Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 10/96 tsamba 2
  • Misonkhano Yautumiki ya October

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Misonkhano Yautumiki ya October
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira October 7
  • Mlungu Woyambira October 14
  • Mlungu Woyambira October 21
  • Mlungu Woyambira October 28
Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
km 10/96 tsamba 2

Misonkhano Yautumiki ya October

Mlungu Woyambira October 7

Nyimbo Na. 47

Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu. Kambaniponi pa lipoti la utumiki wakumunda la July la dziko lino ndi la mpingo wanu.

Mph. 15: Bokosi la Mafunso. Woyang’anira utumiki kapena mkulu wina wokhoza akambitsirana nkhaniyo ndi omvetsera.

Mph. 20: “Dzikonzereni Ulaliki Wanu wa Magazini.” (Ndime 1-7) Funsani mafunso m’ndime 1-4, ndiyeno khalani ndi zitsanzo zachidule ziŵiri kapena zitatu zosonyeza mmene magazini atsopano angagaŵidwire, mwa kugwiritsira ntchito malingaliro omwe ali m’ndime 5-7. Phatikizanipo ndemanga za mu Nsanja ya Olonda ya March 1, 1987, tsamba 24, ndime 8-9.

Nyimbo Na. 222 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira October 14

Nyimbo Na. 39

Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Lipoti la maakaunti.

Mph. 15: “Kufalitsa Uthenga Wabwino wa Chinthu Chabwino Kwambiri.” Mafunso ndi mayankho. Tchulani zina za nkhani zopanga mbiri zimene zaonekera mu Nsanja ya Olonda.—Onani Nsanja ya Olonda ya March 1, 1987, tsamba 20.

Mph. 20: “Dzikonzereni Ulaliki Wanu wa Magazini.” (Ndime 8-11) Mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo ndemanga zonena za malingaliro anayi a mu Nsanja ya Olonda ya January 1, 1994, masamba 24-5, ndime 18-21. Mwa kugwiritsira ntchito makope a mu October a magaziniwo, sonyezani mokonzekerera ulaliki: (1) Sankhani nkhani imene ikuoneka kuti izadzutsa chikondwerero m’gawo lanu, (2) pezani mfundo yokondweretsa imene mudzatchula, (3) pangani funso limene mungagwiritsire ntchito pofuna kusonyeza mfundoyo, (4) sankhani lemba limene mudzaŵerenga mutapatsidwa mpata, ndipo (5) konzani mawu anu oyambira ndi zimene mudzanena pa magaziniwo kuti mulimbikitse mwini nyumba kuwalandira. Khalani ndi ofalitsa okhoza aŵiri kapena atatu amene aliyense wa iwo adzachita chitsanzo cha ulaliki. Phatikizanipo wachichepere amene adzachita chitsanzo chosavuta cha kugaŵira magazini.

Nyimbo Na. 82 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira October 21

Nyimbo Na. 169

Mph. 15: Zilengezo zapamalopo. Fotokozani moyambira njira ya magazini: (1) Lembani zilizonse zimene mwagaŵira ndi nkhani imene munasonyeza, (2) linganizani kudzabweranso ndi makope otsatira, ndipo (3) patulani nthaŵi yakutiyakuti pa ndandanda yanu ya mlungu ndi mlungu ya utumiki kuti mubwerere kumeneko. Gaŵirani masabusikripishoni ndipo kumbukirani kuchitira lipoti ulendo uliwonse pa njira ya magazini monga ulendo wobwereza.

Mph. 15: “Gwirani Ntchito m’Gawo Lanu Mosamala.” Kambitsiranani nkhaniyo ndipo tchulani makonzedwe apamalopo kaamba ka kugwira ntchito m’malo a malonda. Pemphani omvetsera kusimba zokumana nazo zolimbikitsa zimene anakhala nazo pamene anagwirira ntchito m’masitolo amene ali m’gawo lawo.

Mph. 15: Zosoŵa zapamalopo. Kapena nkhani ya mkulu pa mutu wakuti “Sungani Chidaliro Chanu Chili Cholimba Kufikira Mapeto,” wa mu Nsanja ya Olonda ya May 1, 1996, masamba 21-4.

Nyimbo Na. 12 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira October 28

Nyimbo Na. 27

Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Pokhala kuti holide ya kudziko ikuyandikira m’December, imene mwinamwake adzatipatsa nthaŵi yopuma pantchito yolembedwa ndi kusukulu, limbikitsani onse kulingalira za kuthekera kwa kulembetsa monga apainiya othandiza. Limbikitsani onse kupereka malipoti a October a utumiki wakumunda pa kutha kwa mlungu uno.

Mph. 20: “Kusamalira Magazini ndi Mabuku Mumpingo.” Mafunso ndi Mayankho. Ŵerengani ndime zonse.

Mph. 15: Pendani Mabuku Ogaŵira m’November. Buku la Chidziŵitso lidzagaŵiridwa, ndipo tidzayesetsa kubwerera konse kumene tinagaŵira mabuku, ndi cholinga cha kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba. Ofalitsa okhoza aŵiri kapena atatu akambitsirana za phindu la bukulo ndi mmene angaligwiritsire ntchito. Chidziŵitso chimene lili nacho chimakhudza moyo wa anthu amakhalidwe onse. Limafotokoza nkhani ndi mapulinsipulo aakulu a Baibulo amene atsopano afunika kumvetsa asanabatizidwe. Ngati timachititsa phunziro lathu nthaŵi zonse, wophunzira angapite patsogolo mwamsanga. Kambitsiranani ndi kusonyeza moyambira phunziro mwa kugwiritsira ntchito mafikidwe achindunji: Pendani chithunzi ndi mawu ake pamasamba 4-5; fotokozani mmene timachitira phunziro; kambitsiranani mwachidule ndime zisanu zoyamba m’mutu 1; panganani kudzabweranso kudzapitiriza makambitsiranowo, kudzayankha funso lakuti, Kodi moyo wosatha ndi loto chabe? Gogomezerani chimwemwe chimene chimadza ndi mwaŵi wa kuchititsa phunziro la Baibulo lapanyumba.

Nyimbo Na. 162 ndi pemphero lomaliza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena