Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira February 14
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu.
Mph. 15: “Lalikira Mawu . . . Mwachangu.” Kambani mawu oyamba m’mphindi yosakwana imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo ndemanga za m’buku la Olinganizidwa, tsamba 170. Perekani malingaliro ena a mmene tingafutukulire ntchito yolalikira m’nthaŵi ya dzinja.
Mph. 20: “Mmene Tingakulitsire Luso la Kukambirana.” Nkhani ndi chitsanzo. Fotokozani chifukwa chake luso la kukambirana lili lofunika kwambiri mu utumiki ndi mmene tingalipezere. Ofalitsa odziŵa bwino aŵiri akambirane mmene angakonzekerere utumiki mwa kutsatira njira zimene zili m’ndime 3 ya nkhaniyi ndiyeno asonyeze chitsanzo cha ulaliki wawowo.
Nyimbo Na. 182 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira February 21
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti.
Mph. 15: “Akazi Amene Agwiritsa Ntchito mwa Ambuye.” Kambani mawu oyamba m’mphindi yosakwana imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo ndemanga za mu Nsanja ya Olonda ya September 15, 1996, masamba 14-15, ndime 18-19. Ayamikireni alongo chifukwa cha thandizo lawo la mtima wonse, ntchito zabwino zimene amachitira ena, ndi ntchito yawo yolalikira mwachangu.
Mph. 20: “Kodi N’chiyani Chimene Chingatithandize Kukhala Ochilimika M’chikhulupiriro?” Nkhani yokambidwa ndi mkulu. Tikukhala m’nthaŵi zovuta, ndipo tonsefe timafuna thandizo m’njira zosiyanasiyana. Pendani zimene akulu ndi atumiki otumikira angachite kulimbikitsa anthu amene akumana ndi mavuto olefula. (Onani kamutu kakuti “Kuŵeta Komangirira” mu Nsanja ya Olonda ya September 15, 1993, masamba 21-3.) Fotokozani mmene tonse tingalimbikitsirane m’njira zimene zidzatithandiza kukhala okhazikika mwauzimu.—Aroma 1:11, 12.
Nyimbo Na. 82 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira February 28
Mph. 17: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani onse kupereka malipoti a muutumiki wakumunda a February. Mwachidule pendani nkhani yakuti “Gwiritsani Ntchito Mabuku Athu Mwanzeru” patsamba 4 la Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha. Mwa kugwiritsa ntchito maulaliki ali m’ndime 4-7, sonyezani chitsanzo cha mmene tizigaŵira mabuku athu pogwiritsa ntchito makonzedwe atsopano a chopereka ameneŵa. Mwezi uno, tonse tiyenera kuyesetsa kwambiri kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba atsopano.
Mph. 10: Bokosi la Mafunso. Nkhani yokambidwa ndi mkulu.
Mph. 18: “Kulalikira Uthenga Wabwino ndi Chikhulupiriro Cholimba.” Kambani mawu oyamba mogwira mtima m’mphindi ziŵiri kapena zitatu kuchokera mu nkhaniyi komanso m’malemba amene aperekedwa osagwidwa mawu ndi ogwidwa mawu m’ndime 1 ndi 2. Ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho ndime 3-12.
Nyimbo Na. 61 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira March 6
Mph. 5: Zilengezo za pampingo.
Mph. 10: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 10: “Yang’anirani Mamvedwe Anu.” Bambo akambirane ndi mkazi wake pamodzi ndi ana ake zimene angachite kuti azipindula kwambiri ndi misonkhano ya mpingo, yadera, ndi yachigawo. Akuganiza kuti onse m’banjamo akufunikira kumamvetsera kwambiri. Apende malingaliro operekedwawo ndi mmene angagwiritsire ntchito lingaliro lililonse palokha, kuphatikizapo kufunika kokambirana kwambiri za zinthu zimene aphunzira. Apende mmene angachitire zimene agwirizanazo kuti asaphonye msonkhano uliwonse kapena mbali iliyonse ya msonkhano wachigawo kapena wadera ngati n’kotheka.
Mph. 20: “Kulalikira Uthenga Wabwino ndi Chikhulupiriro Cholimba.” Mukatha kupenda mwachidule zimene munakambirana mlungu watha m’ndime 12 zoyambirira m’mphatikayi, kambiranani mwa mafunso ndi mayankho ndime 13-24. Gwiritsani ntchito bwino malemba amene aperekedwawo ogwidwa mawu ndi osagwidwa mawu.
Nyimbo Na. 186 ndi pemphero lomaliza.