Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 10/15 tsamba 3
  • Kodi Kuli Moyo Pambuyo pa Imfa?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Kuli Moyo Pambuyo pa Imfa?
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Funso Limene Lakhalako Nthaŵi Yaitali
  • Muli ndi Chifukwa Chokhalira Odera Nkhawa
    Kodi Moyo Uno Ndiwo Wokha Umene Ulipo?
  • Kufufuza Bwino Zikhulupiriro Zina Zopeka Zokhudza Imfa
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Kodi Muyenera Kuopa Anthu Akufa?
    Galamukani!—2009
  • N’chifukwa Chiyani Timaopa Imfa?
    Galamukani!—2007
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 10/15 tsamba 3

Kodi Kuli Moyo Pambuyo pa Imfa?

MAFUNSO aŵiri asautsa anthu kwa zaka zikwi zambiri: Kodi nchifukwa ninji timakalamba ndi kufa? Kodi kuli mtundu wina wa moyo pambuyo pa imfa?

Loyambalo lathetsa nzeru anthu ambiri chifukwa chakuti ngakhale sayansi yamakono, ndi zinthu zake zonse zochititsa chidwi zimene yatulukira, sinathe kupereka yankho lenileni lokhutiritsa.

Funso lachiŵirilo lakhala ndi mayankho osiyanasiyana ochuluka. Komabe, kaŵirikaŵiri mayankho onena za kuti kaya kuli moyo pambuyo pa imfa ali osiyana pakati pa aja amene amatsimikizira kuti moyowu sindiwo wokha umene ulipo ndi aja amene amaumirira gwagwagwa kuti moyo umathera pa imfa. Ochuluka a gulu lomalizirali amatiuza kuti samakayikira konse kuti munthu ayenera kuyembekezera moyo wanyengo yofinimpha. Kaŵirikaŵiri, ngati mupereka zigomeko zilizonse zotsutsa amayankha mokhutira kuti, “Ehe, palibetu aliyense amene anayamba wabwerako kudzatiuza, sichoncho kodi?”

Monga momwe zilili ndi mafunso ena odzutsa mkangano, pakali ambiri amene alibe chosankha​—akumanenetsa kuti ali okonzekera nthaŵi zonse kulondola njira ina. Komano ena amayankha, mwinamwake mwamphwayi kuti, “Tifunikira kuyembekezera ndi kudzaona pamene nthaŵiyo ifika!”

Funso Limene Lakhalako Nthaŵi Yaitali

Funso loyambirira ponena za moyo wa pambuyo pa imfa linadzutsidwa pafupifupi zaka 3,500 zapitazo ndi Yobu Wakummaŵa wodziŵika bwino, amene ali wotchuka chifukwa cha kupirira kwake mavuto. Umu ndimo mmene Yobu anafunsira funso lake: “Munthu afa ndipo aikidwa pansi; apuma komaliza ndipo kulibe. Monga momwe madzi amazimiririka m’nyanja kapena monga momwe mtsinje umaumira ndi kuphwa, momwemonso munthu agona pansi ndipo saukanso . . . Ngati munthu afa, kodi adzakhalanso ndi moyo?”​—Yobu 14:10-14, New International Version.

Koma Yobu sanali yekha pa kufuna kudziŵa kwake za moyo wa pambuyo pa imfa. Encyclopædia of Religion and Ethics imapereka mawu awa opatsa chidziŵitso pa mutu wakuti “Mkhalidwe wa Akufa” kuti: “Palibe nkhani yokhudza moyo wake wauzimu imene yakopa kwambiri chidwi cha munthu kuposa ija ya mkhalidwe wake pambuyo pa imfa. [Nzika] m’madera onse a dziko lapansi kaŵirikaŵiri zimakhulupiriradi kuti kuli dziko la mizimu​—moyo wake, mikhalidwe yake, malo ake​—ndipo zimenezi zimasonyeza kuti nkhani imeneyi njaikulu kwa iwo. Kuwopa akufa kofala kumasonyeza lingaliro lachikale lakuti mkhalidwe wawo unali wakuti moyo sunathe. Imfa inathetsa mphamvu; zimenezo zinali zoonekera mokwanira; koma kodi panalibe mphamvu zina zimene zinali kugwirabe ntchito, kapena kodi mphamvu zimenezo sizikanakhoza kudzionetsera mwamachenjera ndi mwachinsinsi? Kaya anthu poyamba anakhulupirira mzimu, sou, kapena mzukwa, wolekana ndi thupi, kapena ayi, zichita ngati pali chifukwa chabwino chokhulupirira kuti anaona akufa monga omapitirizabe kukhalako mwamtundu winawake.”

Mungakhale m’limodzi la magulu atatu otchulidwawo: wosatsimikizira chimene chimachitika pambuyo pa imfa; wotsimikizira kuti moyo wamtundu winawake uliko pambuyo pa imfa; kapena wotsimikizira kuti moyo uno ndiwo wokha umene ulipo. Mulimonse mmene zilili, tikukupemphani kuŵerenga mosamalitsa nkhani yotsatirayo. Onani ngati mungapezemo umboni wokhutiritsa wa m’Baibulo wakuti pali chiyembekezo chabwino kwambiri cha moyo wachimwemwe pambuyo pa imfa, mmene udzakhalirapo, kuti, ndipo liti.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena