Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/96 tsamba 2
  • Misonkhano Yautumiki ya April

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Misonkhano Yautumiki ya April
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira April 1
  • Mlungu Woyambira April 8
  • Mlungu Woyambira April 15
  • Mlungu Woyambira April 22
  • Mlungu Woyambira April 29
Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
km 4/96 tsamba 2

Misonkhano Yautumiki ya April

Mlungu Woyambira April 1

Nyimbo Na. 132

Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu. Tchulani malipoti alionse apadera a Chikumbutso chimene munachita ndipo fotokozani makonzedwe apadera a utumiki wakumunda pa holide ya pamapeto a mlungu uno.

Mph. 20: “Khalani ‘Achangu Pantchito Zokoma’ m’April!” Nkhani ya mafunso ndi mayankho pandime 1-10 yokambidwa ndi woyang’anira utumiki. Fotokozani (1) zimene mwalinganiza kwanuko kaamba ka ntchito yowonjezereka ya utumiki wakumunda mu April, (2) mmene mungathandizire onse kutengamo mbali, ndi (3) mmene mungaphatikiziremo atsopano ndi achichepere.

Mph. 15: “Funafunani Aja Ofuna.” Pendani maulaliki osonyezedwa, ndiyeno khalani ndi zitsanzo ziŵiri zosonyeza mmene angagwiritsidwire ntchito. Ngati nthaŵi ilola, fotokozani njira zina zogaŵira magazini, zopezeka mu Utumiki Wathu Waufumu wa September 1995, tsamba 5.

Nyimbo Na. 20 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira April 8

Nyimbo Na. 72

Mph. 15: Zilengezo zapamalopo. Lipoti la maakaunti; tchulani ziyamikiro zochokera ku Sosaite kaamba ka zopereka. Fotokozani njira zogwira ntchito zimene tingathandizire atsopano amene anapezeka pa Chikumbutso kuti apitirize kupita patsogolo. Pendani Nsanja ya Olonda ya April 1, 1991, masamba 9-12.

Mph. 15: “Perekani Utumiki Wopatulika Usana ndi Usiku.” Mafunso ndi mayankho. Ŵerengani ndime 5 ndi 6.

Mph. 15: “Khalani ‘Achangu Pantchito Zokoma’ m’April!” Nkhani ya mafunso ndi mayankho pandime 11-15. Limbikitsani onse kupenda mikhalidwe yawo ndi kufunafuna njira zowonjezera chichirikizo chawo pa utumiki wakumunda.

Nyimbo Na. 113 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira April 15

Nyimbo Na. 133

Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Kumbutsani omvetsera nkhani yapadera pa April 21, yamutu wakuti “Kukhala Opanda Banga Pakati pa Mbadwo Wokhotakhota.” Alimbikitseni kuti alimbikire kwambiri kuthandiza aliyense kudzapezekapo.

Mph. 15: “Nthaŵi Zasintha.” Mafunso ndi mayankho. Gogomezerani kufunika kwa kupereka uthenga wa Ufumu mwa njira imene idzakwaniritsa zosoŵa zazikulu za anthu. Tchulani nkhani za banja, ndi za kakhalidwe ka anthu zimene zili m’maganizo mwa anthu ambiri, monga momwe inatchulira Nsanja ya Olonda ya January 1, 1994, masamba 22-3.

Mph. 20: “Chikhulupiriro Chidza ndi Mbiri.” Fotokozani mmene magazini ogaŵiridwa angagwiritsidwire ntchito kukulitsa chidwi chimene chingatsogolere ku maphunziro a Baibulo m’buku la Knowledge. Khalani ndi zitsanzo ziŵiri kapena zitatu za maulalikiwo.

Nyimbo Na. 204 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira April 22

Nyimbo Na. 6

Mph.15: Zilengezo zapamalopo. Bwerezani mfundo zazikulu za nkhani yapadera imene inakambidwa pamapeto a mlungu wathawu. Fotokozani mmene chilangizo chimenecho chiyenera kusonkhezerera okondwerera kuima zolimba kumbali ya kulambira koona. Ndiponso, kambanipo pakamutu kakuti “Pitirizani Kukula m’Chidziŵitso Cholongosoka,” ndipo gogomezerani kufunika kwa kupezeka pa Phunziro la Buku la Mpingo nthaŵi zonse.

Mph. 12: Bokosi la Mafunso. Nkhani ya mkulu. Fotokozani chifukwa chake abale ochititsa misonkhano ayenera kupeŵa kuzoloŵerana kopambanitsa ndi ena mwakuwatcha ndi maina awo oyamba okha.

Mph. 18: Kukambitsirana kwa mkulu ndi mtumiki wotumikira pankhani yamutu wakuti “Mabanja Opembedza Akale—Chitsanzo cha Tsiku Lathu,” yopezeka pamasamba 20-3 m’kope la Nsanja ya Olonda ya September 15, 1995. Kambitsiranani zinthu zogwira ntchito kuti mabanja apamalopo apindule.

Nyimbo Na. 143 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira April 29

Nyimbo Na. 144

Mph. 12: Zilengezo zapamalopo. Ena amatcha Mboni za Yehova “mpatuko,” akumasokeretsa ena ponena za ntchito yathu ndi zolinga zake. Mukumagwiritsira ntchito buku la Kukambitsirana, tsamba 273, kamutu kachiŵiri, fotokozani mwachidule mmene tingatsutsire chinenezo chimenecho.

Mph.15: Kufola Gawo Lathu Bwino Lomwe. Nkhani ya woyang’anira utumiki. Madera omwazikana kapena akutali angafoledwe kamodzikamodzi. Ena angapeŵere dala kugwira ntchito kumalo kumene anthu ali olemera kapena opembedza kwambiri. Magawo kumene kuli zamalonda anganyalanyazidwe. Nthaŵi zonse ofalitsa ena angamafunsire ndime zimene iwo akonda m’malo mwa zija zofuna kufoledwa. Alimbikitseni onse kugwirizana ndi zoyesayesa zakufola ndime zosafoledwa. Nthaŵi zambiri nyengo yachilimwe imapereka mpata wabwino wokagwira ntchito kumadera akutali; mwinamwake mungalinganize magulu okhala ndi galimoto kapena njinga. Tsimikizirani kuti ndime yafoledwa yonse, kuphatikizapo osapezeka panyumba, musanaibweze. Tchulani njira zina zothandiza kusonyeza mmene onse angathandizire kufola gawo lanu bwino lomwe.

Mph. 18: Gaŵirani sabusikripishoni ya Nsanja ya Olonda m’May. Gwiritsiraninso ntchito makope ake. Khalani ndi cholembedwa cha zogaŵiridwa zonse, ndi cholinga cha kukhazikitsa njira ya magazini. Gogomezerani mapindu ochuluka a kugaŵira magazini monga njira ina yogwira mtima koposa yoperekera uthenga wa Ufumu kwa anthu. Titsimikizire kuti tili ndi mtokoma wake popita mu utumiki; agaŵireni pampata uliwonse. Makonzedwe aumwini a Tsiku la Magazini mlungu ndi mlungu ali njira yabwino yowonjezera zogaŵira. Ntchito ya kusitolo ndi sitolo ndi umboni wa m’khwalala ndi magazini zimabalanso zipatso. Pitani kwa ochita chidwi pamaulendo obwereza olinganizidwa kuyambitsa maphunziro, m’buku la Knowledge. Sonyezani chitsanzo chimodzi kapena ziŵiri zachidule za kugaŵira makope atsopano, mwinamwake mukumagwiritsira ntchito maulaliki opezeka mu Utumiki Wathu Waufumu wa September 1995, tsamba 3, ndime 3-5; ŵerengani ndime 6.

Nyimbo Na. 195 ndi pemphero lomaliza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena