Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira July 9
Mph. 8: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu.
Mph. 10: Lipoti la Utumiki Wakumunda la March. Nkhani ndiponso kufunsa, ikambidwe ndi woyang’anira utumiki. Tchulani lipoti la utumiki wakumunda la March, la dziko lanu ndiponso la mpingo wanu. Funsani ofalitsa angapo amene anawonjezera utumiki wawo mwezi umenewu. Apempheni kusimba chimwemwe chimene apeza chifukwa chochita zochuluka mu utumiki ndiponso anene zimene akuchita kuti akhalebe otanganidwa mu utumiki.—Onani m’mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa March 2001, ndime 28-30.
Mph. 12: “Misonkhano Yachigawo—Nthaŵi Yosangalala!” Nkhani yopatsa chidwi yokambidwa ndi woyang’anira sukulu ya Utumiki Wateokalase.
Mph. 15: “Kodi Mungatumikire ku Gawo Losoŵa Kwambiri?” Kambani mawu oyamba m’mphindi yosaposa imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo zokumana nazo zolimbikitsa zimene ofalitsa a pampingopo apeza m’magawo akutali kapena ogwiridwa ntchito mwa kamodzikamodzi.—Onani buku la Olinganizidwa, masamba 112-13.
Nyimbo Na. 42 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira July 16
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti.
Mph. 15: Achinyamata—Ŵerengerani Mtengo wa Ntchito Yanu. Bambo ndi mwana wawo wamwamuna kapena wamkazi wazaka zapakati pa 13 mpaka 19 alankhule ndi mkulu amene akudziŵa zambiri pankhani yantchito yolembedwa. Mwanayo atalingalira nkhani imene inakambidwa pa Msonkhano wa Utumiki masabata aŵiri apitawo yonena za kusankha ntchito, akuganiza mozama zoyamba utumiki waupainiya koma akudera nkhaŵa mmene angapezere zosoŵa zake zakuthupi. Mkuluyo agogomezere kufunika koona zinthu moyenera. (Nsanja ya Olonda ya September 1, 1999, tsamba 11, ndime 13) Ndi bwino kuphunzira maphunziro ena ake kuti athe kumapeza zofuna zawo. Anthu ambiri zinthu zikuwayendera bwino mwa kungophunzira maluso ofunika amene satenga nthaŵi ndiponso ndalama zambiri. (Nsanja ya Olonda ya February 1, 1996, tsamba 14; Achichepere Akufunsa, tsamba 178) Akambirane Galamukani! ya March 8, 1996, masamba 9-11, ndiponso malangizo ena othandiza pofuna ntchito kapena podzipezera chochita.
Mph. 20: Mboni za Yehova—Kodi Iwo Ndani? Kodi Amakhulupirira Chiyani? Kukambirana ndi omvetsera ndiponso chitsanzo. Pendani buloshali ndiponso kambiranani mmene tingaligwiritsire ntchito pouza ena za ife ndiponso ntchito yathu. Limalongosola za ife (masamba 3-5), limatchula ina mwa mbiri ndiponso zochita zathu zamakono (masamba 6-11), limatchula zikhulupiriro zomwe zimatisiyanitsa ndi zipembedzo zina (masamba 12-14), limafotokoza uthenga wabwino umene timalalikira ndiponso mmene timalalikirira uthengawo (masamba 15-21), limasonyeza momwe ntchito yathu imathandizira anthu (masamba 22-4), limanena zochita za gulu lathu la padziko lonse (masamba 25-6), ndipo limayankha mafunso amene anthu ambiri akhala akufunsa onena za ife (masamba 27-31). Sonyezani wofalitsa akugwiritsa ntchito buloshali kuyankha funso limodzi la patsamba 29 limene mwininyumba wachidwi wafunsa, kenako wofalitsa auze munthuyo chiitano chimene chili pachikuto chomalizira cha buloshali. Limbikitsani onse kugwiritsa ntchito buloshali kuti abale athu amene si Mboni atidziŵe bwino, komanso mukulitse chidwi paulendo wobwereza ndi kusonyezera ophunzira Baibulo ku gulu.
Nyimbo Na. 50 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira July 23
Mph. 8: Zilengezo za pampingo.
Mph. 10: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 12: “Mvetserani Ndipo Wonjezerani Kuphunzira.” Kambani mawu oyamba m’mphindi yosaposa imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
Mph. 15: “Konzekerani Kuphunzira Ulosi wa Yesaya!” Kambani mawu oyamba m’mphindi yosaposa imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Thirirani ndemanga mwachidule mmene tidzapindulire mwa kuphunzira buku la Yesaya. (Onani mutu 1, ndime 10-12, m’buku la Ulosi wa Yesaya 1.) Limbikitsani onse kupezeka pa Phunziro la Buku la Mpingo nthaŵi zonse.
Nyimbo Na. 53 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira July 30
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti awo a utumiki wakumunda a July.
Mph. 20: Achinyamata—Khalani Anzeru Posankha Maphunziro. Mkulu akambirane ndi makolo ena pamodzi ndi ana awo azaka zapakati pa 13 mpaka 19 pankhani ya maphunziro akusukulu owonjezera. Mkuluyo ayambitse kukambirana za mu Nsanja ya Olonda ya September 1, 1999 masamba 16-17, ndime 11-13, agogomezere chifukwa chake utumiki wanthaŵi yonse uyenera kukhala patsogolo pa zofuna zawo zonse. (Nsanja ya Olonda ya December 1, 1996, masamba 18-19, ndime 13-15) Ndiyeno onse apende uphungu wa mu Galamukani! ya March 8, 1998, masamba 27-28, agogomezere kufunika kwa nzeru poona ubwino ndi kuipa kwa maphunziro akusukulu owonjezera. Gogomezeraninso kufunika kochita zinthu zongofunika podzithandiza wekha kwinaku ukuchita utumiki mwachangu. Onse akuvomereza kuti atsatira mawu a Yesu oika Ufumu patsogolo.—Mat. 6:33.
Mph. 15: “Chitani Zabwino Ndipo Mudzatamandidwa!” Nkhani yokambidwa ndi woyang’anira wotsogolera.
Nyimbo Na. 57 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira August 6
Mph. 15: Zilengezo za pampingo. Pemphani omvetsera kusimba zokumana nazo za muulaliki wa mwamwayi popita ku msonkhano wachigawo, kutchuti, kapena kwa achibale amene si Mboni.
Mph. 10: “Dongosolo ‘Loyenera ndi Lolongosoka.’” Akulu aŵiri akambirane.
Mph. 20: “Musachite Mantha!” Kambani mawu oyamba m’mphindi yosaposa imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Ngati nthaŵi ilola, simbani zokumana nazo za mu Nsanja ya Olonda ya December 15, 1999, tsamba 25.
Nyimbo Na. 63 ndi pemphero lomaliza.