Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 11/01 tsamba 2-7
  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira November 12
  • Mlungu Woyambira November 19
  • Mlungu Woyambira November 26
  • Mlungu Woyambira December 3
Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
km 11/01 tsamba 2-7

Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Mlungu Woyambira November 12

Nyimbo Na. 170

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu. Lengezani makonzedwe apadera opita mu utumiki wakumunda pa November 22.

Mph. 15: “Dalirani Yehova Kuti Akupatseni Mphamvu.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo ndemanga zachidule za mu Nsanja ya Olonda ya October 1, 1999, masamba 18-19, ndime 6-8.

Mph. 20:  Za m’Buku la Kukambitsirana. Kukambirana ndi omvetsera. Onani zitsanzo zili m’munsizi za mmene tingagwiritsire ntchito zinthu zosiyanasiyana za m’bukuli zimene zingathandize kwambiri pofotokoza ziphunzitso za Baibulo: Matanthauzo, monga a “Ufumu” (masamba 374-5) kapena “mzimu” (tsamba 319); kufanana kwa matembenuzidwe a mabaibulo osiyanasiyana pamene dzina la Mulungu limapezeka ndi momwe aligwiritsira ntchito (masamba 415-7) kapena zoona zake za helo (masamba 144-5); limafotokoza mwatsatanetsatane zikhulupiriro zimene zimatisiyanitsa ndi zipembedzo zina (masamba 270-2) kapena kusonyeza momwe munthu angadziŵire chipembedzo choona (masamba 89-91); umboni wakale wosonyeza momwe Khirisimasi inayambira (masamba 239-41) kapena kusaloŵerera m’ndale kwa Akristu oyambirira (masamba 371-4); umboni wa sayansi, woikira kumbuyo chilengedwe (masamba 74-6) kapena wosonyeza kuopsa kwa chamba ndi kusuta (masamba 250-3). Limbikitsani ofalitsa kugwiritsa ntchito chida chabwinochi mu utumiki wakumunda, ngati papezeka mpata wochita zimenezo.

Nyimbo Na. 191 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira November 19

Nyimbo Na. 172

Mph. 8: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti.

Mph. 15: Zosoŵa za pampingo.

Mph. 22: “Kulitsani Luso Lanu la Kuzindikira.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Mkulu atsogolere mosangalatsa kupenda pulogalamu ya tsiku la msonkhano wapadera umene unachitika chaka chautumiki chapitacho.

Nyimbo Na. 195 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira November 26

Nyimbo Na. 177

Mph. 15: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti a utumiki wakumunda a November. Sonyezani zitsanzo ziŵiri zokonzedwa bwino za ulaliki wa magazini mwa kugwiritsa ntchito malingaliro a mu “Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini.” M’chitsanzo chimodzi gwiritsani ntchito Nsanja ya Olonda ya December 1, ndipo chinacho gwiritsani ntchito Galamukani! ya December 8. Ndiyeno longosolani momwe tingapezere chitsanzo cha ulaliki wofunika kugwiritsa ntchito pogaŵira buku la Munthu Wamkulu kapena limodzi mwa mabuku amene tingagaŵire ngati mabuku ofunika kugaŵira mu December tilibe.

Mph. 15: “Kodi Ndingaipeze Kuti Nthaŵi?” Nkhani ndi kukambirana ndi omvetsera. Phatikizanipo mfundo zazikulu za mu Nsanja ya Olonda ya October 1, 2000, masamba 20-1, ndime 9-10, za pakamutu kakuti “Mmene Ena Amapezera Nthaŵi Yophunzira.” Pemphani omvetsera kunena njira zowathandiza kupeza nthaŵi yochitira zinthu zofunika kwambiri mwa kusachita zinthu zosafunika kwenikweni. Gogomezerani kufunika kogaŵa nthaŵi yathu kuti tichite phunziro laumwini ndi labanja, misonkhano ya mpingo, utumiki wakumunda, ndi kuŵerenga Baibulo tsiku lililonse.

Mph. 15: Ana Akutamanda Yehova. Kukambirana ndi omvetsera. Mipingo yambiri ili ndi ana ambiri amene amagwira nawo ntchito yolalikira. Akufunikadi kuchita zimenezi, ngakhale kuti nthaŵi zambiri amalalikira kwa anthu akuluakulu. (Sal. 148:12, 13; Mat. 21:15, 16) Ana amasangalala kwambiri mu utumiki wakumunda ngati makolo ndi ofalitsa ena achita nawo chidwi, kuwaphunzitsa ndi kuwalimbikitsa. Pemphani omvetsera kunena njira zimene zingathandize kutenganso ana mu ntchito ya ku khomo ndi khomo ndiponso ku ulendo wobwereza. Funsani makolo kusimba zimene achita pothandiza ana awo kuphunzira kugaŵira magazini, kugwiritsa ntchito Baibulo polalikira, ndi kulankhula motsimikiza panyumba ya munthu. Gogomezerani ubwino woyamikira ana. Funsani mwana mmodzi kapena aŵiri amene ndi wofalitsa kuti anene zimene amasangalala nazo polalikira ndiponso chifukwa chake.

Nyimbo Na. 198 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira December 3

Nyimbo Na. 179

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani onse kugaŵira mathirakiti ambiri a Kodi Mukufuna Kudziŵa Zambiri za Baibulo?

Mph. 20: “Tili ndi Chida Chatsopano Choyambitsira Maphunziro!” Kukambirana ndi omvetsera. Ikambidwe ndi woyang’anira utumiki. Akalinde apereke thirakiti latsopano lakuti Kodi Mukufuna Kudziŵa Zambiri za Baibulo?, kwa aliyense amene wabwera ngati mathirakitiwa alipo. Phatikizanipo zitsanzo ziŵiri zokonzedwa bwino, gwiritsani ntchito malingaliro a m’bokosi lakuti “Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini.” Wofalitsa mmodzi agwiritse ntchito Nsanja ya Olonda ya November 15, ndipo winayo agwiritse ntchito Galamukani! ya December 8. M’zitsanzo zonsezi, wofalitsa amalize mwa kum’patsa mwininyumbayo thirakiti lakuti Kudziŵa Baibulo—wina woti wakana kulandira magazini ndi wina woti walandira magazini. Limbikitsani onse kupereka mathirakiti atsopanoŵa kwa onse amene akumana nawo mu utumiki.

Mph. 15: “Madalitso Amene Amabwera Chifukwa Choyamikira Chikondi cha Yehova—Gawo 1.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Pokambirana ndime 3-6, pemphani anthu pampingopo kunena zinthu zabwino zimene zinawachitikira pamene anali kulalikira kunyumba ndi nyumba, mumsewu, ku ulendo wobwereza ndiponso pochititsa phunziro la Baibulo.

Nyimbo Na. 200 ndi pemphero lomaliza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena