Kodi Mukukumbukira?
Kodi mwasangalala ndi kuŵerenga makope aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Chabwino, tiyeni tione ngati mungayankhe mafunso otsatirawa:
◻ Kodi chifuno chachikulu cha maphunziro nchiyani kwa wachinyamata wachikristu?
Chifuno chachikulu cha maphunziro chiyenera kukhala kukonzekeretsa wachinyamata kukhala mtumiki wogwira mtima wa Yehova. Ndipo maphunziro ofunika kwambiri pa onse ndiwo maphunziro auzimu.—8/15, tsamba 21.
◻ Kodi nchifukwa ninji tiyenera kuulula machimo a Mkristu mnzathu kwa akulu?
Chifukwa chimodzi choululira tchimo lalikulu nchakuti kumathandiza kusunga chiyero cha mpingo. Chifukwa china nchakuti kuchita zimenezo ndiko chikondi cha lamulo chachikristu kwa Mulungu, kumpingo, ndiponso kwa wochimwayo.—8/15, masamba 28, 30.
◻ Kodi “kukumbukira tsiku la Yehova nthaŵi zonse” kumatanthauzanji? (2 Petro 3:12, NW)
Zimenezi zimatanthauza kuti sitiyenera kuchotsa “tsiku la Yehova” m’maganizo mwathu. Sitiyenera kuiŵala kuti tsiku limene Yehova adzawononga dongosolo ili la zinthu layandikira. Tiyenera kuliona kuti ndi lenileni, kuliona bwino, ngati kuti libwera maŵa. (Zefaniya 1:7, 14)—9/1, tsamba 19.
◻ Kodi nchifukwa ninji masiku otsiriza a dongosolo ili apitiriza nthaŵi yaitali yomwe ambiri sankayembekezera?
Yehova amalingalira za ubwino wa anthu onse. Amadera nkhaŵa moyo wa anthu. (Ezekieli 33:11) Tiyenera kukhala ndi chidaliro chakuti mapeto adzadza panthaŵi yake kukwaniritsa chifuno cha Mlengi wathu wachikondi ndi wanzeru zonse.—9/1, tsamba 22.
◻ Kodi awo amene ali mu utumiki wa nthaŵi zonse angasungebe motani chimwemwe chawo mosasamala kanthu za mavuto amene angakumane nawo?
Ayenera kuganizira za madalitso ambiri amene ali nawo ndiponso kuzindikira kuti zikwizikwi za ena amavutika ndi mavuto aakulupo. (1 Petro 5:6-9)—9/15, tsamba 24.
◻ Kodi cholinga cha William Tyndale potembenuza Baibulo chinali chiyani?
Cholinga cha Tyndale chinali chakuti alole Malemba kulankhula kwa anthu wamba m’chilankhulo cholongosoka komanso chosavuta kumva.—9/15, tsamba 27.
◻ Kodi tingasonyeze motani kuti ndife ochirikiza okhulupirika a Mawu a Mulungu?
Timasonyeza kuti ndife okhulupirika pa Mawu a Mulungu mwa kuwalalikira kwa ena mwachangu. Monga aphunzitsi, tiyenera kugwiritsira ntchito Baibulo mosamala, osalipotoza kapena kuwonjezera zimene limanena kuti zigwirizane ndi malingaliro athu. (2 Timoteo 2:15)—10/1, tsamba 20.
◻ Kodi mzimu woipa wa dziko ungafooketse motani kukhulupirika kwathu?
Mzimu wa dziko ungafooketse kukhulupirika kwathu mwakutipangitsa kusakhutira ndi zimene tili nazo ndi kutipangitsa kudera nkhaŵa kwambiri zofuna ndi zinthu zathu choyamba m’malo motsogoza za Mulungu. (Yerekezerani ndi Mateyu 16:21-23.)—10/1, tsamba 29.
◻ Kodi kutumikira Yehova ndi mtima wonse kumatanthauzanji?
“Mtima” umatanthauza munthu weniweniyo, ndi luso lake lonse lakuthupi ndi lamaganizo. Kutumikira Yehova ndi mtima wonse kumatanthauza kudzipereka ife eni, kugwiritsira ntchito nzeru zathu ndi mphamvu zathu zonse moyenerera monga momwe tingathere m’kutumikira Mulungu. (Marko 12:29, 30)—10/15, tsamba 13.
◻ Kodi nchiyani chimene chili mfungulo yokhalira munthu wa mapulinsipulo aumulungu?
Mfungulo yake ndiyo kumdziŵadi Yehova, kudziŵa zomwe amakonda, zomwe amadana nazo, ndi zifuno zake. Pamene mapulinsipulo aakulu a Mulungu ameneŵa alamulira miyoyo yathu, kwenikweni, amakhala mapulinsipulo ogwiradi ntchito. (Yeremiya 22:16; Ahebri 4:12)—10/15, tsamba 29.
◻ Kodi atumiki a Yehova ali ndi lingaliro loyenerera liti ponena za ulamuliro wa anthu?
Iwo amasunga uchete pankhani zandale popeza akutumikira monga akazembe kapena nthumwi zoimira Ufumu wa Mulungu. (2 Akorinto 5:20) Komabe, amagonjera aulamuliro malinga ndi chikumbumtima chawo.—11/1, tsamba 17.
◻ Kodi tingaphunzirepo chiyani pa zimene mneneri Elisa anachita?
Ataitanidwa ndi Eliya ku utumiki wapadera, Elisa nthaŵi yomweyo anasiya munda wake napita kukatumikira Eliya, ngakhale kuti ntchito zake zina zinali zapansi. (2 Mafumu 3:11) Ena a atumiki a Mulungu lerolino asonyeza mzimu wofananawo wodzimana mwa kusiya njira zawo zopezera ndalama kuti akalalikire uthenga wabwino kumagawo akutali.—11/1, tsamba 31.
◻ Kodi ndi uphungu wofunika wotani umene ukupezeka m’kalata ya Yakobo?
Kalatayo imatisonyeza mmene tingalimbanirane ndi ziyeso, imatipatsa uphungu wotsutsa tsankhu, ndiponso imatilimbikitsa kuchita ntchito zoongoka. Yakobo akutilimbikitsa kulamulira lilime, kukana chisonkhezero cha dziko, ndi kuchirikiza mtendere. Mawu ake angatithandizenso kukhala oleza mtima ndi olimbikira kupemphera.—11/15, tsamba 24.
◻ Nchifukwa ninji Yehova ali “wokhululukira”? (Salmo 86:5)
Yehova amakhululukira mofunitsitsa chifukwa chakuti saiŵala konse kuti ndife zolengedwa zochokera kufumbi, zokhala ndi zophophonya, kapena zifooko, monga zotsatirapo za kupanda ungwiro. (Salmo 103:12-14)—12/1, masamba 10, 11.
◻ Nchifukwa ninji tiyenera kukhala ofunitsitsa kukhululukira ena?
Ngati tikana kukhululukira ena pamene tili ndi mwaŵi wa kuchitira chifundo, zimenezo zingaipitse kwambiri unansi wathu ndi Mulungu. (Mateyu 6:14, 15)—12/1, tsamba 17.