Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira March 12
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Gwiritsani ntchito malangizo amene ali pa tsamba 8 kapena ulaliki wina uliwonse woyenererana ndi gawo lanu, posonyeza zitsanzo za mmene tingachitire pogawira Nsanja ya Olonda ya March 15 ndi Galamukani! ya March. (Ngati mpingo wanu sunalandire magazini tatchulawa gwiritsirani ntchito zitsanzo zimene zinatchulidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)
Mph.15: Wachibale Akasiya Yehova. Nkhani yokambidwa ndi mkulu, yochokera mu Nsanja ya Olonda ya September 1, 2006, masamba 17 mpaka 21.
Mph.20: “Muzichita Zimenezi Pondikumbukira Ine.”a Pokambirana ndime 3, phatikizanipo ndemanga za mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa March 2006, tsamba 1, ndime 3, zonena mmene tingagwiritsire ntchito buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani pofotokoza za mwambo wa Chikumbutso kwa anthu achidwi omwe tikuwaitanira ku mwambowu.
Nyimbo Na. 168 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira March 19
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno. Kambani mfundo zazikulu za m’bokosi lomwe lili pa tsamba 7, lakuti “Zofunika Kukumbukira pa Chikumbutso.” Komanso tchulani masiku ndi malo a Msonkhano Wachigawo wa 2007 wakuti “Tsatirani Khristu!” umene mpingo wanu udzapite.
Mph.20: Njira Zowonjezera Utumiki Wanu. Nkhani ndi kukambirana ndi omvetsera yochokera m’mutu 10 wa buku la Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova.
Mph.15: “Kodi Mungayankhe Bwanji?”b Sonyezani chitsanzo chachidule cha mmene mbali imeneyi ingagwiritsidwire ntchito nthawi zina pa phunziro la banja.
Nyimbo Na. 216 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira March 26
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti a utumiki wa kumunda a mwezi wa March. Werengani lipoti la maakaunti ndiponso mawu oyamikira zopereka a pa sitetimenti yochoka ku nthambi. Gwiritsani ntchito malangizo amene ali pa tsamba 8 kapena ulaliki wina uliwonse woyenererana ndi gawo lanu, posonyeza zitsanzo za mmene tingachitire pogawira Nsanja ya Olonda ya April 1 ndi Galamukani! ya April. M’zitsanzozi gawiraninso kapepala kapadera koitanira anthu ku Chikumbutso. (Ngati mpingo wanu sunalandire magazini tatchulawa gwiritsirani ntchito zitsanzo zimene zinatchulidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)
Mph.10: Zosowa za pampingo.
Mph.25: “Zimene Mungachite Kuti Utumiki Wanu Waupainiya Uyende Bwino.”c Ikambidwe ndi woyang’anira utumiki. Ngati muli ndi nthawi mungawerenge ndime zake. Mukamakambirana ndime 12, funsani mafunso mpainiya wokhazikika. M’funseni kuti: Kodi n’chiyani chinakuthandizani kuti mukwanitse maola amene amafunika pachaka, chaka chautumiki chapitachi? Kodi munakumana ndi mavuto otani? Kodi mpingo unakuthandizani bwanji? Ngati kulibe mpainiya wokhazikika, kambiranani ziyeneretso za apainiya okhazikika.—od-CN 113.
Nyimbo Na. 148 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira April 2
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Kambiranani mawu oitanira anthu ku nkhani ya onse yapadera omwe ali pa tsamba lomaliza la Nsanja ya Olonda ya April 1, 2007. Limbikitsani ofalitsa kuti aitanire anthu achidwi ku nkhaniyi, yomwe idzakambidwe pa April 15.
Mph.20: Pitirizani Kuthandiza Anthu Omwe Anabwera ku Chikumbutso. Nkhani yokambidwa ndi mkulu. Tchulani chiwerengero cha anthu omwe anabwera pa Chikumbutso pampingo wanu, ndipo tchulani chiwerengero chomwe mukuganizira kuti ndi cha anthu okondwerera omwe analipo. Fotokozani zokumana nazo zosangalatsa kwambiri za anthu omwe analandira kapepala kapadera koitanira anthu ku Chikumbutso, kapena amene pambuyo pa mwambo wa Chikumbutsowo anapita kwa akalinde n’kupempha phunziro la Baibulo. Fotokozani mmene tingapitirizire kuwathandiza mwauzimu anthu amene anabwera pamwambowu. (Onani km-CN 3/06, tsa. 1, ndime 5; km-CN 2/05, tsa. 4, ndime 9; km-CN 2/04, tsa. 5, ndime 16.) Limbikitsani ofalitsa kuti ayambe kuchita zimenezi mwamsanga.
Mph.15: “Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira.”d
Nyimbo Na. 179 ndi pemphero lomaliza.
[Mawu a M’munsi]
a Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
b Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
c Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
d Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.