Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 11/02 tsamba 2
  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
  • Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira November 11
  • Mlungu Woyambira November 18
  • Mlungu Woyambira November 25
  • Mlungu Woyambira December 2
Utumiki wathu wa Ufumu—2002
km 11/02 tsamba 2

Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Mlungu Woyambira November 11

Nyimbo Na. 183

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe za mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno.

Mph. 15: Anthu Othandiza Kulambira Koona—Akale ndi Amasiku Ano. Nkhani yochokera mu Nsanja ya Olonda ya November 1, 2002, masamba 26 mpaka 30.

Mph. 20: “Thandizani Woyang’anira Phunziro Lanu la Buku la Mpingo.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Ikambidwe ndi mkulu amene ndi woyang’anira Phunziro la Buku la Mpingo. Pokambirana ndime 3, phatikizanipo ndemanga za mu buku la Sukulu ya Utumiki, patsamba 70. Yamikirani anthu mu mpingomo chifukwa cha zinthu zimene amachita pochirikiza phunziro la buku, ndipo gogomezerani mwachikondi mbali zilizonse zimene akufunika kuwongolera.

Nyimbo Na. 114 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira November 18

Nyimbo Na. 78

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti. Fotokozani dongosolo lapadera la utumiki wakumunda pa November 28. Mwa kugwiritsira ntchito mfundo za patsamba 8, sonyezani zitsanzo ziŵiri za momwe tingagaŵire Nsanja ya Olonda ya November 15 ndi Galamukani! ya December 8. M’chitsanzo chimodzi, fotokozani kumene kumachokera ndalama zimene timagwiritsira ntchito pantchito yathu ya padziko lonse.—Onani Nsanja ya Olonda, patsamba 2, kapena Galamukani! patsamba 5.

Mph. 10: Bokosi la Mafunso. Nkhaniyi ikambidwe ndi mkulu waluso.

Mph. 25: “Mitu ya Mabanja—Khalanibe ndi Ndandanda Yabwino Yochitira Zinthu Zauzimu.” Mukatha kukamba mawu oyamba achidule kuchokera mu ndime 1 mpaka 3, kambiranani nkhaniyi ndi omvetsera kuyambira ndime 4 mpaka 13. Nthaŵi ikalola, ŵerengani ndime 7, 8, 11 ndi 12. Komanso funsani kholo limodzi kapena makolo aŵiri. N’chiyani chathandiza banja lawo kukhala ndi ndandanda yabwino yochitira zinthu zauzimu? Kodi anafunika kuchita chiyani kuti zimenezi zitheke? Kodi apindula motani? Malizani ndi mawu achidule kuchokera mu ndime 14.

Nyimbo Na. 31 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira November 25

Nyimbo Na. 16

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Bwerezani mwachidule chitsanzo chimene chingagwiritsidwe ntchito pogaŵira buku lakuti Munthu Wamkulu.—Onani Utumiki Wathu wa Ufumu wa June 1998, tsamba 8.

Mph. 15: “Lalikirani Choonadi Chonena za Yesu.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo ndemanga za m’buku la Sukulu ya Utumiki, patsamba 278. Limbikitsani onse kubweretsa bukuli pa Msonkhano wa Utumiki wa mlungu wamawa, lidzagwira ntchito pankhani yakuti “Sukulu Imene Imatikonzekeretsa Kuchita Zinthu Zimene Zili Zofunika Kwambiri.”

Mph. 20: “Ganizirani ndi Kukonda ‘Ana Amasiye.’” Choyamba, kambani kwa mphindi zitatu mmene Yehova amaonera ana amasiye, kuchokera pandime 1. Malizani mbali yotsala ya nkhaniyi mwa mafunso ndi mayankho. Gogomezerani njira zabwino zimene ena angathandizire ndi kulimbikitsa anthu otereŵa. Pokambirana ndime 3 ndi 4, phatikizanipo ndemanga zachidule za mu Galamukani! ya October 8, 1995, masamba 8-9.

Nyimbo Na. 142 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira December 2

Nyimbo Na. 213

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti awo a utumiki wakumunda a November. Mwamuna ndi mkazi wake amene ali limodzi mu utumiki asonyeze momwe tingagwiritsire ntchito mfundo za patsamba 8 pogaŵira magazini ya Nsanja ya Olonda ya December 1 ndi Galamukani! ya December 8. Mwamunayo achite chitsanzo chogaŵira Nsanja ya Olonda, ndipo mkaziyo achite chitsanzo chogaŵira Galamukani!

Mph. 10: Zosoŵa za pampingo.

Mph. 25: “Sukulu Imene Imatikonzekeretsa Kuchita Zinthu Zimene Zili Zofunika Kwambiri.” Kukambirana ndi omvetsera ndipo ikambidwe ndi woyang’anira sukulu. Thandizani anthu kuyembekezera mwachidwi pulogalamu yatsopano ya sukulu, imene iyambe mu January. Tchulani mbali za “Ndandanda ya Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya 2003,” yomwe ndi mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa October 2002. Fotokozani zimene zimafunika kuti munthu aloŵe nawo m’sukuluyi, monga momwe anenera mu buku la Sukulu ya Utumiki, tsamba 282, ndipo limbikitsani amene sanalembetse kuti alembetse ngati akuyenera.

Nyimbo Na. 127 ndi pemphero lomaliza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena