Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 11/1 tsamba 19-21
  • Ufulu wa Chipembedzo Uchirikizidwa ku Japan

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ufulu wa Chipembedzo Uchirikizidwa ku Japan
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Timitu
  • Kodi Mlandu Wake Unali Wotani?
  • Chigamulo cha Bwalo la Chigawo Chisonkhezera Ouzidwa Ake Kuchitapo Kanthu
  • Maganizo Opanda Dyera a Odandaula
  • Ku Bwalo Lapamwamba
  • Chiyambukiro Chofika Patali
Nsanja ya Olonda—1996
w96 11/1 tsamba 19-21

Ufulu wa Chipembedzo Uchirikizidwa ku Japan

KWA zaka zambiri ku Japan, ophunzira achichepere amene ali Mboni za Yehova ayang’anizana ndi chosankha chovuta: Kodi ayenera kutsatira chikumbumtima chawo chophunzitsidwa Baibulo, kapena kodi ayenera kutsatira mpambo wa makosi a sukulu umene umawombana ndi chikumbumtima chawo? Kodi nchifukwa ninji pali chosankha chovutachi? Chifukwa chakuti kuyeseza maseŵero a nkhondo kuli mbali ya kosi ya maphunziro olimbitsa thupi m’sukulu zawo. Mboni zachicheperezo zinalingalira kuti kuyeseza kumeneko kunali kosagwirizana ndi mapulinsipulo a Baibulo, monga lija lopezeka pa Yesaya chaputala 2, vesi 4. Limeneli timaliŵerenga kuti: “Adzasula malupanga awo akhale zolimira, ndi nthungo zawo zikhale anangwape; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.”

Posafuna kuphunzira maluso onga ankhondo, amene amaloŵetsamo kuvulaza munthu wina, Mboni zachikristu zachicheperezo zinalongosolera aphunzitsi awo kuti sizikufuna kukhala ndi phande m’maseŵero ankhondo chifukwa cha chikumbumtima chawo. Atayesa kukakamiza ophunzira ameneŵa kuti avomere mpambo wa kosi yasukuluyo, aphunzitsi ambiri omvetsetsa potsirizira pake anavomera kulemekeza zikumbumtima za ophunzirawo ndi kuwapatsa mtundu wina wa zochita.

Komabe, aphunzitsi ena anatengeka ndi nkhaniyi, ndipo sukulu zina zinamana Mboni zachichepere mamalikisi a maphunziro olimbitsa thupi. Mu 1993, Mboni zosachepera pa zisanu ndi zinayi zinamanidwa kuloŵa m’makalasi apamwamba ndipo anaziumiriza kusiya sukulu kapena kuzithamangitsa chifukwa cha kusatengamo mbali m’maseŵero ankhondo.

Mwachionekere, imeneyi inali nthaŵi ya kutetezera zoyenera za Akristu achichepere za kulandira maphunziro popanda kugonja pa chikumbumtima chawo. Ophunzira asanu amene anamanidwa kuloŵa m’kalasi lachiŵiri lapamwamba pa Kobe Municipal Industrial Technical College (yotchedwa mwachidule kuti Kobe Tech) anasankha zosuma mlandu.

Kodi Mlandu Wake Unali Wotani?

M’ngululu ya 1990 pamene ophunzira asanuwo analoŵa pa Kobe Tech, anafotokozera aphunzitsiwo kuti sangathe kutenga mbali m’kuyeseza kendo (ukatswiri wachijapani wa kugwiritsira ntchito lupanga) chifukwa cha malingaliro awo ozikidwa pa Baibulo. Bungwe la maphunziro olimbitsa thupi linatsutsa mwamphamvu ndi kuwamana njira ina iliyonse yopezera mamalikisi a maphunziro olimbitsa thupi. Potsirizira pake, ophunzirawo analephera kalasi la maphunziro olimbitsa thupi ndipo motero anafunikira kubwereza kalasi loyamba (kosi ya pakoleji ya chaka choyamba). Mu April 1991 iwo anasuma mlanduwo ku Kobe District Court, akumanena kuti sukuluyo inachita motsutsana ndi ufulu wa chipembedzo woperekedwa ndi konsichushoni.a

A sukuluwo ananena kuti kupereka zochita zina kwa iwo kukakhala kusonyeza kukondera chipembedzo china ndipo motero kukhala chopinga pa kusakhalira mbali kwa maphunziro a onse. Ndiponso, iwo ananena kuti analibe ziŵiya kapena antchito oti apereke programu ya mtundu wina ya maphunziro olimbitsa thupi.

Chigamulo cha Bwalo la Chigawo Chisonkhezera Ouzidwa Ake Kuchitapo Kanthu

Pamene anali kuzenga mlanduwo, aŵiri mwa ophunzira asanuwo analepheranso kupeza mamalikisi a maphunziro olimbitsa thupi, pamene kuli kwakuti atatu enawo anangowakankhira m’kalasi lotsatira. Malamulo a sukulu ananena kuti ophunzira amene mamalikisi awo a sukulu anali otsika ndi amene anabwereza kalasi limodzimodzilo zaka ziŵiri zotsatizana ayenera kuthamangitsidwa. Polingalira zimenezi, mmodzi wa ophunzira aŵiriwo anasankha kusiya sukulu asanathamangitsidwe, koma wina, Kunihito Kobayashi, anakana kusiya. Chotero anathamangitsidwa. Chokondweretsa nchakuti, avareji ya maphunziro onse ya Kunihito kuphatikizapo olimbitsa thupi, amene analephera mwa kungopeza mapointi 48, inali mapointi 90.2 mu 100. Iye ndiye anapambana ophunzira a m’kalasi lake onse 42.

Pa February 22, 1993, Kobe District Court inagamula mlandu mokomera Kobe Tech ndipo inati: “Zochita za sukuluyo sizinaswe konsichushoni,” ngakhale kuti inazindikira kuti “singakane kuti ufulu wa kulambira wa odandaulawo unatsekerezedwa mwa njira ina ndi zimene sukuluyo inafuna kuti akhale ndi phande m’kuyeseza kendo.”

Mofanana ndi mtumwi Paulo m’zaka za zana loyamba, odandaulawo anasankha zochitira apilo ku khoti lapamwamba. (Machitidwe 25:11, 12) Mlanduwo unamka ku Osaka High Court.

Maganizo Opanda Dyera a Odandaula

Katswiri wina wotchuka, Profesa Tetsuo Shimomura wa Tsukuba University, anavomera kupereka umboni monga mboni yaukatswiri mu Osaka High Court. Monga katswiri wazamaphunziro ndi zamalamulo, iye anagogomezera za mmene zochita za sukuluyo zinalili zosalingalira ena pochita ndi ophunzirawo. Kunihito Kobayashi analongosola malingaliro ake m’khotilo, ndipo maganizo ake oona mtima anasonkhezera mtima wa awo amene anali m’khotimo. Ndiponso, pa February 22, 1994, Kobe Bar Association, polengeza kuti zochita za sukuluyo zinapondereza ufulu wa kulambira ndi kuyenera kwa kulandira maphunziro kwa Kunihito, inanena kuti abwezeredwe kusukuluyo.

Pamene nthaŵi inayandikira yakuti chigamulo chiperekedwe mu Osaka High Court, Akristu onse achichepere amene analoŵetsedwamo anali ofunitsitsa kukhala mbali ya nkhondoyo kufikira mapeto. Analingalira kuti anali kumenya nkhondo ya m’khoti kaamba ka Mboni zachichepere zikwi zambiri zimene zinayang’anizana ndi nkhani imodzimodziyo m’masukulu m’Japan monse. Komano popeza kuti anali asanathamangitsidwe pasukulu, zinali zoonekera kwambiri kuti khoti lidzanyalanyaza mlandu wawo. Ndipo, anatha kuona kuti ngati akabweza pempho lawo, nkhanza ya sukulu pothamangitsa Kunihito idzasonyezedwa bwino. Motero, ophunzira onse kusiyapo Kunihito anasankha zoleka mlanduwo.

Pa December 22, 1994, Woweruza Wamkulu Reisuke Shimada wa Osaka High Court anapereka chigamulo chimene chinabweza chigamulo cha Kobe District Court. Khotilo linapeza kuti chifukwa cha Kunihito cha kukanira kuyeseza kendo chinali choona ndi kuti chivulazo chimene analandira pa mchitidwe wake wozikidwa pa chikhulupiriro chake cha chipembedzo chinali chachikulu kwambiri. Sukuluyo, anatero Woweruza Wamkulu Shimada, inayenera kupereka zochita zina. Chigamulo chabwino kwambiri chimenechi chinakhudza bwino mtima wa aja amene ali ndi nkhaŵa yonena za zoyenera za munthu. Komabe, sukuluyo, inachitira apilo mlanduwo ku Bwalo Lapamwamba la Japan, ikumamana Kunihito maphunziro kwa nyengo yoposa chaka china chimodzi.

Ku Bwalo Lapamwamba

Nkhani ina m’nyuzipepala ya Kobe Shimbun pambuyo pake inati: “Kobe City School Board ndi sukuluyo inayenera kuvomera kubwezera a Kobayashi kusukulu panthaŵiyo [chigamulo cha Osaka High Court chitaperekedwa]. . . . Mkhalidwe wawo wa kulimbana wosafunikirawo wamanitsa munthu nyengo yofunika ya uchichepere wake.” Komabe, Kobe Tech inaumitsa khosi pa mlanduwu. Motero, inakhala nkhani yaikulu ya panyuzi m’dziko monsemo. Aphunzitsi ndi akuluakulu ena asukulu m’dziko monsemo anadziŵa zimenezi, ndipo chigamulo cha khoti lapamwamba koposa la m’dzikomo chikakhala monga chitsanzo champhamvu cha chiŵeruzo pa milandu ina yamtsogolo yofanana nawo.

Pa January 17, 1995, patapita pafupifupi mlungu umodzi sukuluyo itachitira apilo mlanduwo ku Bwalo Lapamwamba, chivomezi cha Kobe chinakantha Ashiya City kumene Kunihito ndi banja lake anali kukhala. Pafupifupi nthaŵi ya 5:30 mmaŵa umenewo, mphindi zoŵerengeka chivomezicho chisanakanthe m’deralo, Kunihito, anachoka panyumba pawo kumka ku ntchito yake ya maola ochepa. Iyeyo anali kuyenda pa njinga mu msewu wodutsa pansi pa Hanshin Expressway, ndipo pamene chivomezicho chinachitika, iye anali kungoyandikira kumene mbali imene inagwa. Anabwerera kunyumba nthaŵi yomweyo napeza kuti chipinda choyamba cha nyumba yawo yosanja chinali chitaphwanyikiratu. Kunihito anaona kuti akanataya moyo wake mosavuta m’chivomezicho ndipo anathokoza Yehova chifukwa cha kumlola kupulumuka. Akanafa, kuli kwachionekere kuti mlandu wa kendo ukanatha popanda chigamulo cha Bwalo Lapamwamba.

Bwalo Lapamwamba ku Japan kaŵirikaŵiri limapenda milandu ya apilo pamapepala pokha ndi kugamula kaya ngati khoti laling’ono linali lolondola kapena ayi. Palibe kuzenga mlandu kumene kumachitidwa, kusiyapo ngati pali chifukwa chachikulu chosinthira chigamulo cha khoti laling’onolo. Khotilo silimadziŵitsa eni mlanduwo za tsiku limene chigamulocho chidzaperekedwa. Chotero Kunihito anadzidzimutsidwa mmaŵa wa March 8, 1996, pamene anauzidwa kuti chigamulocho chikaperekedwa mmaŵawo. Mwachimwemwe ndi mokondwera, anamva kuti Bwalo Lapamwambalo linachirikiza chigamulo cha Osaka High Court.

Oweruza anayi, limodzi ndi Woweruza Shinichi Kawai amene anali kutsogolera, anagamula mogwirizana kuti “machitidwewo ayenera kuonedwa monga osayenera konse pa miyezo yovomerezedwa ndi anthu, opatuka pa kulingalira bwino zoyenera, motero, zimenezi nzosaloledwa ndi lamulo.” Khotilo linavomereza kukana koona mtima kwa Kunihito kuyeseza kendo ndipo linati: “Chifukwa chokanira kukhala ndi phande m’kuyeseza kendo cha wochitiridwa apiloyo chinali choona ndipo chogwirizanitsidwa kwambiri ndi maziko a chikhulupiriro chake.” Bwalo Lapamwambalo linagamula kuti sukuluyo ikanayenera ndipo iyenera kupereka njira zina kotero kuti achitire ulemu chikhulupiriro cha wochitiridwa apiloyo.

Chiyambukiro Chofika Patali

Mosakayikira chosankha chimenechi chidzapereka chitsanzo chabwino choyanja ufulu wa kulambira m’sukulu. The Japan Times inati: “Chigamulochi nchoyamba m’Bwalo Lapamwamba pa nkhani ya maphunziro ndi ufulu wa chipembedzo.” Komabe, chigamulo chimenechi, sichikuchotsa thayo la wophunzira wachichepere aliyense la kutenga kaimidwe kololedwa ndi chikumbumtima chake poyang’anizana ndi mayeso a chikhulupiriro.

Profesa Masayuki Uchino wa Tsukuba University anathirira ndemanga kuti chimodzi cha zochititsa zimene zinasonkhezera oweruza kupereka chipambano kwa Kunihito chinali chakuti iyeyo anali “wophunzira woona mtima amene mamalikisi ake a maphunziro anali apamwamba.” Baibulo limapereka uphungu uwu kwa Akristu amene amayang’anizana ndi ziyeso za chikhulupiriro chawo kuti: “Mayendedwe anu mwa amitundu akhale okoma, kuti, mmene akamba za inu ngati ochita zoipa, akalemekeze Mulungu pakuona ntchito zanu zabwino, m’tsiku la kuyang’anira.” (1 Petro 2:12) Akristu achichepere okhulupirika angasonyeze kuti kaimidwe kawo kozikidwa pa Baibulo nkoyenerera kuchitiridwa ulemu ndi anthu mwa kukhala ndi moyo wawo wonse mogwirizana ndi miyezo ya Baibulo.

Chigamulo cha Bwalo Lapamwamba chitaperekedwa, Kunihito Kobayashi anabwezeretsedwa pa Kobe Tech. Ophunzira ochuluka amene analoŵa pa sukulupo ndi Kunihito anali atamaliza kale maphunziro. Kunihito tsopano akuphunzira ndi ophunzira amene ali aang’ono kwa iye ndi zaka zisanu. Kwa anthu ambiri a m’dziko, zingaoneke ngati anataya padera zaka zisanu zofunika kwambiri mu uchichepere wake. Komabe, umphumphu wa Kunihito ngwamtengo wapatali pamaso pa Yehova Mulungu, ndipo kudzimana kwake ndithudi sikuli chabe.

[Mawu a M’munsi]

a Kaamba ka tsatanetsatane wake, chonde onani masamba 10 mpaka 14 a kope la Galamukani wachingelezi la October 8, 1995, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

[Zithunzi patsamba 20]

Kumanzere: Panyumba pawo pa Kunihito chivomezi chitachitika

Pansi: Kunihito lerolino

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena