Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/99 tsamba 5-6
  • Kupenda Kolemba m’Sukulu ya Utumiki Wateokalase

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kupenda Kolemba m’Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
km 4/99 tsamba 5-6

Kupenda Kolemba m’Sukulu ya Utumiki Wateokalase

Kupenda kolemba mabuku atatsekedwa pankhani zokambidwa m’Sukulu ya Utumiki Wateokalase zogaŵiridwa kuyambira mlungu wa January 4 kufikira April 19, 1999. Gwiritsirani ntchito pepala lina kuti mulembepo mayankho ambiri othekera m’nthaŵi yoperekedwa.

[Tamverani: Mkati mwa kupendaku, gwiritsirani ntchito Baibulo lokha kuyankhira funso lililonse. Magwero a nkhani amene amaikidwa pambuyo pa mafunso ngoti mukadzifufuzire. Manambala a tsamba ndi ndime nthaŵi zonse sangasonyezedwe m’magwero onse a mu Nsanja ya Olonda.]

Yankhani kuti Zoona kapena Kunama m’ndemanga zotsatirazi:

1. Yehova sanatchule liwu lililonse limene linalembedwa m’Baibulo. (2 Tim. 3:16) [w97-CN 6/15 tsa. 5 ndime 3]

2. Kugwirizana pabanja ndi kukula kwauzimu kwa ana kumadalira kotheratu pa makolo. (Miy. 22:6) [fy-CN tsa. 85 ndime 19]

3. Popeza kuti ‘uchimo [unali] kubwatama pakhomo,’ Kaini sakanapewa kuchita tchimo lalikulu. (Gen. 4:7) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w94-CN 6/15 tsa. 14 ndime 11.]

4. Pamene wachinyamata akukula, ayenera kupatsidwa ufulu wochuluka wa kusankha zosangulutsa. [fy-CN tsa. 73 ndime 20]

5. Chikhumbo chokondweretsa Mlengi wathu chimatisonkhezera bwino kwambiri kuti tizilankhula choonadi nthaŵi zonse. (Miy. 6:17) [g97-CN 3/8 tsa. 19 ndime 4]

6. Kuti ‘mawu a m’kamwa mwathu ndi maganizo a m’mtima mwathu avomerezeke pamaso pa Yehova’ m’pemphero, tiyenera kuyesetsa kukhala olankhula mwaluso kwambiri monga mmene tingathere. (Sal. 19:14) [w97-CN 7/1 tsa. 29 ndime 4-5]

7. Maweruziro, malemba, ndi malamulo a Yehova otchulidwa pa Genesis 26:5 ndiwo aja a pangano la Chilamulo. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w92-CN 7/1 tsa. 10 ndime 8.]

8. Pamene Yesu anati “chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe,” monga momwe kwalembedwera pa Luka 8:48, anali kutanthauza kuti mkazi wodwalayo anafunika kuyamba wavomereza kuti anali kumkhulupirira iye monga Mesiya asanamchiritse. [w97-CN 7/1 tsa. 4 ndime 2-4]

9. Lemba la Genesis 11:1 ndi limodzi mwa malemba ochuluka m’Baibulo amene amagwiritsa ntchito mawu akuti “dziko” kunena mtundu wa anthu, kapena anthu onse. [g97-CN 1/8 tsa. 31 ndime 3]

10. Ngakhale kuti panalibe chisonyezo chilichonse choti Dina anagwirizana nazo, komabe iye anali ndi mlandu ndithu chifukwa chotaya unamwali wake. (Gen. 34:1, 2) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w85 6/15 tsa. 31 ndime 4.]

Yankhani mafunso otsatirawa:

11. Kodi Satana anapereka malingaliro otani mwa kukambirana komwe kuli pa Genesis 3:1-5? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w95-CN 7/15 tsa. 5 ndime 2.]

12. Pa Chivumbulutso 19:15, kodi “lupanga lakuthwa” limene likutuluka m’kamwa mwa Yesu likuimira chiyani? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w90-CN 5/15 tsa. 4 ndime 4.]

13. Kodi nchiyani chimene Mose anagogomezera mwa kupereka madeti enieni a Chigumula cha m’tsiku la Nowa? [g97-CN 2/8 tsa. 18 ndime 4]

14. Kodi ndi motani mmene Abrahamu ‘anaitanira dzina la Yehova’? (Gen. 12:8) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w89-CN 7/1 tsa. 20 ndime 9.]

15. Malinga ndi nkhaniyo, kodi Yehova anatanthauzanji pamene anauza Paulo kuti: “Chisomo changa chikukwanira”? (2 Akor. 12:9) [w97-CN 6/1 tsa. 25 ndime 3]

16. Kodi nchiyani chimene chingakhale chitasonkhezera mkazi wa Loti kuti ayang’ane kumbuyo, nkumchititsa kukhala mwala wa mchere? (Gen. 19:26) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w90-CN 4/15 tsa. 18 ndime 10.]

17. Kodi kugula katundu wakuba Akristu amakuona motani? (Eks. 22:1; Yer. 17:11) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w92-CN 6/15 tsa. 30 ndime 3; tsa. 31 ndime 1, 6-7.]

18. Mogwirizana ndi Genesis 33:18, kodi Yakobo anasonyeza motani kuti sanali kufuna kuyanjana ndi Akanani? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w95-CN 9/15 tsa. 21 ndime 4.]

19. Kodi zochita za Yosefe zolongosoledwa pa Genesis 37:13 zinafanana motani ndi za Yesu? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w87-CN 5/1 tsa. 12 ndime 12.]

20. Kodi Mulungu ndi anthu amasiyana motani posonyeza mkwiyo? [g97-CN 6/8 tsa. 12 ndime 2, 3]

Pezani liwu kapena mawu ofunika kutsiriza ndemanga zotsatirazi:

21. ․․․․․․․ zolinga za ena popanda chifukwa ․․․․․․․ kuli ngati kuwaweruza. [w97-CN 5/15 tsa. 26 ndime 5]

22. Pamisonkhano ya mpingo, mungadziteteze ku kukhala ndi maganizo osakhazikika kapena kulota masana mwa ․․․․․․․. [sg-CN tsa. 26 ndime 7]

23. Zitsanzo za Rehabiamu ndi Eli zingathandize makolo kuzindikira zomwe zimachitika pamene akhala ․․․․․․․ kwambiri kapenanso ․․․․․․․ kwambiri polera ana. [fy-CN mas. 80-1 ndime 9-13]

24. Kuloŵetsa ․․․․․․․ ndilo sitepi lofunika kwambiri pa kukhala ndi ․․․․․․․ chaumulungu. [w97-CN 8/1 tsa. 4 ndime 5]

25. Kuulula tchimo ndiko chikondi cha lamulo chachikristu kwa ․․․․․․․, ndiponso kwa ․․․․․․․. [w97-CN 8/15 tsa. 30 ndime 2]

Sankhani yankho lolondola m’ndemanga zotsatirazi:

26. Chilango (chonkitsa; chopepuka; choyenera) chili umboni wa chikondi cha kholo kwa mwana wake. (Aheb. 12:6, 11) [fy-CN tsa. 72 ndime 18]

27. Genesis 7:6, 11 amasonya ku chaka cha (2970; 2370; 2020) B.C.E., “pamene chigumula cha madzi chinali pa dziko lapansi.” [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani tchati mu si tsa. 294.]

28. Pa Yohane 8:32, Yesu anali kulingalira za kumasuka ku (ulamuliro wa Roma; mwambo; uchimo ndi imfa). [w97-CN 2/1 tsa. 5 ndime 1]

29. M’kukwaniritsidwa komaliza kwa Genesis 22:18, mbewuyo ndi (Isake; Aisrayeli; Yesu ndi a 144,000). [ 9, Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w98-CN 2/1 tsa. 14 ndime 8.]

30. Kunali (kumvera Chilamulo cha Mose; kudziŵa kuti Mulungu alipo ndi kukhala ndi mantha oyenerera a kusamkondweretsa; kuopa chilango) kumene kunathandiza Yosefe kukana chiyeso cha chigololo. (Gen. 39:9) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w81 2/15 tsa. 7 ndime 2.]

Gwirizanitsani malemba otsatirawa ndi ndemanga zondandalikidwa pansipa:

Miy. 5:3, 4; 15:22; 20:11; Aef. 5:19; 2 Tim. 3:16

31. Ndi kofunika kwambiri kuti makolo azitsimikizira kuti ana awo akukhulupirira ndi mtima wonse kufunika kokhala ndi khalidwe labwino ndi moyo woyera. [fy-CN tsa. 67 ndime 8]

32. Upo wakukambirana pakati pa makolo ndi ana awo achinyamata ndi wofunika kwambiri pa kusunga njira zolankhulirana zili zotseguka. [fy-CN tsa. 65 ndime 4]

33. Chinsinsi choimba bwino pa misonkhano yampingo ndi kukhala ndi maganizo abwino mumtima. [w97-CN 2/1 tsa. 27 ndime 3]

34. Kukhala ndi chidziŵitso cha ziphunzitso za Mawu a Mulungu, Baibulo, ndicho chiyeneretso cha moyo wosatha. [w97-CN 8/15 tsa. 6 ndime 5]

35. Kuti tipewe chiyeso cha chisembwere, tiyenera kuzindikira kuti nkulakwa ndi kuti zotsatirapo zake zimakhala zatsoka ndi zowawa. [fy-CN tsa. 93 ndime 9]

S-97-CN Zam, Mal & Moz #297 4/99

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena