Chilungamo Chenicheni—Liti Ndipo Motani?
ANTHU opanda mlandu sayenera kuopa chiweruzo cholungama. Ndithudi, nzika za kulikonse zingakhale ndi chifukwa chabwino choyamikira ngati dziko lawo lili ndi dongosolo la zamalamulo amene amachirikiza chilungamo. Dongosolo limenelo ndilo mpambo wa malamulo, apolisi amene amaona kuti malamulowo akusungidwa, ndiponso makhoti amene amaweruza. Akristu oona amalemekeza malamulo a m’maiko m’mene amakhala, pomvera uphungu wa Baibulo wakuti ‘mverani maulamuliro aakulu.’—Aroma 13:1-7.
Komabe, a dongosolo la zamalamulo m’maiko osiyanasiyana agamulapo milandu mwa njira yovulaza ndi yochititsa manyazi.a M’malo molanga anthu ochimwa ndi kutetezera anthu opanda mlandu, nthaŵi zina anthu opanda mlandu ndiwo amene alangidwira upandu umene sanachite. Anthu ena akhala m’ndende kwa zaka zambiri, koma nkudzatulutsidwamo zaka zokhala m’ndendemo zisanathe, atakayikiridwa kwambiri zoti anali ndi mlandudi ndi kutinso kumangidwa kwawo kunali mwa lamulo kapena ayi. Chotero, ambiri amafunsa kuti, Kodi kudzakhala chiweruzo cholungama kwa aliyense? Ngati chidzakhalako, ndi liti ndiponso motani? Kodi tingadalire yani kuti atetezere anthu osalakwa? Ndiponso kodi anthu ochitiridwa mosalungama ali ndi chiyembekezo chotani?
Chiweruzo Cholakwika
M’ma 1980, dziko la Germany linakhala ndi “nkhani ya m’khoti yosautsa mtima anthu ochuluka kwambiri pambuyo pa nkhondo.” Panthaŵi imeneyo mayi wina anaponyedwa m’ndende kwa moyo wake wonse chifukwa anapha ana ake aŵiri. Komabe, patapita zaka zingapo, mlandu wakewo unapendedwanso, ndipo anammasula akumayembekezera kuti ayambirenso kumzenga mlandu. Mu 1995, nyuzipepala ya Die Zeit inati chiweruzo choyambacho “mwina chinali cholakwika.” Kufikira nthaŵi imene nkhaniyi inalembedwa, mkaziyo anali atakhala m’ndende kwa zaka zisanu ndi zinayi komabe oweruza akumakayikira ngati analidi ndi mlandu.
Usiku wina mu November 1974, mumzinda wa Birmingham ku England, munaphulika mabomba aŵiri amene anapha anthu 21. Membala wina wa Nyumba Yamalamulo, Chris Mullen analemba kuti, chinali chochitika chimene “aliyense wokhala m’Birmingham sadzaiŵala konse.” Zitatha zimenezo, “amuna asanu ndi mmodzi osalakwa anaimbidwa mlandu wakupha mwankhanza yoopsa m’mbiri yonse ya Britain.” Patapita nthaŵi, milandu yawo inathetsedwa—koma atakhala m’ndende zaka 16!
Loya wina, Ken Crispin, anakambapo za nkhani ina imene “inadzidzimutsa anthu mwa njira yachilendo kwambiri m’mbiri yonse ya nkhani zachiweruzo ku Australia.” Banja lina linali kuchita pikiniki pafupi ndi Ayers Rock, pamene khanda lawo linangosoŵa, osadzaonekanso. Mayi wake anaimbidwa mlandu wakupha, ndipo anaweruzidwa kuti akhale m’ndende moyo wake wonse. Mu 1987, atakhala m’ndendemo zaka zoposa zitatu, khoti litafufuza linapeza kuti umboni womuimba mlandu sunali wokwanira kuti nkuponyedwa m’ndende. Anammasula ndi kumpepesa.
Mtsikana wina wazaka 18 yemwe ankakhala cha kummwera kwa United States anaphedwa mu 1986. Mwamuna wina wachinyamata anagwidwa, nkuweruzidwa kuti aphedwe. Anatha zaka zisanu ndi chimodzi m’ndende ya oyembekezera kuphedwa, zisanadziŵike kuti sanali iye anachita upanduwo.
Kodi zimenezi ndi zitsanzo zosamvekamveka za chiweruzo cholakwika? David Rudovsky, wa pa Yunivesite ya Pennsylvania Law School anati: “Ndakhala ndikuweruza milandu kwa zaka ngati 25 ndipo ndamva milandu yambiri. Ndikuganiza kuti anthu amene anaweruzidwa kuti aponyedwe m’ndende koma amene kwenikweni alibe mlandu . . . angakhale pakati pa 5 peresenti ndi 10 peresenti.” Crispin anafunsa funso lomvetsa chisoni kuti: “Kodi alipobe anthu ena osalakwa omwe ali khale m’ndende mothedwa nzeru?” Kodi kulakwa komvetsa chisoni ngati kumeneko kumachitika bwanji?
Dongosolo la Anthu la Zamalamulo—Lokhala ndi Zophophonya za Umunthu
Mu 1991, British Court of Appeal inati, “pazochita zonse za munthu, palibe chimene chingakhale changwiro.” Kuti malamulo akhale olungama ndi odalirika ndiye kuti anthu opanga malamulowo ayenera kukhalanso odalirika. Anthu samachedwa kulakwa, amakonda chinyengo, ndiponso ali ndi tsankhu. Choncho, nzosadabwitsa kuona kuti malamulo opangidwa ndi munthu nawonso ngolakwika. Talingalirani zotsatirazi.
Malinga ndi Woweruza Rolf Bender wa ku Germany, pa 95 peresenti ya milandu yonse yaupandu, umboni wonse umene mboni zimapereka umakhala ngati umboni woona. Koma kodi mboni za m’khoti zimenezo nzodalirika? Woweruza Bender anakayikira zimenezo. Amaona kuti theka la mboni zimene zimaloŵa m’khoti zimanama. Bernd Schünemann, profesa wa zamalamulo ochita ndi apandu wa pa Yunivesite ya ku Munich, ku Germany, ananenanso zofananazo. Pofunsidwa ndi atola nkhani a nyuzipepala ya Die Zeit, Schünemann anavomereza kuti mawu a mbonizo—ngakhale ngosadalirika—ndiwo umboni wofunika kwambiri. “Ndingatero kuti chifukwa chimene oweruza amaweruzira molakwika nchakuti amadalira mawu osadalirika a mboni.”
Mboni zikhoza kulakwa; apolisi nawonso chimodzimodzi. Makamaka pamene kwachitika upandu umene wakwiyitsa anthu ambiri, apolisi amasonkhezeredwa kungomanga munthu aliyense. Pamikhalidwe yoteroyo, apolisi ena ndi ena amakakamizika kupeka umboni kapena kukakamiza munthu yemwe akumuganizira kuti ndiye ali ndi mlandu kuti avomere. Pamene amuna asanu ndi mmodzi aja anamasulidwa, omwe anaimbidwa mlandu wakuponya mabomba mumzinda wa Birmingham, nyuzipepala ya ku Britain, ya The Independent, inatuluka ndi mutu wakuti: “Asanu ndi Mmodzi Anaimbidwa Mlandu Chifukwa cha Apolisi Onyenga.” Malinga nkunena kwa The Times, “Apolisi ananama, kuchita chiŵembu ndi kunyenga anthu.”
Pankhani zina, tsankhu limapangitsa apolisi ndi anthu onse kukayikira anthu a fuko lina, a chipembedzo china, kapena a mtundu wina. Monga mmene U.S.News & World Report inanenera, kuzenga mlandu waupandu kwangokhala tsopano “nkhani yautundu osatinso nkhani ya maumboni.”
Mlandu ukangoti wafika kukhoti, sikuti umangogamulidwa mwa zimene mboni zimanena iyayi, komanso mwa maumboni asayansi. Pasayansi yopitabe patsogolo yopezera wolakwa, woweruza angapemphedwe kugamula ngati munthu ali ndi mlandu kapena ayi, akumagwiritsira ntchito sayansi yopenda bala lachipolopolo, kapena kuzindikira zidindo za zala, kalembedwe ka munthu, mtundu wa magazi, maonekedwe a tsitsi, ulusi wa nsalu, kapena mtundu wa DNA m’mwazi. Loya wina anati m’makhoti mumangodzaza “asayansi amene amafotokoza zinthu zovuta kwambiri kumvetsetsa zogamulira milandu.”
Ndiponso, magazini ya Nature inatero kuti si asayansi onse amene amagwirizana pamfundo yopezera umboni mwa sayansi. “Asayansi okhaokha angalephere kugwirizana.” Nzachisoni kuti “umboni wopeza mwa sayansi wawononga kale zinthu nkupangitsa oweruza kugamula mlandu molakwika.”
Zilibe kanthu kuti tikukhala kuti, koma dongosolo la anthu la za malamulo likusonyeza kuti anthu amaphophonya. Choncho, kodi tingadalire yani kuti atetezere anthu osalakwa? Kodi tingayembekezere kuti chilungamo chenicheni chingadzakhalepo? Ndipo kodi anthu amene anazengedwa mlandu molakwika ali ndi chiyembekezo chotani?
“Ine Yehova Ndikonda Chilungamo”
Mutakhala inuyo kapena wina wa pabanja lanu yemwe wazengedwa mlandu molakwika, Yehova Mulungu ndi Mwana wake, Yesu, akuona zimene zikukuchitikirani. Chisalungamo choipitsitsa kwambiri chinachitidwa pamene Yesu Kristu anaphedwa pamtengo wozunzirapo. Mtumwi Petro amatiuza kuti Yesu “sanachita tchimo.” Koma anatsutsidwa ndi mboni zonama, nkumuimba mlandu, nkumupha.—1 Petro 2:22; Mateyu 26:3, 4, 59-62.
Tangoganizani kuti Yehova anamva bwanji poona Mwana wake akuchitidwa zimenezo! Chilungamo ndiwo mkhalidwe wina waukulu wa Mulungu. Baibulo limatiuza kuti: “Njira zake zonse ndi chilungamo.”—Deuteronomo 32:4, NW; Salmo 33:5.
Yehova anapatsa Aisrayeli njira yoweruzira yabwino kwambiri. Mlandu wakupha munthu ngati unali wosatsimikizika, anthu ankangopereka nsembe kuti mlandu uthe. Oweruza sanali kungozenga mlandu paupandu uliwonse kuopera kuti angaimbe mlandu munthu wosalakwa. Palibe aliyense amene anali kuzengedwa mlandu wakupha pachifukwa chosamveka bwino kapena paumboni wasayansi; pankafunikira mboni ziŵiri zoona ndi maso. (Deuteronomo 17:6; 21:1-9) Zitsanzo zimenezo zikusonyeza kuti Yehova ali ndi malamulo abwino kopambana ndipo amafuna kuona chilungamo chikuchitidwa. Ndithudi nchifukwa chake iye akuti: “Ine Yehova ndikonda chilungamo.”—Yesaya 61:8, NW.
Nzoona kuti malamulo a Aisrayeli anali m’manja mwa anthu opanda ungwiro ngati ife tomwe. Panali nthaŵi zina pamene nawonso anali kugwiritsira ntchito lamulo molakwa. Mfumu Solomo analemba kuti: “Ukaona anthu alikutsendereza aumphaŵi, ndi kuchotsa chilungamo ndi chiweruzo mwachiwawa pa dera lina la dziko, usazizwepo.”—Mlaliki 5:8.
Yehova anawongola zinthu pamene Mwana wake anaweruzidwa molakwa. Kutsimikizika kwa zimenezo kunamlimbikitsa Yesu, “chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira mtanda [“mtengo wozunzirapo,” NW].” Mofananamo, chiyembekezo cha kukhala ndi moyo padziko lapansi laparadaiso mu ulamuliro wa Mesiyayo, pamene kudzakhaladi chilungamo chenicheni, chimatilimbikitsa kupirira tikamamva zosalungama kapena kuchitiridwa mosalungama m’dongosolo lakaleli. Palibe vuto lina lililonse limene Yehova sangathe kulithetsa nthaŵi yake ikamkwanira. Ngakhale aja amene anaphedwa chifukwa choweruzidwa molakwa angaukitsidwe.—Ahebri 12:2; Machitidwe 24:15.
Ngati nafe tinaweruzidwa molakwa, tizingoyamikira kuti makhoti ambiri alinso ndi mabungwe ena a lamulo amene angatithandize kuwongolera zinthu. Akritsu angagwiritsire ntchito mabungwe amenewo. Komabe, amakumbukira chinthu chimodzi ichi: Madongosolo olakwika a malamulo akusonyeza kuti anthu akufunikira kungoyamba zatsopano. Zimenezo zidzachitika posachedwapa—adzazichita ndi Mulungu.
Posachedwapa Yehova adzangochotseratu dongosolo la zinthu losalungamali ndi kuika dongosolo latsopano m’mene ‘mudzakhalitsa chilungamo.’ Tikudalira kuti Mlengi wathu panthaŵiyo adzakhazikitsa chilungamo kudzera mwa Mfumu yake, Mesiya, Yesu Kristu. Chilungamo chenicheni kwa aliyense chayandikira! Tikuchiyamikiradi kwambiri chiyembekezo chimenechi.—2 Petro 3:13.
[Mawu a M’munsi]
a Pankhani zikutchulidwa panozi, Nsanja ya Olonda siikunena kuti wolakwa ndani kapena wosalakwa ndani, ndipo magaziniyi siikuchirikiza zoti njira yoweruzira ya dziko lina njabwino kuposa lina. Ndiponso, magazini ino siimachirikiza mtundu wina wa chilango kuposa wina. Nkhaniyi ikungofotokoza zimene zinkadziŵikadi pamene tinali kulemba.
[Mawu Otsindika patsamba 27]
Dongosolo lolakwika la malamulo—limodzi ndi boma losaona mtima, chipembedzo chonyenga, ndi malonda aumbombo—zikusonyeza kuti anthu angofunikira dongosolo lina la malamulo
[Bokosi patsamba 28]
Chitonthozo cha m’Malemba
Mu November 1952, Derek Bentley ndi Christopher Craig anaboola nkuloŵa m’nyumba yosungira katundu ku Croydon, pafupi ndi London, England. Bentley anali wazaka 19 ndipo Craig anali wazaka 16. Apolisi anaitanidwa, ndiye Craig anaombera wa polisi wina nkumupha. Craig anakhala m’ndende zaka zisanu ndi zinayi, pomwe Bentley ananyongedwa mu January 1953 chifukwa chakupha munthu.
Mlongo wa Bentley, Iris, analimbikira kwa zaka 40 kuyesayesa kusonyeza kuti Bentley sanaphe munthu. Mu 1993, Mfumu inapepesa zachigamulocho, ikumati Derek Bentley sakanaphedwa. Iris Bentley anadzalemba za nkhaniyo m’buku lakuti Let Him Have Justice. (Mchitireni Chulungamo)
“Chaka chimodzi kuwomberako kusanachitike, Derek anakumana ndi wa Mboni za Yehova mumsewu . . . Mlongo Lane ankakhala pafupi nafe mu Fairview Road ndipo anaitana Derek kudzamvetsera nkhani za m’Baibulo. . . . Ubwino wake unali wakuti Mlongo Lane anali ndi nkhani za m’Baibulo zojambulidwa patepi, ndiye ankambwereka Derek zimenezo [popeza Derek sankadziŵa kuŵerenga bwino]. . . . Ndiye ankati akabwera kunyumba ankandiuza zimene Mlongoyo anali kumuuza, zinthu zonga ngati tonsefe tidzabweranso tikadzafa.”
Iris Bentley anakamchezera mlongo wake m’ndende ya oyembekezera kuphedwa. Anamva bwanji? “Zinthu zimene Mlongo Lane ankamuuza zinamthandiza kwa masiku angapo otsirizirawo.”—Tapendeketsa mawu ndife.
Ngati inunso mwazengedwa mlandu mosalungama, zingakuthandizeni kuŵerenga Baibulo ndi kuganizira za choonadi chake. Zimenezo zingakutonthozeni kwambiri, chifukwa Yehova Mulungu ali “Atate wa zifundo ndi Mulungu wa chitonthozo chonse, wotitonthoza ife m’nsautso yathu yonse.”—2 Akorinto 1:3, 4.
[Chithunzi patsamba 29]
Chisalungamo choipitsitsa chinachitidwa pamene Kristu anaphedwa