Singapore Apondereza Ufulu wa Kulambira
MADZULO pa February 24, 1995, nyumba zinayi mu mzinda wa Singapore zinaloŵeredwa ndi apolisi. Anthu okwanira 69 anagwidwa.a Pakati pawo panali mkazi wazaka 71 ndi asungwana aŵiri azaka 15. Chifukwa ninji? Kodi chinali chifukwa cha upandu kapena kuukira boma? Ayi. Palibe aliyense wa iwo amene anachita chilichonse chimene chikanalingaliridwa mpang’ono pomwe kukhala chowopsa, choipa, kapena kusokoneza bata ndi mtendere. Sanaike pangozi makhalidwe, chitetezo, ndiponso ubwino wa anzawo a ku Singapore. Komabe, atagobedeza zinthu m’nyumba zinayizo, apolisiwo anatenga anthu 69 amenewo, amene anasonkhana kudzaphunzira Baibulo ndi kuyanjana, kumka nawo kupolisi. Anasungidwa kumeneko usiku wonse, akumafunsidwa, kutengedwa zidindo za zala, ndi kujambulidwa—inde, kuchitidwa monga apandu odziŵika! Panthaŵiyi—ya maola ngati 18 ali m’malo oipa—anawakaniza kupeza loya ndipo anawakanizanso kuimba foni kuti auze achibale awo kumene anali. Munthu akhoza kuyerekezera mmene mchitidwe wamwamsangamsanga umenewu unakhudzira nzika zokonda mtendere ndi zomvera lamulo zimenezi!
Zochitikazi nzofanana ndi mikhalidwe imene inalipo m’masiku owopsa a Nazi Germany ndi nyengo ya Chikomyunizimu ku Soviet Union ndi ku Eastern Europe. Si zimene mlendo wamba woyenda ku Singapore angayembekezere kupeza m’dziko la mzinda waukhondo ndi wotukuka limenelo. Singapore wapanga mbiri ya kukhala wopambana modabwitsa pachuma ndi chikhalidwe cha anthu mu zaka za zana la 20. Ndi dziko la demokrase limene lili ndi konsichushoni yopatsa nzika zake zoyenera za munthu, kuphatikizapo ufulu wa kulankhula, chipembedzo, ndi misonkhano.
Komabe, awo amene anagwidwa mu February anasankhidwa makamaka chifukwa chakuti anali Mboni za Yehova zosonkhana kudzaphunzira Baibulo ndi kuyanjana Kwachikristu. Mlandu umene anapatsidwa unali wa “kufika pamsonkhano wa anthu osaloledwa.”
Kwenikweni, boma lakana kuzindikira Mboni za Yehova ku Singapore kuyambira 1972 pamene Mpingo wa Singapore unachotsedwa m’kaundula ndipo mabuku, kuphatikizapo ma Baibulo, ofalitsidwa ndi Watch Tower Bible and Tract Society analetsedwa. Panalibe mpata umene unaperekedwa wa kufuna kudziŵa zifukwa za njira imene inatengedwayo. Posachedwapa, kuyenera kwa mchitidwe wa boma wa kusankha umenewu kunakayikiridwa m’mabwalo a milandu a Singapore pa mlandu wa Mboni zinayi zimene zinapatsidwa mlandu mu February 1994 wa kukhala ndi mabuku ofotokoza Baibulo oletsedwa. Mlandu wawo wa apilo unazengedwa mu August 1994 ndipo unathetsedwa msanga. Woweruza Wamkulu Yong Pung How wa Bwalo Lalikulu anafalitsa malingaliro ake mwezi wotsatira. Iye ananenetsa kuti boma silinapondereze ufulu wachipembedzo ndi kuti chiweruzo choperekedwacho chinali bwino chifukwa chakuti Mboni za Yehova zinali kuwononga chitetezo cha boma popeza sizimaloŵa ntchito yausilikali. Pa February 17, 1995, Mboni zinayizo zinapempha kuchita apilo pa chigamulo choipa chimenechi ku Singapore Court of Appeal. Pempho linakanidwa.
Chigamulo chomalizira chimenechi chinafalitsidwa kwambiri m’nyuzipepala ya mu Singapore ya boma. Mosakayika chigamulo chimenechi cha bwalo la milandu ndi kufalitsidwa kwake chinali chizindikiro cha zochitika zimene zinatsatira. Mlungu usanathe Mboni 69 zinagwidwa. Mlandu wa anayi mwa ameneŵa—nzika za Britain, France, ndi Luxembourg—unafafanizidwa pambuyo pake. Komabe, ngakhale kwa anayi ameneŵa, zochitikazo zinali zodetsa nkhaŵa. Mwamuna wina anali atakhala ndi kugwira ntchito ku Singapore kwa zaka zambiri ndi mkazi wake. Anathamangitsidwa pantchito ndi pa nyumba yomwe anali kuchita lendi ndipo anakakamizika kutsazikana ndi mabwenzi awo ambiri apamtima.
Anthu 63 otsalawo anapatsidwa mlandu wa kukhala a gulu loletsedwa, ndipo ena anapatsidwanso mlandu wa kupezeka ndi mabuku oletsedwa. Apatsidwa chilango chachikulu cha zaka zitatu m’ndende kapena faindi ya S$3,000 ($2,100, U.S.) kapena ziŵiri zonsezo. Asungwana aŵiriwo azaka 15 anaweruzidwa m’bwalo lina la ana.
Sizili Zogaŵanitsa Mtundu ndi Umodzi
Kuzungulira dziko lonse, m’maiko oposa 200 mmene zimakhala, Mboni za Yehova zimadziŵika kukhala anthu akhalidwe labwino, oona mtima, omvera lamulo. Zimadziŵika chifukwa cha kukana kwawo zolimba kugwirizana ndi ena m’machitidwe oukira ndi kutsutsa boma—mchitidwe wotsutsana ndi Chikristu umene ungawachititse kuchotsedwa, kapena kulekanitsidwa ndi mpingo. Zoonadi, boma la Singapore siliyenera kuziwopa. Sizili zosokoneza konse chitetezo cha boma la Singapore kapena zogaŵanitsa mtundu ndi umodzi wake. (Aroma 13:1-7) Zimenezi zinafotokozedwa bwino m’kalata ya deti la March 21, 1995, yochokera kwa Milton G. Henschel, pulezidenti wa Watch Tower Bible and Tract Society, yomka kwa Nduna Yaikulu a Goh Chok Tong ku Singapore. Kalatayi yasonyezedwanso pano kuti oŵerenga onse aione.
Anthu okonda ufulu m’zachuma, m’boma, ndi ena adzapenyerera mwachidwi kuti aone mmene mkhalidwewu ku Singapore udzayendera. Kodi boma la Singapore lidzachita zinthu mogwirizana ndi zoyenera za munthu ndi maufulu ochirikizidwa ndi konsichushoni yake ndi maiko ena pa dziko lapansi? Zoonadi, Mboni za Yehova padziko lonse zikudera nkhaŵa olambira anzawo ku Singapore. Akuwakumbukira m’mapemphero awo ndi kukumbukiranso chilimbikitso chopezeka m’Baibulo chakuti: “Yehova akonda chiweruzo, ndipo sataya okondedwa ake.”—Salmo 37:28.
[Mawu a M’munsi]
a M’miyezi yotsatira chiyambire kugwidwa kwa aŵa 69, Mboni zina 11 zagwidwa ndi kupatsidwa mlandu wa kukhala ndi mabuku osaloledwa.
[Bokosi patsamba 30]
March 21, 1995
Goh Chok Tong
Prime Minister
Istana Annexe
Singapore 0923
Republic of Singapore
Lee Kuan Yew
Senior Minister
Prime Minister’s Office
460 Alexandra Road
37-00 PSA Bldg
Singapore 0511
Republic of Singapore
Mabwana Okondedwa:
Nkhani ya Reuters yaposachedwapa yochokera ku Singapore ya deti la February 25, 1995, inali yovutitsa maganizo kwambiri. Nkhaniyo inasimba kuti misonkhano yophunzira Baibulo ya Mboni za Yehova inasokonezedwa ndi apolisi ndipo anthu 69 anagwidwa. Lipoti limeneli lasonkhezera chidwi cha dziko pa mkhalidwe wa Mboni za Yehova ku Singapore, kumene ntchito yawo ndi mabuku zaletsedwa zaka zoposa 20.
Nkovuta kudziŵa bwino chifukwa chimene gulu la chipembedzo limene limagwira ntchito poyera motetezeredwa ndi lamulo m’maiko oposa 200 lingaletsedwere ku Singapore, dziko limene limachirikiza njira za demokrase. Zimenezi nzovutitsanso maganizo kwambiri polingalira kuti konsichushoni ya Singapore imapereka ufulu wa kulambira kwa nzika zake.
Mboni za Yehova sizinasokonezepo chitetezo cha boma kulikonse. Ndithudi, zili ndi mbiri ya kukhala okonda mtendere padziko lonse, ogwira ntchito zolimba, a makhalidwe abwino, ndi omvera lamulo—mikhalidwe imene ndikukhulupirira kuti mumachirikiza m’dziko lanu.
Nzoona kunena kuti chifukwa cha kutsatira kwawo mosamalitsa miyezo ya Akristu ya m’Baibulo, nthaŵi zina mkhalidwe wa Mboni za Yehova waonedwa ndi kutanthauziridwa molakwika. Koma, kodi si mmenenso zinalili kwa woyambitsa Chikristu amene anaonedwa molakwika monga woukira “Kaisara,” boma la m’tsiku lake? Mboni za Yehova zimangotsatira chitsanzo cha Yesu ndi cha Akristu oyambirira. Zimalemekeza boma kumene zimakhala, zimakhoma misonkho yawo, ndi kuchirikiza makhalidwe abwino. Izo ndi nzika za chikumbumtima chabwino ndi zoona mtima. Mboni za Yehova sizinayambe zaukirapo boma m’dziko lililonse ndipo ndikuuzani zoona kuti kupezeka kwawo mu Singapore sikungasokoneze zolinga za dziko lanu.
Malinga ndi malipoti aposachedwa a nkhani, mchitidwe wotsendereza wochitidwa kwa Mboni za Yehova mu Singapore ndi boma lanu tsopano ngwodziŵika ndi anthu onse. Makamaka imeneyi ndi nkhani yochititsa nkhaŵa kwa mabwenzi awo 12 miliyoni padziko lonse. Ndikukupemphani kugwiritsira ntchito ulamuliro wanu kuwongolera mkhalidwewo ndi kulola Mboni za Yehova m’dziko lanu kukhala ndi ufulu wa kulambira ndi wa chikumbumtima zoperekedwa ndi Konsichushoni.
Ndikhulupirira kuti kukambitsirana kosabisa ndi oimira Mboni za Yehova kungathandizire kuthetsa malingaliro olakwa alionse ponena za gulu lathu ndi ntchito yake ndipo kudzakupatsani chidaliro chakuti boma la Singapore siliyenera kuchita mantha ndi Mboni za Yehova. Ndingakonde kulinganiza za kuonana nanu kumeneko.
Ndiyembekezera yankho lanu.
Ndine wanu,
Milton G. Henschel
Pulezidenti
[Mawu a Chithunzi patsamba 31]
Nick Wheeler/H. Armstrong Roberts