Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
DZIWANI IZI: Pakadutsa mwezi umodzi kapena iwiri mutachoka ku Msonkhano Wachigawo wa “Kumvera Mulungu,” dzagwiritseni ntchito mphindi 15 mpaka 20 za mu Msonkhano wa Utumiki (mwina mungagwiritse ntchito chigawo cha zosowa za pampingo) kuti mubwereze mfundo zazikulu za msonkhano wachigawo zimene ofalitsa aziona kukhala zothandiza mu utumiki wa kumunda. Mbali yapadera ya mu Msonkhano wa Utumiki imeneyi idzatipatsa mwayi wofotokoza mmene tikugwiritsira ntchito mfundo zimene tinaziphunzira kumsonkhano ndiponso kufotokoza mmene zathandizira utumiki wathu kukhala wogwira mtima.—Onani Utumiki Wathu wa Ufumu wa July 2005, tsa. 2.
Mlungu Woyambira August 8
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno. Kumbutsani ofalitsa za pulogalamu ya tsiku la msonkhano wapadera wa chaka cha utumiki cha 2006 ngati mukulidziwa.
Mph. 15: Kodi Mwayesapo Ulaliki Wosavuta Kuusintha? Nkhani yokambidwa ndi woyang’anira utumiki kuchokera mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 2005, tsamba 6. Kambani mfundo zimene zingakhale zoyenerera mogwirizana ndi gawo lanu.
Mph. 20: “Ino Ndiyo Nthawi Yofunika Kulalikira!” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Konzeranitu nthawi idakalipo zoti mpainiya wokhazikika mmodzi kapena awiri adzapereke ndemanga zokhudza zinthu zimene asintha n’cholinga choti achite upainiya ndiponso madalitso amene apeza chifukwa chochita zimenezo.
Nyimbo Na. 197 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira August 15
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Gwiritsani ntchito mfundo zimene zili patsamba 8 (ngati zingakhale zothandiza m’gawo lanu) kuchitira chitsanzo choonetsa mmene tingagawire Nsanja ya Olonda ya August 15 ndi Galamukani! ya September 8. Sonyezani mkulu ndi wofalitsa amene akudwala chifukwa cha ukalamba akuchita ulaliki wa pa telefoni. (Ngati magazini amenewa sanafike pampingopo, gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulaliki cha mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)
Mph. 15: Kodi Mukukumbukira? Kukambirana ndi omvera kuchokera mu Nsanja ya Olonda ya April 15, 2005, tsamba 30. Pemphani omvera kupereka ndemanga pa funso lililonse. Fotokozani phindu la nkhani imeneyi. Limbikitsani onse kuti aziwerenga magazini iliyonse ya Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!
Mph. 20: “Kuyambitsa Maphunziro a Baibulo Achidule Pakhomo ndi pa Telefoni.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo chitsanzo chachidule chosonyeza mmene tingayambitsire phunziro la Baibulo pa ulendo woyamba pogwiritsa ntchito ndime imodzi kapena ziwiri za m’bulosha la Mulungu Amafunanji. Simbani mwachidule chokumana nacho cholimbikitsa chimodzi kapena ziwiri zonena za kuyambitsa maphunziro kudzera pa telefoni.
Nyimbo Na. 30 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira August 22
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Werengani lipoti la maakaunti ndi mawu oyamikira zopereka olembedwa pa masitetimenti.
Mph. 15: Zosowa za pampingo.
Mph. 20: “Kulalikira Ufumu—Ntchito Yofunika Zedi.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Pokambirana ndime 4, bwerezani mfundo zokhudza dongosolo lapadera lochepetsa maola a utumiki wa kumunda kufika pa mphindi 15 kwa awo amene sangathe kuchita zambiri mu utumiki chifukwa cha ukalamba kapena matenda.—Onani Utumiki Wathu wa Ufumu wa October 2002, tsa. 8, ndime 6.
Nyimbo Na. 204 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira August 29
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti a utumiki wa kumunda a mwezi wa August. Mwa kugwiritsa ntchito mfundo zimene zili patsamba 8 (ngati zingakhale zothandiza m’gawo lanu), sonyezani chitsanzo choonetsa mmene tingagawire Nsanja ya Olonda ya September 1 ndi Galamukani! ya September 8. M’chitsanzo chimodzi, asonyeze akupanga ulendo wobwereza kwa munthu amene amakam’patsira magazini. (Ngati magazini amenewa sanafike pampingopo, gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulaliki cha mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)
Mph. 15: “Kupereka Umboni Popanda Mawu.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Pemphani ofalitsa ena kuti afotokoze mmene khalidwe labwino la anthu a Mulungu linawathandizira kuti akhale atumiki a Yehova.
Mph. 20: Gwiritsani Ntchito Baibulo Paulendo Woyamba. Nkhani ndi kukambirana ndi omvera. Kambani mfundo zimene zili mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa September 2004, tsamba 4, ndime 2, zosonyeza zimene tingachite kuti munthu achite chidwi ndi Mawu a Mulungu paulendo woyamba. Sonyezani chitsanzo kuonetsa mmene tingagwiritsire ntchito ulaliki umodzi kapena awiri amene ali mmenemo pamene tikugawira mabuku mu September. Ngati nthawi ilipo, mungathenso kukambirana ndi kusonyeza zitsanzo za maulaliki zimene zili mu mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 2005.
Nyimbo Na. 71 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira September 5
Mph. 10: Zilengezo za pampingo.
Mph. 15: “Kuchititsa Maphunziro a Baibulo Opita Patsogolo—Gawo 11.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Phatikizanimo chitsanzo chosonyeza wochititsa phunziro ndi wofalitsa watsopano akukonzekera za ulendo wobwereza. Akambirane mmene zinalili paulendo woyamba ndiyeno asankhe mfundo yabwino yoti akakambirane paulendo wobwereza. Akonzekerenso mawu oyamba osavuta ndiponso funso loti akam’funse mwininyumbayo pomalizira pake. Chitsanzocho chithere poti akufuna kuyeserera zimene akonzekerazo.
Mph. 20: “Konzani Zothandiza Okalamba.” Nkhani yokambidwa ndi mkulu. Fotokozani zimene mpingo wakonza zothandiza anthu amene akudwala ndiponso okalamba.
Nyimbo Na. 164 ndi pemphero lomaliza.