Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 8/15 tsamba 23-25
  • Kudyetsera Onga Nkhosa mu Dziko la Anavajo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kudyetsera Onga Nkhosa mu Dziko la Anavajo
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Kufikitsa Uthenga Wabwino ku Dziko la Anavajo
  • Kumanga “Msasa wa Nkhosa”
  • Ambiri Avomereza Uthenga wa Ufumu
Nsanja ya Olonda—1997
w97 8/15 tsamba 23-25

Kudyetsera Onga Nkhosa mu Dziko la Anavajo

HÓZHÓNÍ, m’chilankhulo cha Aindiya achinavajo, ndiye kuti “chokongola,” ndipo ndi mmene anthu achinavajo amanenera dziko lawo. Kuyambira mu 1868 boma la United States linagaŵira Anavajo mtunda womwe ankangousunga wa makilomita 62,000 mbali zonse zinayi kumpoto chakummaŵa kwa Arizona, pafupi mpamene pamatchedwa kuti four corners, pomwe maboma a Arizona, Colorado, New Mexico, ndi Utah amakumana. Chigwa cha Monument, chomwe chinatchukitsidwa ndi mafilimu Akumadzulo, tsopano chikusungidwa monga Malo Okhala Anavajo ndipo alendo odzaona malo ochokera padziko lonse lapansi amabwera kudzachiona. M’chigwachi muli miyala yofiira yokongola yaukulu wokwana mamita mazana atatu yomwe imaonekera patali monga nsanja m’chipululu cha thyathyathya chimenechi. Mogwirizana ndi mmene malowo alili, dzina la Chinavajo la chigwa chimenechi limatanthauza “mpata wa pakati pa miyala.”

Anthu achinavajo ndi odziŵika ndi khalidwe lawo lodzichepetsa, kulandira alendo mwachikondi, ndi kusamalirana pachibale. Anthu 170,000 okhala kumeneko ambiri, amakhala payekhapayekha, monga mwa mwambo wawo. Ena amaŵetabe nkhosa ndipo amakhalabe m’nyumba zotchedwa kuti hogan. Zopangapanga zaluso za Anavajo zatchuka m’madera ambiri. Makamaka mikeka ndi mabulangeti awo zopangidwa ndi ubweya wa nkhosa za timabokosi ta mitundumitundu kapena mapangidwe ena ozoloŵereka kwawoko, ndizo zamtengo wapatali koposa. Zinanso zodziŵika bwino ndi mikanda ndi makoza za Chinavajo za siliva zopakidwa turquoise ndi zopakapaka zina za komweko.

Kufikitsa Uthenga Wabwino ku Dziko la Anavajo

Kwazaka zoposa 30, Mboni za Yehova zakhala zikufika ku dziko la Anavajo, osati kudzaonako chabe komanso kubweretsa uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu kwa okhala m’dera la kwalokhalokha limeneli. (Mateyu 24:14) Apainiya okhazikika ndi apadera a Mboni za Yehova akutsogolera pantchito yolalikira. Ambiri a iwo anabwera poyankha mapempho a oyang’anira oyendayenda ndi Mboni za komweko kuti akathandize komwe kuli kusoŵa kwakukulu. Ena anachokera m’mipingo yapafupi, koma ena, kuphatikizapo Eni America a mitundu ina, anabwera kuchokera m’madera osiyanasiyana a United States.

Azibambo ndi azimayi odzipereka ameneŵa amayerekeza utumiki wawo kumeneko monga ntchito yaumishonale. Chifukwa ninji? Choyamba, zilankhulo za kumeneko nzovuta kwambiri kuziphunzira chifukwa cha katchulidwe ka mawu kovuta, kalumikizidwe, ndiponso mawu okuluŵika. Ndiyenso, anthu akumeneko, ambiri a iwo, ndi oumirira chikhalidwe chawo pa zachipembedzo, kakhalidwe ka banja, ndiponso kudalira nthaka pa zofunika zawo. Kuwonjezera apo, nyumba ndi ntchito nzosoŵa kwa omwe si Aindiya, zikumapangitsa kukhala kovuta kwa amene asamukirako kuti akhalebe kumeneko. Chomaliza, nthaŵi yaitali imene azungu achitira nkhanza anthuwa inawapangitsa kusakhulupiriranso munthu wachilendo.a

Poyamba, pamene Mboni zinapita kukalalikira ku nyumba ndi nyumba zitavala bwino ndi kumanga matayi, anaziganizira kuti ndi achipembedzo cha Mormon, motero ambiri samatsegula zitseko zawo. Pamene anasintha kuyamba kuvala mwawamba, anayamba kumawaloŵetsa m’nyumba, nthaŵi zina kwa ola lathunthu kapena kuposerapo. Tsopano anthu amazidziŵa Mboni za Yehova, ngakhale kuti zinayambanso kuvala bwino ndi kumanga matayi popita mu utumiki.

Kupita kumene kumakhala anthu achinavajo nkovuta zedi. Umayenera kuyenda ndi galimoto pamsewu wopanda zizindikiro umene nthaŵi zina umakhala wamiyalamiyala, wamchenga, ndi wamatope. Zimenezi zimawononga magalimoto ndiponso kufooketsa okweramo. Galimoto zikhozanso kutitimira, komabe odutsa amakhala okonzeka kuthandiza. Kupita kwa okondwerera, kupita ku phunziro la Baibulo la panyumba, kapena kutenga munthu kupita naye ku msonkhano wachikristu kumalira maola ambiri kupita ndi kubwera. Komabe Mboni mofunitsitsa zimagwira ntchito modzifunira, motero zikumasonyeza chikondi chawo kwa eni dziko.​—Yerekezerani ndi 1 Atesalonika 2:8.

Anavajo amakonda kukambitsirana za m’Baibulo. Kaŵirikaŵiri amasonkhana banja lonse​—ana, makolo, ndi agogo​—kuti adzamvetsere za chiyembekezo chamtsogolo cha mudzi wa anthu, Paradaiso. Atafunsidwa za zomwe amaganiza ponena za mmene paradaiso adzakhalira, mwamuna wina wachinavajo anayankha kuti, “Wa msipu, ndiponso nkhosa zambiri,” zimene zimasonyeza kukonda kwawo nthaka ndi ziŵeto zawo. Amakondanso mabuku ofotokoza za m’Baibulo, ndipo amasonyeza zimenezi nthaŵi zina mwa kupereka mikanda, mtanda wa sopo, mkaka wa m’zitini, ndi zina zotero pothandizira utumiki wa Ufumu. Mpainiya wina wapadera anapeza ma sabusikripishoni a magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! 200 chaka chimodzi, kuphatikizapo aŵiri kwa munthu wokwera kavalo.

Kumanga “Msasa wa Nkhosa”

Nthaŵi ya dzuŵa ikafika, mbusa wachinavajo amatenga nkhosa zake kupita nazo ku msasa wa nkhosa. Malo odyetserako nkhosa ameneŵa nthaŵi ya dzuŵa, omwe amawasankha malinga ndi kufupikirana kwake ndi kumene kuli msipu ndi madzi, amathandiza kuti nkhosa zikhale za thanzi. Kunena mophiphiritsa, Nyumba ya Ufumu ikhoza kuyerekezeredwa ndi msasa umenewu​—malo a msipu wauzimu ndi madzi a choonadi. Anthu amene amabwera akhoza kupezako chakudya chopatsa thanzi ndi mphamvu mwauzimu.

Kwa nthaŵi yaitali, misonkhano inkachitikira m’kalasi pa sukulu ku Kayenta, Arizona. Ndiye mu August 1992, mothandizidwa ndi Mboni mazanamazana zodzipereka zochokera ku maboma osiyanasiyana, Nyumba ya Ufumu yatsopano inamangidwa ku Kayenta. Nyumba ya Ufumu imeneyi ndiponso zina zambiri m’deralo zimasonyeza kwa anthu akumaloko kuti ntchito yolalikira idzapitirizabe osaleka. Nyumba zina za Ufumu m’derali zimaphatikizapo zija za ku Tuba City ndi Chinle, zonsezo m’deralo losungidwira Anavajo, ina ku Keams Canyon ku dera la mtundu wa Ahopi mkatikati mwa chigawocho chosungidwira Anavajo, komanso m’matauni angapo oyandikana ndi derali. Kodi pakhala zotsatira zotani?

Ambiri Avomereza Uthenga wa Ufumu

Ku Kayenta, oposa khumi ndi aŵiri anabatizidwa chimangire Nyumba ya Ufumuyi, kusonyeza madalitso a Yehova pamalo a kulambira koona ameneŵa. Holoyi imapereka umboni wakuti Mboni za Yehova zabwereratu kudzakhala ku dera lino ndiponso kupangitsa chikhulupiriro mu uthenga wabwino waufumu umene zimalalikira. Posachedwa nkhani yapoyera ya Baibulo yoyamba inaperekedwa m’Chilankhulo cha Chinavajo. Anthu 40 ampingowo anakondwera kulandira anthu 245 pa nkhani yonena ma udindo a ukholo. Ndi mitima yachisangalalo, banja lina la anthu asanu ndi atatu linayenda kwa maola atatu popita ndi pobwera kuti lidzamve nkhaniyi​—kubwera kwawo koyamba ku Nyumba ya Ufumu.

Chida china chimene Yehova wapereka ndi brosha la Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha! m’chilankhulo chachinavajo. Kutembenuza brosha limeneli m’chilankhulo chachinavajo, chilankhulo chovuta kwambiri chimenechi, kunali kosautsa ndithu. Otembenuzawo pamodzi anawononga nthaŵi yoposa maola 1000 kuti aonetsetse kuti broshalo likupereka uthenga wa Ufumu moyenera. Kuyambira pamene linatulutsidwa cha kumapeto kwa 1995, Mboni zakumaloko zagaŵira makope zikwizikwi, chomwe chapangitsa kuchita maphunziro a Baibulo ndi anthu ochuluka ofuna choonadi.

Chilankhulo chachinavajo chikugwiritsiridwa ntchito mowonjezereka mu utumiki pamene olengeza Ufumu akuchiphunzira. Mipingo m’deralo yayamba kugwiritsira ntchito Chinavajo mu Sukulu ya Utumiki Wateokratiki, ndiponso ofalitsa Ufumu akuphunzira Chinavajo. Kuwonjezera apo, programu pa misonkhano yaikulu yakumeneko amaitembenuziranso m’Chinavajo. Kuyesayesa konseku kwapangitsa kuti anthu ambiri amve uthenga kumeneko.

Chomwe sitiyenera kunyalanyaza pakati pa zipatso za Ufumu ku malo a Aindiyaku ndi makhalidwe apamwamba kwambiri auzimu amene abale athu achinavajo amasonyeza. Kwa zaka zisanu ndi ziŵiri, Jimmy ndi Sandra ankabwera ndi ana awo asanu kumsonkhano mlungu uliwonse pamtunda wa makilomita 120. Banjalo limakondwera pokumbukira kuimba nyimbo za Ufumu ndiponso kuphunzirira Baibulo pamodzi pamaulendo awo aataliwo. Chikondi ndi khama la makolowo pa choonadi zinapangitsa ana kutsatira chitsanzo chawo kukhala atamandi odzipereka a Yehova. Anayi mwa iwo akutumikira monga apainiya okhazikika tsopano ndipo Jimmy ndi mkulu. Kuwonjezera pa chimwemwe chimenechi cha banjali, mlongo wake wa Jimmy, Elsie posachedwa anakhala munthu woyamba wolankhula Chinavajo chokha kubatizidwa.

Maonekedwe okongola a abusa akumalowa ndi nkhosa zawo amawonjezera kukongola kwa miyala yodziŵikayo imene imakongoletsa malo a Anavajo. Kalekale mneneri Yesaya ananeneratu za Yehova kuti: “Iye adzadyetsa zoŵeta zake ngati mbusa, nadzasonkhanitsa ana a nkhosa pachapa pake, nadzawatengera pachifuwa chake, ndipo adzatsogolera bwinobwino zimene ziyamwitsa.” (Yesaya 40:11) Kupyolera mwa Mbusa wake Wabwino, Yesu Kristu, Yehova akusonkhanitsira onse okhala ku malo a Anavajo ku malo a msipu wauzimu onse olakalaka kumva uthenga wabwino wa Ufumu ndi kukhala nawo pa m’ndandanda wokalandira moyo wosatha.

[Mawu a M’munsi]

a Onani Galamukani! yachingelezi ya May 8, 1948: February 22, 1952; June 22, 1954 yachingelezi; ndi September 8, 1996.

[Chithunzi patsamba 24]

Mbusa wachikazi wachinavajo akumvetsera uthenga wabwino

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena