Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/02 tsamba 2
  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
  • Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira April 8
  • Mlungu Woyambira April 15
  • Mlungu Woyambira April 22
  • Mlungu Woyambira April 29
  • Mlungu Woyambira May 6
Utumiki wathu wa Ufumu—2002
km 4/02 tsamba 2

Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Mlungu Woyambira April 8

Nyimbo Na. 39

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina muzisankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu.

Mph. 15: Zosoŵa za pampingo.

Mph. 20: “Chitirani Onse Chokoma.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Mukakambirana mwa mafunso ndi mayankho, funsani wofalitsa mmodzi kapena aŵiri afotokoze zimene akuchita kuti awonjezere utumiki wawo.

Nyimbo Na. 157 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira April 15

Nyimbo Na. 101

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti.

Mph. 15: Apainiya Pitirizani Kuthandiza Ena. Woyang’anira utumiki akambirane nkhaniyi ndi woyang’anira Phunziro la Buku la Mpingo, mpainiya, ndi wofalitsa. Woyang’anira utumiki apende pulogalamu ya Apainiya Athandiza Ena mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa September 1998, patsamba 4. Ndiyeno akambirane ndi aliyense wa anthu tatchula aja ntchito yawo m’pulogalamuyi ndi mmene ikuthandizira. Kodi achita zotani kuti zinthu ziyende bwino? Woyang’anira utumiki auze ofalitsa onse kuti ayenera kum’dziŵitsa ngati akufuna kuti wina awathandize mu utumiki. Aja amene anathandizidwa m’mbuyomo angathandizidwenso panopo mbali ina ya utumiki.

Mph. 20: “Utumiki wa Nthaŵi Zonse Umasangalatsa.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Limbikitsani achinyamata kufunsira upainiya wothandiza miyezi ikubwerayi.

Nyimbo Na. 199 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira April 22

Nyimbo Na. 90

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Mwa kugwiritsa ntchito mfundo za patsamba 8, khalani ndi zitsanzo ziŵiri za ulaliki zosonyeza mmene tingagaŵire Nsanja ya Olonda ya April 15 ndi Galamukani! ya May 8. M’zitsanzo zonsezi, sonyezani njira zosiyana za mmene tingachitire munthu akanena mawu otsekereza kukambirana akuti, “Ndili ndi chipembedzo changa.”—Onani buku la Kukambitsirana, pamasamba 18-19.

Mph. 10: Fikani Panthaŵi Yake. Nkhani. Ntchito za kulambira kwathu ndiponso utumiki wathu n’zofunika kwambiri, zili ndi “nthaŵi yake.” (Mlal. 3:1) Tikufuna kupindula kwambiri ndi makonzedwe a utumiki wathu kwa Mulungu. Misonkhano ya mpingo ndiponso yokonzekera utumiki wa kumunda iziyamba panthaŵi imene munasankha. Yehova sachedwa kugwira ntchito yake. (Hab. 2:3) Kodi tikufunika kuwongolera mbali imeneyi? Nthaŵi zina, ena sangachitire mwina, angachedwe basi. Koma ngati timakonzekera, sitiyenera kukhala ndi chizoloŵezi chochedwa, kufika pa msonkhano nyimbo yoyamba ndi pemphero zitatha kapena atamaliza msonkhano wa utumiki wa kumunda ndi kugaŵana mmene ayendere. Kambiranani njira zimene zingathandize kukhala ndi chizoloŵezi chabwino chimene chingatithandize kufika pa zochitika zonse zauzimu panthaŵi yake.—Onani Nsanja ya Olonda ya June 15, 1990, patsamba 29.

Mph. 25: “Makolo—Kodi Ana Anu Akukula Mwauzimu?” Kukambirana mwa mafunso ndi mayankho. Komanso kuti ena alimbikitsidwe, makolo pampingopo asimbe zimene achita pothandiza ana awo kukula mwauzimu.

Nyimbo Na. 191 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira April 29

Nyimbo Na. 162

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti awo a utumiki wa kumunda a April. Mwa kugwiritsa ntchito mfundo za patsamba 8, mtumiki wotumikira achite chitsanzo kusonyeza momwe tingagaŵire Nsanja ya Olonda ya May 1 ndipo mlongo asonyeze momwe tingagaŵire Galamukani! ya May 8. Pambuyo pa chitsanzo chilichonse bwerezani chiganizo chimodzi kapena ziŵiri zoyambirira zimene anagwiritsa ntchito podzutsa chidwi cha mwininyumba.

Mph. 15: “Kulalikira Ufumu Kumathandiza Kupulumutsa Anthu!” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Funsani omvetsera kunena momwe malembawo akugwirizanira ndi nkhaniyo.

Mph. 20: Gwiritsani Ntchito Buku la Kukambitsirana Pofufuza. Kukambirana ndi omvetsera. Nthaŵi zambiri mu utumiki, anthu amafunsa nkhani zimene sizili mu buku la Kukambitsirana pa “Nkhani Zazikulu” (masamba 5-6). “Zosonyezera” (masamba 439-45) zimathandiza kwambiri kupeza Malemba otsimikiza zikhulupiriro zathu. Pemphani omvetsera kufufuza mayankho a mafunso otsatiraŵa, ayang’ane mawu opendekekawo pa zosonyezera: Kodi Akristu amati chiyani pa nyimbo zautundu ndi mbendera? N’chifukwa chiyani Mulungu walola kuti masoka azichitika? Kodi mungafotokoze bwanji zimene Baibulo limanena pankhani ya chisudzulo? Kodi n’chifukwa chiyani alongo amafunika kuvala chophimba kumutu nthaŵi zina ndipo ndi nthaŵi ziti zimene afunika kuchita zimenezo? Kodi Tsiku la Amayi linayamba bwanji? Kodi timadziŵa bwanji kuti m’Baibulo 144,000 ndi chiŵerengero chenicheni? Kodi fanizo la munthu wachuma ndi Lazaro limatanthauza chiyani? Limbikitsani onse kugwiritsa ntchito buku la Kukambitsirana mu utumiki.

Nyimbo Na. 28 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira May 6

Nyimbo Na. 141

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Kambani nkhani yakuti “Pitirizani Kupindula ndi Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!”

Mph. 10: Kukonzekera Miyezi Ikubwerayi. Nkhani ndi kukambirana ndi omvetsera. Tchulani zimene zimakonda kuchitika miyezi ingapo ikudzayi: kupezeka pa msonkhano wonse wachigawo, kuchita upainiya wothandiza mwezi umodzi kapena ingapo, kusamalira panyumba, ndiponso mwina kupita kutchuti kapena kokasangalala. Pemphani anthu angapo anene zimene akonza kuti achite m’miyezi imeneyi ndiponso zimene adzachite kuti asadzaphonye phunziro la banja, misonkhano ya mpingo, ndi utumiki wa kumunda, ngakhale kuti akupita kwina. Ngati mpingowo uli ndi gawo limene sulalikiramo pafupipafupi, lengezani dongosolo limene mukukonza kuti gawolo mudzalifole lonse. Kumbutsani onse kupereka malipoti awo a utumiki wa kumunda kwa woyang’anira Phunziro la Buku la Mpingo, kaya ali kunyumba kapena achoka.

Mph. 25: “Kodi Tingatani Kuti Mabanja Athu Akhale Olimba Mwauzimu?” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Mukatha kukambirana nkhaniyi, simbani zokumana nazo zabwino za mu Nsanja ya Olonda ya February 15, 1999, masamba 10-12.

Nyimbo Na. 17 ndi pemphero lomaliza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena