Mapindu Ochuluka a Utumiki Wopatulika
Yosimbidwa ndi Harry Bloor
Pafupifupi zaka zana limodzi zapitazo, agogo anga aamuna anali wokhulupirira wokangalika wa Tchalitchi cha Methodist. Iwo analinso mlaliki wolemekezeka amene anathandiza kwambiri kuchirikiza matchalitchi ochuluka a ku Stoke-on-Trent, tauni ya ku England yodziŵika bwino chifukwa cha zoumba zadothi. Ndipo kenako analibe ndalama. Pofuna kuthandiza Agogo, atate anga analinganiza kuti agogowo akhale ndi kasitolo m’mudzi. Kasitoloko kanali ndi chilolezo chogulitsa moŵa, ndipo pamene a mpingo wa Methodist anazindikira zimenezi, nthaŵi yomweyo anawachotsa Agogo.
ATATE anakwiya kwambiri ndipo analumbira kuti sadzachitanso chilichonse chokhudzana ndi chipembedzo—ndipo anachitadi zimenezo. Anali wapolisi, koma pambuyo pake anatsegula nyumba yogulitsiramo moŵa. Choncho, ndinaleredwera m’malo amenewo onunkha ndiponso odzaza ndi utsi. Zachipembedzo sizinali kundikhudza pamoyo wanga, koma ndinaphunzira kuseŵera maseŵero ambiri apathabwa mwaluso! Komabe, chifukwa cha chisonkhezero chakale cha Agogo, ndinali kulemekeza Baibulo, ngakhale kuti sindinali kulidziŵa kwenikweni.
Ndinaphunzira Choonadi cha Baibulo
Mu 1923, pamene ndinali ndi zaka 24, ndinasamukira chakummaŵa ku Nottingham ndipo ndinapalana ubwenzi ndi Mary, amene ankakhala pamtunda wa makilomita 40 m’mudzi wa Whetstone, kummwera chakumadzulo kwa Leicester. Atate ake, a Arthur Rest, anakhalapo woimba limba patchalitchi cha kwawoko, koma panthaŵiyi anali Wophunzira Baibulo wokangalika, monga momwe Mboni za Yehova zinali kudziŵikira panthaŵiyo. A Arthur ankakonda kundiuza za chikhulupiriro chawo chatsopanocho—koma sindinazigwiritsire ntchito kwenikweni. Komabe, chidwi changa chinakula pamene ndinatsagana nawo kutchalitchi cha Baptist chakomweko Lamlungu masana, pa July 13, 1924, kukamvetsera nkhani imene inakambidwa ndi wakunyumba yamalamulo amene anali membala wotchuka wa tchalitchi cha Baptist. Mutu wake wakuti, “The Teachings of Pastor Russell Investigated in the Light of Scripture,” [Ziphunzitso za Pasitala Russell Zopendedwa mwa Malemba] unandigwira mtima. Ngakhale lero manotsi amene ndinalemba panthaŵiyo akalipobe.
A Baptist anakana pempho la Ophunzira Baibulo lakuti ayankhe mafunso okhudza zikhulupiriro zawo. Ndinakhumudwa ndi zimenezi ndipo ndinaganiza zopeza malo ena okachitirapo msonkhanowo. Tinagwiritsira ntchito nkhokwe ina imene inali pafupi. Tinasesamo, kuchotsa akangaude, makina opunthira mbewu tinawaika mbali imodzi, ndipo kenaka tonse tinakonzekera. Tinasonkhanitsa mipando 70, ndipo tinasindikiza mapepala olengezera za msonkhanowo.
Pamene Frank Freer anafika kuchokera ku Leicester kudzakamba nkhaniyo, mipando yonse inali itadzaza, ndipo anthu ena okwanira 70 anaimirira! Frank anandigwira mtima ndi kufotokoza kwake Malemba komvekera bwino, mongadi momwe zinalili kwa ambiri amene anapezekapo. Kuyambira nthaŵiyo, mpingo waung’ono wa Ophunzira Baibulo ku Blaby pafupi ndi Leicester unakula mofulumira. Mpamenenso zinthu zinasintha pamoyo wanga—komanso pamoyo wa Mary. Mu 1925 tonse aŵirife tinadzipatulira kwa Yehova, tinabatizidwa, ndipo tinakwatirana.
Madalitso Auzimu
Chaka chotsatira, ndinasankhidwa kukhala woyang’anira utumiki wa Mpingo wa Blaby. Ineyo ndi mkazi wanga tinafuna kutsatira mapazi a apainiya ndi kukhala alaliki a nthaŵi zonse, koma posakhalitsa tinaona kuti chifukwa cha thanzi lake, Mary sakanakwanitsa ntchito yovuta imeneyo. Ngakhale kuti anali wodwaladwala mpaka imfa yake mu 1987, iye anali bwenzi labwino ndiponso mtumiki wodziŵa bwino ntchito yake amene anali ndi luso la kuchita umboni wamwamwaŵi ndi kuyambitsa maphunziro a Baibulo. Usiku uliwonse tinali kupezeka pamisonkhano kapena kugaŵana choonadi cha Baibulo ndi anansi athu.
Ndinali injiniya ndipo ndinagwira ntchito pakampani yopanga makina ochekera matabwa. Ntchito yanga inandipangitsa kuyenda m’madera ambiri m’Britain, ndiponso ku France, ndipo nthaŵi zambiri Mary ankatsagana nane pamaulendo ameneŵa. Maulendo ameneŵa anatipatsa mwaŵi wa kuchitira umboni m’dera lalikulu.
Maziko a Kufutukuka
Mu 1925 tinamanga nyumba yabwino yochitiramo misonkhano yathu ku Blaby, ndipo panthaŵi imeneyi tinakhazikitsa programu yochitira umboni mwachipambano. Lamlungu lililonse m’maŵa, tinali kuchita hayala basi imene inali kukatitula m’midzi yosiyanasiyana ndi m’matauni ang’onoang’ono. Ofalitsa anali kutsika pamalo osiyanasiyana kukalalikira, ndipo anali kukweranso basiyo pobwerera. M’miyezi yotentha ya m’chilimwe, tinali kuchita phunziro la Baibulo limene linkachitika nthaŵi yakumadzulo, pogwiritsira ntchito kope latsopano la Nsanja ya Olonda. Zitatha izi, pa 8 koloko, tinali kusonkhana pamsika wa ku Leicester kaamba ka nkhani yapoyera yokambidwira panja. Usiku wina anthu okwanira 200 anadzamvetsera nkhaniyo. Ntchito imeneyi inayala maziko a kukhazikitsidwa kwa mipingo yambiri imene ikupezeka ku Leicester ndi m’madera ozungulira.
Mu 1926 msonkhano wosaiŵalika unachitika ku Alexandra Palace ya ku London ndiponso ku Royal Albert Hall. Pamsonkhanowo Joseph F. Rutherford, amene anali pulezidenti wa Watch Tower Society panthaŵiyo, anatulutsa buku la Deliverance. Chigamulo chakuti “A Testimony to the Rulers of the World” [Umboni kwa Olamulira a Dziko] ndi nkhani yapoyera yogwira mtima ya Mbale Rutherford yakuti “Why World Powers Are Tottering—The Remedy” [Chifukwa Chake Maulamuliro Amphamvu a Dziko Akugwedezeka—Yankho Lake] zinasindikizidwa mwatsatanetsatane m’nyuzipepala yotchuka tsiku lotsatira nkhanizo zitakambidwa. Anthu oposa 10,000 anamvetsera nkhani yapoyerayo, ndipo makope 50,000,000 a chigamulocho pambuyo pake anafalitsidwa padziko lonse. Msonkhano umenewo unapangitsa kufutukuka kwa ntchito yolalikira ku Britain.
Msonkhano Waukulu m’Nthaŵi ya Nkhondo
Nkhondo yadziko yachiŵiri inaulika mu September 1939, ndipo cha mu 1941 nkhondoyo inafika poipa. Ndege za ajeremani zoponya mabomba zinali kuponya mabomba usana ndi usiku, ndipo kunakhazikitsidwa lamulo lakuti magetsi azime m’dziko lonse. Chakudya chinali chosoŵa, ndipo chakudya chochepa chimene chinalipo chinali kugaŵidwa mosamala. Zoyendera zinali zochepa kwambiri, ngakhale masitima apamtunda. Ngakhale kuti panali zopinga zooneka ngati zovuta kuzithetsazi, tinachitabe msonkhano waukulu wa dziko lonse pa September 3-7, 1941.
Nyumba yotchedwa De Montfort Hall ya ku Leicester inasankhidwa kukhala malo ochitirapo msonkhanowo chifukwa chakuti mzinda wa Leicester uli pamchombo pa dziko la England. Popeza kuti ndinali pantchito ya matabwa, ndinathandiza mwa kupanga zikwangwani zolengezera msonkhanowo. Ndinalinganizanso za mayendedwe a anthu odzasonkhana. Mwa kuguliratu matikiti ndi kulipira ndalama zochuluka kuposa mtengo wake, tinapangitsa kuti matramu a ku Leicester ayende ngakhale Lamlungu.
Popeza kuti mayendedwe anali ovuta, tinali ndi chiyembekezo chakuti mwinamwake kudzasonkhana Mboni zokwanira 3,000. Tangolingalirani za chimwemwe chimene tinali nacho pamene nthumwi zoposa 10,000 zinati zidzafika! Koma kodi adzakhala kuti? Nzika za ku Leicester mokoma mtima zinaitana ambiri a iwo kuti akakhale nawo m’nyumba zawo. Kuwonjezera pamenepo, pafupifupi anthu chikwi chimodzi anali kukhala m’mahema amene anamangidwa pamalo amene anali pamtunda wa makilomita atatu kuchokera pamalo a msonkhanowo. Msasawo tinautcha Camp Gideon [Msasa wa Gideoni] ndipo unadabwitsa anthu oyandikana ndi malowo.
Tinabwereka mahema akuluakulu oyera kuti agwiritsidwe ntchito ndi madipatimenti a msonkhano ndiponso kuti muzikhala ena mwa khamu la anthulo. Pamene tinaona kuti oyendetsa ndege zoponya mabomba za Anazi angaone ndi kuphulitsa mahemawo mosavuta chifukwa cha kuŵala kwa mwezi, tinawapaka utoto wopangitsa kuti asamaoneke. Anthu a m’derali anada nkhaŵa chifukwa cha nkhondoyo, makamakanso chifukwa chakuti Mboni sizinatengemo mbali. Mboni mazanamazana zinali m’ndende panthaŵiyo chifukwa cha uchete wawo wozikidwa pa Baibulo.—Yesaya 2:4; Yohane 17:16.
Nyuzipepala ya The Leicester Mercury, ya pa September 7, 1941, inalengeza kuti: “Ndi chinthu chodabwitsa kwambiri kuona anthu 10,000, ambiri a iwo achinyamata, akutha mlungu wathunthu kukambirana zachipembedzo osatchulako zankhondo, pokhapokha ngati wina anachita kuigwetseramo nkhaniyo.
“Ndinafunsa ngati Mboni zimenezi zinali ndi otsatira ake ku Germany. Inde, anandiuza chotero, ndipo pafupifupi onsewo, ngati 6,000, anali m’misasa yachibalo.”
Mtolankhaniyo anawonjezera kuti: “Ha, inde, Anazi ndi adanidi enieni, koma Mboni sizikuchitapo kalikonse, kusiyapo kugulitsa matrakiti ndi kumvetsera nkhani.”
Ndemanga zapanyuzipepala zonena za ife kwakukulukulu zinali kutinenera zoipa, ndipo otsutsa anafuna ngakhale kuchita chiwawa ncholinga chosokoneza msonkhano wathuwo koma analephera. Komabe, nyuzipepala ya Daily Mail ya ku London inavomereza, komatu mosamasuka kwenikweni kuti: “Panali dongosolo labwino, zinthu zinali zooneka bwino, ndiponso zokonzeka bwino.”
Anatiimba mlandu wakuti tatha ndudu mumzindawo. Koma The Daily Mail inafotokoza kuti: “Leicester kapena Woyang’anira Zafodya sangadandaule kuti Mboni zikutha ndudu za ku Leicester. Iwo sasuta.” Ndiponso, madandaulo akuti Mboni zinatha chakudya cha anthu akumaloko anatsutsidwa pamene anafotokoza kuti Mbonizo zinabwera ndi chakudya chawochawo. Kunena zoona, pamapeto a msonkhanowo, makilogramu 1.8 a mkate anaperekedwa ku Leicester Royal Infirmary—chithandizo chachikulu ndithu m’nyengo imeneyo ya kusoŵa kwa chakudya.
Msonkhano umenewo unapangitsa kupita patsogolo kwauzimu kwa Mboni pafupifupi 11,000 za ku Britain. Iwo anasangalala kwambiri ataona kuti panasonkhana anthu pafupifupi 12,000! Nthumwi mosangalala zinaloŵa m’ntchito yochitira umboni m’misewu ya mu Leicester, ndipo anachezera midzi yakutali ndi nkhani za pagalamafoni.
Nkhani zazikulu za pamsonkhanopo zinali zimene zinajambulidwa mwezi wapita pamsonkhano waukulu wa masiku asanu wa Mboni za Yehova umene unachitikira ku St. Louis, Missouri, U.S.A. Nkhani yojambulidwa ya Mbale Rutherford yakuti “Children of the King” [Ana a Mfumu] inali nkhani yaikulu ya msonkhanowo. Popeza kuti kunali kovuta kuitanitsa makope a buku la Children limene linatulutsidwa ku St. Louis, kope lapadera lachikuto chofeŵa linapangidwa ku Britain pambuyo pake. Makope ake anatumizidwa kwa ana onse amene anadzamvetsera msonkhanowo.
Msonkhano Wapadera Wapachaka wa ku Leicester
Chiŵerengero cha olengeza Ufumu ku Britain chinakwera kwambiri nkhondo itatha! Cha kuchiyambi kwa zaka za m’ma 1980, chiŵerengero cha mipingo ya ku Leicester chinafika khumi. Kenako tinauzidwa kuti Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova linaganiza zoti msonkhano wapachaka wa Watch Tower Bible and Tract Society udzachitikire ku Leicester mu 1983. Monga woyang’anira wa mzinda wa Leicester, mwamsanga ndinayamba kugwira nawo ntchito yokonzekera msonkhanowo, imene inaphatikizapo kubwerekanso nyumba ya De Montfort Hall.
Pamsonkhanowo panafika nthumwi 13 za Bungwe Lolamulira kuchokera kulikulu la Sosaite ku Brooklyn. Nthumwi zokwanira 3,671—zimene panthaŵiyi zinachokera padziko lonse, ndipo ambiri a iwo amene anakhala Mboni kwa nthaŵi yaitali—anadzaza malo a msonkhanowo. Ena owonjezereka okwanira 1,500 anakamvetsera programuyo ku Nyumba Yamsonkhano yoyandikana ndi malowa.
Albert D. Schroeder, amene anali woyang’anira ofesi yanthambi ya Watch Tower Society ku London pamsonkhano wa ku Leicester umene unachitika nthaŵi ya nkhondo, anali woyang’anira msonkhano umenewu wapachaka. Pokumbukira za msonkhano wa mu 1941, Mbale Schroeder anafunsa kuti: “Kodi ndi angati a inu amene muli nafe lero amene analiko panthaŵi ija?” Oposa theka la omvetserawo anakweza manja awo. “Ha! Ndikuyanjananso kotani nanga kwa okhulupirika nonsenu!” iye anatero. Chinalidi chochitika chosaiŵalika.
Tsopano pamsinkhu wa zaka 98, ndikutumikirabe monga mlembi mumpingo wathu ndipo ndikupitirizabe kukamba nkhani zapoyera, ngakhale kuti ndimachita zimenezo chokhala pansi tsopano. Mary atamwalira mu 1987, ndinakwatira Bettina, mkazi wamasiye amene Mary ndi ine tinamdziŵa kwa zaka zambiri. Ndikuthokoza kwambiri chifukwa chakusamaliridwa bwino, zonse ziŵiri mwakuthupi ndiponso mwauzimu. Ngakhale kuti ndalephera kuchita zambiri chifukwa cha kudwaladwala kwa Mary ndipo tsopano chifukwa cha ukalamba wanga, ndaona kuti kukhala ndi zambiri zochita mu utumiki wopatulika kwakhala kondipindulitsa kwambiri.—1 Akorinto 15:58.
[Chithunzi patsamba 26]
Okonzeka kukachita utumiki cha m’ma 1920
[Chithunzi patsamba 26]
Zochitika pamsonkhano waukulu wa ku Leicester