Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu April ndi May: Masabusikiripishoni a Nsanja ya Olonda. Khalani ndi bolosha la Mulungu Amafunanji kaamba ka anthu okondwerera, ndipo yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba. June: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. July ndi August: Mungagwiritse ntchito lililonse la mabolosha a masamba 32 ali m’munsiwa: Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso, Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani—Kodi Mungachipeze Motani?, Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, ndi Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha! Bolosha la Mizimu ya Akufa—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi Iyo Ilikodi? lingagaŵiridwe pamene kuli koyenera kutero.
◼ Kuyambira mwezi wamaŵa, mabaji a msonkhano wachigawo wa 1999 a m’Chingelezi adzatumizidwa pamodzi ndi mabuku. Simudzafunikira kuwaoda. Mabaji adzaikidwa m’mipukutu ya mabaji 25, malinga ndi kukula kwa mpingo uliwonse. Ngati mipingo ikufuna mabaji owonjezereka, ayenera kuoda pafomu ya Literature Order Form (S-14). Mungaode mapulasitiki oikamo mabaji kaamba ka aliyense amene akufuna mumpingo.
◼ N’koyenera kuti Sosaite izikhala ndi maadiresi amene akugwira ntchito a oyang’anira otsogoza ndi alembi onse. Ngati pali kusintha nthaŵi ina, mlembi ayenera kulemba ndi kutumiza mwamsanga fomu ya Kusintha Keyala ya Woyang’anira wotsogoza/Mlembi (S-29) ku Sosaite.
◼ Mipingo yomwe idzakhale ikuchezetsedwa ndi woyang’anira dera, tsiku lapadera kapena msonkhano wadera mapeto a mlungu wa April 18, 1999, ayenera kuika msonkhano wa nkhani yapadera patsiku Lamlungu lotsatira, April 25, 1999. Mipingo yomwe imakhala ndi msonkhano wapoyera tsiku lina lililonse kupatulapo Lamlungu ingaike msonkhano wapadera tsiku lina lililonse kuyambira pa April 19 mpaka April 24.
◼ Alembi a mipingo ayenera kusunga mafomu okwanira a apainiya ali m’munsiwa: Chofunsirapo Utumiki Waupainiya Wokhazikika (S-205), Chofunsirapo Utumiki Waupainiya Wothandiza (S-205b), ndi Chidziŵitso cha Kusiya Utumiki Waupainiya Wokhazikika (S-206). Zimenezi zingaodedwe pafomu ya Literature Order Form (S-14). Sungani zokwanira chaka chimodzi. Pendani mafomu a ofunsira upainiya wokhazikika kuti mutsimikize kuti alembedwa bwino. Ngati wofunsirayo sakukumbukira tsiku lenileni limene anabatizidwa, ayenera kungoyerekeza tsikulo ndiyeno alisunge.
◼ Makaseti Avidiyo Amene Alipo:
Jehovah’s Witnesses—The Organization Behind the Name—Chingelezi
Noah—He Walked with God—Chingelezi
◼ Kaseti Yatsopano ya Sewero Yomwe Ilipo:
Mabanja—Pangani Kuŵerenga Baibulo kwa Tsiku ndi Tsiku Kukhala Chizoloŵezi Chanu! —Chingelezi