Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 10/01 tsamba 2
  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira October 8
  • Mlungu Woyambira October 15
  • Mlungu Woyambira October 22
  • Mlungu Woyambira October 29
  • Mlungu Woyambira November 5
Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
km 10/01 tsamba 2

Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Mlungu Woyambira October 8

Nyimbo Na. 109

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu. Sonyezani zitsanzo ziŵiri zachidule za ulaliki wa magazini mwa kugwiritsa ntchito malingaliro a patsamba 8. M’chitsanzo chimodzi gwiritsani ntchito Nsanja ya Olonda ya October 15, ndipo chinacho gwiritsani ntchito Galamukani! ya November 8.

Mph. 35: “Kodi Mukugwiritsa Ntchito Zimene Munaphunzira ku Msonkhano Wachigawo Wakuti ‘Aphunzitsi a Mawu a Mulungu’?” Kukambirana ndi omvetsera pulogalamu ya msonkhano wachigawo. Ikambidwe ndi wochititsa Phunziro la Nsanja ya Olonda. Mukatha kukamba mawu oyamba m’mphindi imodzi, kambani za m’pulogalamu yatsiku lililonse mu mphindi 10 kapena 12. Kambani mfundo zazikulu pamutu uliwonse, ndiyeno pemphani omvetsera kulongosola (1) momwe ayesetsera kugwiritsa ntchito malangizowo, (2) momwe apindulira mwa kuchita zimenezo, ndiponso (3) zimene akuonanso kuti afunikira kuchita. Gwiritsani ntchito mafunso opangitsa anthu kuganiza kuti kukambirana kwanu kukhale kosangalatsa. Thandizani anthu onse kuzindikira kufunika kochita zimene anaphunzira.

Nyimbo Na. 151 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira October 15

Nyimbo Na. 113

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti.

Mph. 15: Kodi Muli ndi “Mtima Womvera”? (1 Maf. 3:9) Nkhani yokambidwa ndi mkulu, kuchokera mu Nsanja ya Olonda ya July 15, 1998, masamba 29-31. Longosolani njira zimene tingasonyezere kumvera pogwira ntchito ndi mpingo.

Mph. 20: Agwiritseni Ntchito Bwino Magazini Athu. Woyang’anira utumiki ndi mtumiki wa magazini akambirane mavuto a pa mpingowo pankhani yogaŵira magazini. Atchule chiŵerengero cha magazini amene mpingo umalandira mwezi uliwonse ndiye ayerekezere ndi chiŵerengero cha magazini amene anthu amaperekera lipoti kuti agaŵira. Malinga ndi umboni umene ulipo, magazini ambiri timangosunga kapena kutaya. Kodi ndi motani mmene ofalitsa angagwiritsire ntchito bwino magazini athu? Abalewo akambirane mfundo zisanu ndi ziŵiri za m’nkhani ya mu Msonkhano wa Utumiki wa mlungu woyambira October 4, 1999, yakuti “Khalani Ofunitsitsa Kugaŵira Magazini.” Apende chokumana nacho cha mu Nsanja ya Olonda ya February 15, 1998, masamba 28-9, ndipo apende njira zina zomwe malingalirowo angagwirire ntchito pa mpingowo. Tonse tikulimbikitsidwa kuyeseza zitsanzo za ulaliki zimene zimapezeka mu Utumiki Wathu wa Ufumu mwezi uliwonse.

Nyimbo Na. 156 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira October 22

Nyimbo Na. 120

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Sonyezani zitsanzo ziŵiri zachidule za ulaliki wa magazini mwa kugwiritsa ntchito malingaliro a patsamba 8. M’chitsanzo chimodzi gwiritsani ntchito Nsanja ya Olonda ya November 1 ndipo chinacho gwiritsani ntchito Galamukani! ya November 8.

Mph. 15: Kodi Mungayankhe Motani? Tchulani mwachidule za m’buku la Kukambitsirana, masamba 276-7, pamene akuyankha mwachindunji funso lakuti, “Kodi Mboni za Yehova zimafika motani pamalongosoledwe awo a Baibulo?” Sonyezani chitsanzo chokonzedwa bwino cha mmene tingayankhire funso limeneli paulendo wobwereza, ndiyeno muitanireni mwachikondi kuti azipezeka pamisonkhano ya mpingo.

Mph. 20: “Dziperekeni Pothandiza Anthu Atsopano.” Kukambirana nkhaniyi mwa mafunso ndi mayankho. Gogomezerani mfundo za m’nkhaniyi mwa kugwiritsa ntchito chokumana nacho chachidule chimodzi kapena ziŵiri zimene mwasankhiratu. Nenani motsindika ubwino wakuti ofalitsa ozoloŵera azikhala okonzeka kuthandiza anthu atsopano. Ngati n’kotheka, yambani nokha kuthandiza ndipo osamakana otsogolera akakupemphani kuti muthandize atsopano. Limbikitsani kuti onse aziloŵa mu utumiki wakumunda ndi magazini Loŵeruka, kapena tsiku limene anthu ambiri amapita ku msika wanu waukulu.

Nyimbo Na. 47 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira October 29

Nyimbo Na. 164

Mph. 12: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti a utumiki wakumunda a October. Mu November tidzagaŵira bulosha la Mulungu Amafunanji kapena buku la Chidziŵitso. Sonyezani chitsanzo cha ulaliki wachidule uwu: “M’nthaŵi ya mavuto a zachuma ino, anthu ambiri akuvutika kupeza zofunika pamoyo. Kodi mukuganiza kuti maboma a anthu adzathetsa vuto limeneli m’njira yokomera aliyense? [Yembekezerani yankho.] Lonjezo ili la m’Baibulo limandisangalatsa kwambiri.” Ŵerengani Salmo 72:12-14. Ndiyeno gaŵirani bulosha la Mulungu Amafunanji kapena buku la Chidziŵitso, phatikizanipo mawu a m’buloshalo kapena a m’bukulo ogwirizana ndi nkhaniyi.

Mph. 15: Zosoŵa za pampingo.

Mph. 18: “Kodi Mumadya Bwino Mwauzimu?” Kambani mawu oyamba m’mphindi yosaposa imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Funsani omvetsera kuthirira ndemanga pankhaniyi kuchokera mu Nsanja ya Olonda ya April 15, 1997, masamba 28-31, pofotokoza chifukwa chake tiyenera kuyesetsa kumadya bwino mwauzimu ndiponso mmene tingachitire zimenezi.

Nyimbo Na. 181 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira November 5

Nyimbo Na. 167

Mph. 10: Zilengezo za pampingo.

Mph. 18: Kukonzekera Misonkhano pa Banja. Atate akambirane ndi banja lawo momwe onse angakonzekerere kuti aziyankha pamisonkhano. Mwa kugwiritsa ntchito malangizo a mu Nsanja ya Olonda ya July 1, 1999, masamba 19-20, ndime 9, akonzekere ndemanga zokayankha pa Phunziro la Nsanja ya Olonda la mlungu uno. (1) Onse m’banjamo asankhe funso limodzi kapena aŵiri oti akayankhe. (2) Akatha kuŵerenga ndime zimene akayankhezo, akonze mayankho m’mawu awoawo. (3) Asankhe malemba ofunika kwambiri m’ndimezo amene sanagwidwe mawu, akambirane momwe lililonse likugwirizanira ndi nkhaniyo, ndipo akonze zonena pogwirizanitsa malembawo ndi phunzirolo. Onse akonzekere kukayankha pamsonkhano.

Mph. 17: “Kodi Cholinga Chathu N’chiyani?” Kambani mawu oyamba m’mphindi yosaposa imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Gogomezerani kufunika kothandiza ophunzira kuzindikira kufunika kopezeka pamisonkhano yampingo. Phatikizanipo chitsanzo chokonzedwa bwino cha mmene tingachitire zimenezi, mwa kugwiritsa ntchito buku la Chidziŵitso, mutu 17, ndime 6-8.

Nyimbo Na. 186 ndi pemphero lomaliza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena