Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 10/15 tsamba 25-29
  • Mkhalidwe Wochititsa Zinthu Kukula ku Equatorial Guinea

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mkhalidwe Wochititsa Zinthu Kukula ku Equatorial Guinea
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Timitu
  • Kufesa Mbewu m’Masiku Oyambirira
  • “Ozindikira Kusoŵa Kwawo Kwauzimu”
  • Kuchirikiza Kukula mwa Kusonkhana Pamodzi
  • Kuthirira Mbewu Moleza Mtima
  • Kuthandiza Anthu Kuwongolera Moyo Wawo
  • Kukhala Akapolo a Mulungu
Nsanja ya Olonda—1996
w96 10/15 tsamba 25-29

Mkhalidwe Wochititsa Zinthu Kukula ku Equatorial Guinea

ZOMERA zoŵirira ndizo zinthu zoyamba zimene wapaulendo amaona pamene ndege yake itera pa bwalo landege lalikulu la Equatorial Guinea. Msewu wa ndege uli ndi mitengo ikuluikulu m’mbali mwake, imene imachititsa nyumba za pa bwalo landege kuoneka ngati zazifupi. Kuchokera ku gombe la nyanja kufika pamwamba pa mapiri pali zomera zokongola, zochititsidwa kumera kwambiri ndi mvula yochuluka ndi kutentha kwake kwa chaka chonse cha pakati pa ma 80.

Kukulanso kwina kwamphamvu kukuchitika ku Equatorial Guinea, “makulidwe a Mulungu.” (Akolose 2:19) Monga mdindo wa ku Aitiopiya amene anapempha thandizo kwa Filipo, ambiri kuno akufunitsitsa kuzindikira bwino Malemba. (Machitidwe 8:26-39) Si kwachilendo kuona munthu akufikira mmodzi wa Mboni za Yehova m’khwalala ndi kupempha phunziro la Baibulo. Mboni pafupifupi 325 ku Equatorial Guinea zikuchititsa maphunziro a Baibulo oposa chikwi chimodzi.

Kufesa Mbewu m’Masiku Oyambirira

Equatorial Guinea, dziko laling’ono koposa mu Afirika, ali kummwera kwa Nigeria ndi Cameroon. (Onani mapu.) Uthenga wabwino unabwera kuno choyamba ndi Mboni za ku Nigeria zimene zinabwera kudzafuna ntchito m’minda ya cocoa. Ngakhale kuti mipingo ingapo yachingelezi inapangidwa, iyo inatha pambuyo pake pamene abale ameneŵa anabwerera ku Nigeria. Komabe, mwamsanga dzikolo linalandira ufulu mu 1968, amishonale a Watchtower asanu ndi mmodzi okwatirana anatumizidwa kunoku. Chifukwa cha mavuto a zandale, iwo sanathe kukhalitsa, koma umboni wawo unakhala ndi zotulukapo zabwino.

Santiago, mmodzi wa amishonalewo, anakumana ndi Buenaventura, mwamuna wamtali ndi wojincha wodziŵidwa ndi anthu a kumaloko monga chimphona. Anali munthu wokonda chipembedzo amene ankalemekeza Baibulo, komabe anali waukali kwambiri. Chipongwe pang’ono chinali chokwanira kumchititsa kumenya munthu. Atakwiya m’bawa, onse opezekamo ankabalalika, ngakhale kukwera m’mazenera kuti athaŵe nkhonya zake. Kwenikweni, pamene anali kumvetsera kwa Santiago, anali wokonzekera kummenya ngati sakanapereka umboni wotsimikizirika wa m’Malemba wa zimene anali kunena. ‘Palibe amene anganyenge chimphona,’ ankadzitama motero. Anachita chidwi ndi zimene anamva, makamaka ponena za chiyembekezo cha moyo wosatha padziko lapansi la paradaiso, choncho anavomera kumaphunzira Baibulo.

Pamene phunziro linali kupita patsogolo, chikhumbo cha Buenaventura cha kukhala ndi moyo kosatha m’Paradaiso chinali kukula, ndipo anaphunzira kuti anayenera kugwirizanitsa moyo wake ndi miyezo ya Mulungu kuti akapeze mphotho imeneyo. Atazindikira kuti Akristu oona sayenera ‘kubwezera choipa chosinthana ndi choipa,’ iye anayamba kuyesayesa moona mtima kuti alamulire ukali wake.​—Aroma 12:17.

Chiyeso chachikulu chinadza tsiku lina pamene mwangozi anagunda ndi kuswa tambula ya wogula moŵa wina m’bawa. Mwamunayo anakwiya ndi kummenya. Pomwepo, ena m’bawamo anabalalika, akumayembekezera kuti padzabuka ndewu. Koma Buenaventura mofatsa analipirira tambula yoswekayo, nagulira mwamunayo moŵa wina, ndi kupepesa kaamba ka kusasamala kwake. Pamene anansi ake anaona kuti kuphunzira Baibulo kunamsintha motero, ambiri anali ofunitsitsa kuphunzira naye. Podzafika panthaŵi imene Buenaventura anabatizidwa, anali kuchititsa kale maphunziro asanu a Baibulo. Iye watumikira monga mkulu kwa zaka zisanu zapitazo, ndipo ngakhale anthu amamtchabe kuti chimphona, tsopano amachita zimenezo moseka.

“Ozindikira Kusoŵa Kwawo Kwauzimu”

Mkati mwa ma 1970 Mboni zochepa zakumaloko zinapitirizabe kulalikira ndi kusonkhana pamodzi monga momwe zikanathera. Pambuyo pake, amishonale okwatirana angapo achispanya anabwera kudzathandiza. Andrés Botella, yemwe watumikira mu Equatorial Guinea kwa zaka 12, akukumbukira kuti atangofika, anachita chidwi ndi mmene anthu analilidi “ozindikira kusoŵa kwawo kwauzimu.” (Mateyu 5:3, NW) “Kwakhaladi kosangalatsa kwambiri kuphunzira Baibulo ndi anthu oyamikira ameneŵa,” iye akutero.

Mary, mlongo wachispanya, anali kuphunzira Baibulo ndi mtsikana wotchedwa María amene ananena kuti makolo ake, a Francisco ndi a Fausta, nawonso anali kufuna kuphunzira. Popeza Mary anali kuchititsa maphunziro 15 ndipo makolo a María ankakhala kutali, panapita milungu ingapo asanapite kukawachezera.

Pamene Mary ndi mwamuna wake, Serafín, anaonana ndi makolowo pomalizira pake, iwo anali kale ndi buku lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansia ndi Baibulo, ndipo anali ofunitsitsa kuyamba kuphunzira. Choncho anayamba nthaŵi yomweyo. Serafín anaona kuti makolo a María anali kuzidziŵa bwino nkhani zake. Zinalinso chimodzimodzi paulendo wachiŵiri pamene anaphunzira mutu wachiŵiri. “Zinali ngati kuphunzira ndi Mboni ziŵiri zobatizidwa,” akukumbukira motero Serafín. Paulendo wachitatu, popeza kuti anaoneka kuti anazidziŵa bwino nkhanizo, Serafín anafunsa ngati angachite phunziro la mafunso ndi mayankho kuti adziŵe zimene anamvetsetsadi. Iye anapeza kuti a Francisco ndi a Fausta anali ataphunzira buku lonselo paokha!

Kodi chidziŵitso chawo chopezedwa mwatsopano chinawayambukira motani? Mogwirizana ndi zimene anaphunzira, anali ataleka kale kupita kumisonkhano yolambira mizimu ndipo anali ataleka kugwirizana ndi Tchalitchi cha Katolika. Ndiponso, a Francisco anali ataleka kusuta fodya, ndipo sankadyanso nyama yosakhetsedwa bwino. Popeza kuti mwachionekere anali kugwiritsira ntchito zonse zimene anaphunzira, analimbikitsidwa kuyamba kugaŵana chidziŵitso chawo ndi ena. Nthaŵi yomweyo anayamba kulalikira anansi awo. M’miyezi itatu yokha, anayenerera ubatizo. Tsopano a Francisco ndi mtumiki wotumikira, ndipo chifukwa cha chitsanzo chawo chabwino ndi changu pa kulalikira, atatu a ana awo aakazi ndi Mboni tsopano, ana awo aamuna aŵiri amafika pamisonkhano, ndipo achibale ena asanu ndi mmodzi akuphunzira.

Pasanapite nthaŵi yaitali atabatizidwa, a Francisco anakumana ndi Pablo, Mkatolika wodzipereka amene anali kutumikira monga wosunga ziŵiya zopatulika m’tchalitchi chake. Pablo anali kupereka ulaliki nthaŵi iliyonse pamene wansembe panalibe. Ngati membala wa tchalitchi chake anali wodwala, anapitako kukamuona; ngati winawake sanali kuoneka kutchalitchi, Pablo anapita kukamlimbikitsa; ndipo ngati winawake anamwalira, anachita zonse zothekera kutonthoza banjalo. Ndiye chifukwa chake Pablo anali wokondedwa kwambiri ndi onse a m’tchalitchicho.

Popeza Pablo anali kulemekeza kwambiri Baibulo, iye anavomera mofunitsitsa pamene Francisco anampempha kuphunzira naye. Mwamsanga Pablo anaona mmene uthenga wa m’Baibulo unalili wanzeru, ndipo ataphunzira kangapo, anasankha kugwiritsira ntchito ena a malemba amene anaphunzira pa umodzi wa ‘maulendo ake okaŵeta’ kwa membala wodwala wa tchalitchi chake. Mwamsanga pambuyo pake, pa umodzi wa maulaliki ake a pa Sande, Pablo anafotokoza kufunika kwa kugwiritsira ntchito dzina la Mulungu, Yehova, ndi chifukwa chake sitiyenera kugwiritsira ntchito mafano.

Pamene anali kulandira choonadi mosavuta, anayembekezera kuti mamembala ena a tchalitchi chake adzalabadira mofananamo. Koma pambuyo pa maulaliki atatu kapena anayi ozikidwa pa Baibulo ameneŵa, Pablo anaona kuti anthu sanakondwe nacho chidziŵitso chimene anali kupereka. Chotero anasankha kusiya tchalitchicho ndi kugwirizana mokhazikika ndi Mboni za Yehova. M’miyezi yochepa, anayenerera ubatizo, ndipo tsopano ndi mlaliki wachangu wa uthenga wabwino. Ngakhale kuti sali wokhoza kulalikira kwa nthaŵi zonse, panthaŵi ino akuchititsa maphunziro a Baibulo khumi.

Kuchirikiza Kukula mwa Kusonkhana Pamodzi

Mboni za ku Equatorial Guinea zimaona mwamphamvu lamulo la Baibulo la kusaleka kusonkhana pamodzi. (Ahebri 10:25) Chiyambire 1994 pamene ntchitoyo inaloledwanso mwalamulo ndi boma, abale akhala ofunitsitsa kukhala ndi Nyumba za Ufumu zabwino. Kwenikweni, mipingo yambiri yamanga maholo awoawo kapena ikutero kumene.

Ku Mongomo, kumene kaŵirikaŵiri ofika pa misonkhano ya pa Sande amapyola chiŵerengero cha ofalitsa Ufumu nthaŵi ziŵiri ndi theka, mpingo wakhala ukugwiritsa ntchito kuti umange malo aakulu osonkhaniramo. Zipembedzo zina ku Mongomo kaŵirikaŵiri zimalemba ntchito anthu kuti awamangire matchalitchi awo, chotero ntchito ya Mboni za kumaloko inaonekera. Tsiku lina, pasitala wa Iglesia Nueva Apostólica (New Apostolic Church) anaima kuti afunse mmodzi wa akulu ndalama zimene anali kulipira ogwira ntchito zolimba ameneŵa. Pasitalayo ananena kuti ngakhale kuti analemba ntchito amisiri omanga nyumba ndi njerwa ena amene anali mamembala a tchalitchi chake, ntchito inali kuchedwa kwambiri. Anasinkhasinkha za kulemba ntchito amene anali kumanga Nyumba ya Ufumu amenewo. Pamene anauzidwa kuti Mboni zonsezo zinali kugwira ntchito mosalipidwa, anachoka ali wozizwa kwambiri.

Kwa awo amene amakhala kutali ndi Nyumba ya Ufumu, kufika pa misonkhano kungafune kudzimana kwakukulu. Juan, mnyamata amene anabatizidwa mu 1994, anayang’anizana ndi mkhalidwe umenewu. Iye anamva za choonadi ku Gabon, kumene anaphunzira theka loyamba la buku la Kukhala ndi Moyo Kosatha. Ndiyeno anabwerera ku Equatorial Guinea, kumudzi kwawo pafupifupi makilomita 100 kuchokera ku Mongomo. Zimenezi zinali zovuta kwa iye kuti apitirize kuphunzira. Koma sanalefuke. Mwezi uliwonse, ankapanga ulendo wa maola asanu ndi atatu wa ku Mongomo panjinga, kumene Santiago, mmodzi wa akulu akumeneko, anamchititsa phunziro. Ankakhala ku Mongomo masiku angapo ndi kuphunzira katatu kapena kanayi akali kumeneko. Mwa njira imeneyi anakhoza kutsiriza phunziro lake ndi kuyenerera ubatizo.

Kodi ndi motani mmene Juan amakhalira wolimbabe mwauzimu ndi mayanjano ochepa kwambiri ndi Akristu ena? Kwakukulukulu, mwa kukhala mlaliki wachangu wa uthenga wabwino. Iye walalikira anthu onse a m’mudzi mwake, ndipo podzafika nthaŵi imene anabatizidwa, anali kuchititsa maphunziro a Baibulo 13. Asanu ndi mmodzi a ophunzira ake anatsagana naye pa tsiku la msonkhano wapadera ku Mongomo kukaonerera ubatizo wake. Tsopano iye amachititsa Phunziro la Nsanja ya Olonda nthaŵi zonse ndi okondwerera m’dera la kwawo, ndipo kaŵirikaŵiri anthu pafupifupi 20 amapezekapo.

Kuthirira Mbewu Moleza Mtima

Simakulidwe onse auzimu amene amafulumira. Nthaŵi zina pamafunika kuleza mtima kwakukulu kuti muone mbewu ikubala zipatso pomalizira pake. Ndi mmene zinalili ndi Paca, amene anamva uthenga wabwino kwa nthaŵi yoyamba kalelo mu 1984 pamene Edita, mlongo mpainiya, anachitira umboni kwa iye pamsika. Pamene Edita anapita kukachezera Paca kunyumba kwake mlungu wotsatira, Paca anavomera kumaphunzira Baibulo. Ngakhale kuti sanali kupita patsogolo kwambiri, Edita analimbikira chifukwa chakuti anaona mikhalidwe yabwino mwa Paca. “Anaoneka kukhala munthu wonga nkhosa,” akufotokoza motero Edita, “ndipo ndinapemphera kwa Yehova kuti amtsegule mtima.”

Paca anapitiriza phunziro lake modumphadumpha kwa zaka zinayi ndi theka koma mosapitabe patsogolo kwenikweni. Chotero pamene anatsiriza buku la Kukhala ndi Moyo Kosatha, Edita anakambitsirana ndi Paca mosabisa mawu ponena za kufunika kwa kuona choonadi mwamphamvu. Pa kuyesayesa kwake kufika mtima wa Paca, Edita analira.

“Uphungu wochokera mumtima umenewo unandiloŵadi m’maganizo,” akukumbukira motero Paca. “Kuyambira pamenepo ndinayamba kusintha moyo wanga. Ndinalembetsa mu Sukulu Yautumiki Wateokratiki, ndipo m’chaka chimodzimodzicho ndinakhala wofalitsa wosabatizidwa. Tsiku limene ndinabatizidwa linali tsiku lachimwemwe chachikulu koposa m’moyo wanga!” Changu chimene Paca ali nacho tsopano chikusemphana ndi mphwayi yake yakale. Panthaŵi ino akuchititsa maphunziro a Baibulo 13, ndipo alidi woleza mtima ndi awo amene sapita msanga patsogolo.

Kuthandiza Anthu Kuwongolera Moyo Wawo

Mwa kukhala mogwirizana ndi miyezo ya m’Baibulo, Mboni za Yehova ku Equatorial Guinea zakhala ndi mbiri ya kuona mtima ndi kufatsa. Mwamuna wina, amene mwachionekere anachita chidwi ndi khalidwe lawo, anafikira mkulu wina wa mumpingo wa Bata ndi kufunsa kuti: “Kodi muli ndi buku la Kukambitsirana?b Ndatopa kukhala munthu wakudziko. Ndikufuna kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova!”

Antonio, mtumiki wotumikira mumpingo wa Malabo, ndi chitsanzo chabwino kwambiri cha munthu wakudziko amene anakhala Mboni. Asanaphunzire Baibulo, anali ndi moyo wa makhalidwe oipa. Ndalama zochuluka zimene anapeza monga wokonza mawachi anaziwonongera ku moŵa, ndipo analinso wachisembwere. Kodi nchiyani chinamthandiza kusintha moyo wake? Anakhudzidwa mtima kwambiri ndi zimene zanenedwa mwaphamvu pa 1 Akorinto 6:9, 10: “Musasocheretsedwe; adama, . . . kapena oledzera, . . . sadzaloŵa ufumu wa Mulungu.” Anazindikira kuti ngati akufuna kukhala ndi chiyanjo cha Mulungu, ayenera kusintha moyo wake. Chifukwa cha zimenezo anayamba kusankha mayanjano ake. (Miyambo 13:20) Pamene mabwenzi ake akale anafika kudzampempha kukamwa nawo moŵa, anakana pempho lawo ndipo m’malo mwake anawachitira umboni. Posapita nthaŵi analeka kumvutitsa.

Kodi kuyesayesa konseko kunali koyenera? “Ndili wachimwemwe kwambiri kuti ndinasintha moyo wanga,” akufotokoza motero Antonio. “Thanzi langa lili bwino kwambiri ngakhale kuti ndili m’zaka za m’ma 60 tsopano, pamene kuli kwakuti mabwenzi anga akale mwina anamwalira kapena alibe thanzi labwino. Tsopano ndili ndi mabwenzi enieni osati aja ongofuna bwenzi limene lili lofunitsitsa kuwagulira moŵa winanso. Chofunika koposa ndicho chakuti, ndili ndi unansi wabwino ndi Mulungu. Tsopano ndikutumikira monga mpainiya wokhazikika, ndipo ndimachititsa phunziro la Baibulo kwa mwamuna wina amenenso ali ndi vuto la kumwa, choncho ndimagwiritsira ntchito chidziŵitso changa kumthandiza.”

Kukhala Akapolo a Mulungu

Pafupifupi zaka 200 zapitazo, anthu a m’mbali mwa gombe la Equatorial Guinea ankasonkhanitsidwa ndi kutumizidwa ku maiko a ku America monga akapolo. Lerolino, ambiri modzifunira akukhala akapolo​—akapolo a Mulungu. Mtundu umenewu wa ukapolo wawadzetsera ufulu weniweni, ukumawamasula ku ziphunzitso zachibabulo ndi machitachita a kukhulupirira mizimu. Zawaphunzitsanso mmene angakhalire ndi moyo wokhutiritsa ndi wobala zipatso. Aona zimene Yesu analonjeza kuti: “Mudzazindikira choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.”​—Yohane 8:32.

Pokhala ndi 1,937 ofika pa phwando la Chikumbutso mu 1995​—kuŵirikiza chiŵerengero cha ofalitsa a m’dzikomo pafupifupi nthaŵi zisanu ndi imodzi​—pali ziyembekezo zabwino kwambiri za kukula kowonjezereka kwauzimu. Pamene Mboni za ku Equatorial Guinea zipitirizabe mwachangu kufesa ndi kuthirira mbewu ya choonadi, izo zili zotsimikizira kuti ‘Mulungu adzaikulitsa.’ (1 Akorinto 3:6) Mosakayikira konse, ku Equatorial Guinea kuli mkhalidwe wabwino wochititsa kukula kwauzimu!

[Mawu a M’munsi]

a Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

b Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena