ya July 1 ndi Galamukani! ya July. (Ngati mpingo wanu sunalandire magazini tatchulawa gwiritsirani ntchito zitsanzo za mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)

Mph.15: Zosowa za pampingo.

Mph.20: “Kodi Mungalowe pa ‘Khomo la Ntchito Yaikulu’?”b Mwachidule funsani mpainiya wokhazikika mmodzi kapena awiri. Kodi n’zinthu zotani zimene anasintha pa moyo wawo kuti ayambe upainiya wokhazikika? Kodi alandira madalitso otani?

Nyimbo Na. 138 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira July 2

Nyimbo Na. 208

Mph.10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kuti apereke malipoti awo a utumiki wa kumunda a mwezi wa June. Tchulani timabuku togawira m’mwezi wa July, ndipo onetsani chitsanzo cha momwe tingagawire timabukuto.

Mph.15: Ulaliki Wamwamwayi Ndi Njira Yofunika Polalikira Uthenga Wabwino. Nkhani yokambirana ndi omvetsera yochokera m’buku la Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova, masamba 101 ndi 102. Nenani njira zimene ofalitsa angagwiritsire ntchito kuti alalikire mwamwayi. Pemphani omvetsera kuti afotokoze zokumana nazo zolimbikitsa zimene akhala nazo polalikira mwamwayi.

Mph.20: “Pitirizani ‘Kubala Zipatso Zambiri.’”c Pokambirana ndime 4, phatikizanipo ndemanga zokhudza bokosi lakuti, “Mmene ‘Tingabalire Zipatso Mopirira,’” lomwe lili mu Nsanja ya Olonda ya February 1, 2003, tsamba 21.

Nyimbo Na. 69 ndi pemphero lomaliza.

[Mawu a M’munsi]

a Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.

b Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.

c Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena