Ife Sitidzapuma pa Ntchito Yathu!
“IFE SITIDZAPUMA PA NTCHITO YATHU” ndiwo mzimu umene mumapeza mukachezera nyumba ina yapadera m’Tokyo, Japan. Banja limene limakhala kumeneko ndi la amuna ndi akazi 22, onse okhala ndi avareji ya zaka 70. Ali banja osati chifukwa cha chibale, koma chifukwa cha cholinga chimodzi—utumiki wa umishonale. Iwo alimbikira pantchito yolalikira yanthaŵi yonse kwa zaka 1,026, kuphatikiza pamodzi za onse! Ziŵalo zitatu zachikulire kwambiri za banjalo zinabadwa mu 1910. Zisanu ndi ziŵiri zinayamba utumiki wawo wanthaŵi yonse pamene zinali zachinyamata. Zisanu ndi zinayi zaona kukula kwa ntchito yolalikira Ufumu m’Japan kuyambira pa chiyambi chake pambuyo pa Nkhondo Yadziko II.—Yesaya 60:22.
Komabe, nyumba yosanja zipinda zisanu ndi chimodzi imeneyi imene inali ya nthambi ya Watch Tower ili malo olimbikitsa, makamaka chifukwa cha mzimu, mkhalidwe waukulu, wa amishonale amene akhala pomwepo. Ngakhale kuti ochuluka atha mphamvu zakuthupi chifukwa cha ukalamba ndi kudwaladwala, palibe aliyense wa ankhondo auzimu ameneŵa amene afuna kusiya ntchitoyo. Mboni Zachijapani zawakonzeranso bwino kwambiri nyumbayo, kuikamo Nyumba Yaufumu pansi pake ndi chikepe cha anthu.
Kodi Chimene Chimawachititsa Kukhala Achimwemwe Nchiyani?
Popeza akhala m’ntchito yawo kwa zaka zambiri, amishonale ameneŵa amaona malo ameneŵa kukhala kwawo. “Pamene ndinabwerera ku Australia ku msonkhano wachigawo chilimwe chathachi,” anatero wina wa ziŵalo zachikulire kwambiri za banjalo, “ndinafuna kubwerera kwathu pambuyo pa milungu iŵiri!” Iwo amakonda anthu amene akutumikira ndipo akulitsa chikondi chachikulu pa iwo. Amishonale onse amayamikira makalata ndi kuimbiridwa foni zimene zimawakumbutsa masiku akale.
Zimenezi zili chifukwa cha utumiki wakhama. Posonkhezeredwa ndi chikondi pa Yehova, amishonalewo alalikira Mawu a Mulungu mofulumira m’mikhalidwe yosiyanasiyana. (Yerekezerani ndi 2 Timoteo 4:2.) “Taphunzira kukhala achimwemwe chifukwa chakuti tikutumikira Yehova,” akutero Vera MacKay, amene watumikira m’Japan kwa zaka 37. “Ngakhale ngati palibe amene atiyankha pakhomo, ife timachitirabe umboni za Yehova.”
Okwanira 12 mwa amishonale ameneŵa sanakwatirepo, koma ngachimwemwe kutumikira Ambuye popanda chocheutsa. (1 Akorinto 7:35) Mmodzi wa ameneŵa ndi Gladys Gregory, amene watumikira monga mmishonale kwa zaka 43. Iye akuti: “Kuti ndikhale ndi ufulu wokulirapo mu utumiki wa Yehova, ndinayamba ntchito ya upainiya, pambuyo pake ndinapita ku Gileadi [Sukulu ya Baibulo ya Gileadi ya Watchtower], ndiyeno ndinaloŵa ntchito ya umishonale. Popanda kupanga choŵinda, ndapitiriza kukhala mbeta, ndipo monga mabwenzi anga ochuluka, sindinachitepo chisoni ndi zimenezo.”
Chifuno cha Kusintha
Ngakhale kuti anthu ena amakhala aliuma pamene akukalamba, amishonalewo akhala ofuna kusintha. Lois Dyer, Molly Heron, ndi Lena ndi Margrit Winteler anali kukhala m’nyumba ya amishonale yaing’onopo m’komboni ina ku Tokyo. Anakhala komweko zaka zoposa 20 ndipo anakonda kwambiri anthu akumaloko. M’magawo awo, Awinteler paubale wawo anali ndi anthu 40 panjira zawo za magazini, ndipo Molly ndi Lois anali nawo 74. Ndiyeno, Sosaite inawapempha kusamukira kunyumba ya amishonale yosanja zipinda zisanu ndi chimodzi mkati mwa Tokyo. “Poyamba ndinakwinyirira ndipo sindinakondwe,” akuvomereza Lena. Komabe, monga mwa nthaŵi zonse anasintha malinga ndi gawo lawo latsopano. Kodi amamva bwanji tsopano? “Ndife okondwa kwambiri,” akuyankha Lena. “Tsopano abale aŵiri a pa Beteli amatiphikira ndi kutiyeretsera m’nyumba. Amatisamalira bwino kwambiri.” Onse akuvomerezana ndi Lois yemwe akuti: “Chisamaliro chachikondi cha gulu la Yehova chimatithandiza kulimbikira.”
Nayenso Norrine Thompson anasintha malinga ndi mikhalidwe yatsopano. “Zaka 15,” iye akutero, “ndinali ndi mwaŵi wakutsagana ndi mwamuna wanga [wochokera ku New Zealand] m’ntchito ya chigawo pamene Japan yense anali chabe chigawo chimodzi.” Komabe, mwamuna wake anadwala kwambiri, ndipo iye analaka chiyeso chachikulu koposa m’moyo wake—imfa ya mwamuna wake zaka 18 zapitazo. “Panthaŵiyo,” iye akutero, “chimene chinandikhozetsa kupitiriza ndi ntchito ya umishonale chinali chikondi chimene abale onse m’Japan anasonyeza, limodzi ndi pemphero ndi kukhala wotanganitsidwa mu utumiki.”
Kupirira Matenda
“Ochuluka ali ndi matenda osiyanasiyana, koma ngachimwemwe, ndipo chikhumbo chawo cha kutumikira chili mkhalidwe wapadera,” akutero Albert Pastor, woyang’anira nyumba ya amishonale. Kuti asamalire amishonalewo, dokotala wina ndi mkazi wake, amene ndi nesi, agaŵiridwa kunyumbayo.
Tsiku lina zaka zitatu zapitazo, diso lakumanzere la Elsie Tanigawa, womaliza maphunziro a kalasi la 11 la Sukulu ya Gileadi, linaleka kuona mwadzidzidzi. Miyezi inayi pambuyo pake, diso lake lakumanja nalonso linayambukiridwa. “Nthaŵi zina zimandifooketsa popeza sindikhoza kutumikira monga ndinkachitira. Koma pokhala ndi makonzedwe onse okoma mtima a Sosaite ndi chithandizo chachikondi cha mnzanga ndi ena, ndimapezabe chimwemwe mu utumiki wa Yehova,” akutero Elsie.
Shinichi Tohara ndi mkazi wake, Masako, amene anali m’kalasi limodzi la Gileadi ndi Elsie, ayang’anizana ndi ziyeso zambiri za thanzi lawo zaka zingapo zapitazo. Shinichi, mlankhuli waluso, amavutika kwambiri ndi kusaona kwake manotsi chifukwa cha maso ake amene akuleka kuona. Ngakhale kuti wachitidwa opaleshoni yaikulu ndi yaing’ono m’zaka zaposachedwapa, maso ake amaŵala pamene akulankhula za phunziro la Baibulo la zaka 90 limene akuthandiza tsopano.
Ngakhale kuti ali ndi “munga m’thupi,” amishonale ameneŵa amaona zifooko zawo mofanana ndi mtumwi Paulo, amene anati: “Pamene ndifooka, pamenepo ndili wamphamvu.” (2 Akorinto 12:7-10) Ndipo alidi amphamvu! Amadzuka mmaŵa masiku onse ndi 7 koloko kaamba ka kulambira kwa mmaŵa. Atafisula, amene ali ndi mphamvu amatuluka mmaŵa kupita mu utumiki wakumunda.
Richard ndi Myrtle Shiroma ali pakati pa awo amene amatulukira mu utumiki nthaŵi zonse. Myrtle wachitapo masitroko angapo chifukwa cha arteriosclerosis imene inayamba mu 1978, koma anatsagana ndi mwamuna wake m’ntchito yoyendayenda kufikira November 1987. Tsopano Richard, amene ali ndi zaka 70, amathandiza Myrtle kuchita zonse. Amadzuka ndi 5:00 a.m., kumchotsa pakama, kukamsambitsa, kumuveka zovala, kumpaka zokometsera, ndi kumdyetsa. Ndiyeno amamuika panjinga yake yamagudumu ndi kupita naye mu utumiki wakumunda masiku onse mmaŵa, akumapita kunyumba ndi nyumba kwa ola ngati limodzi ndiyeno kulalikira kwa anthu pa masiteshoni a basi. Myrtle sakhozanso kulankhula, koma mawu ake omaliza anali akuti Dendo, dendo, kutanthauza kuti “Kulalikira, kulalikira” m’Chijapani.
Mwana wawo wamkazi, Sandra Sumida, wasamukira m’nyumba ya amishonale kukawathandiza. Posachedwapa Sandra anafedwa mwamuna wake chifukwa cha nthenda ya mtima. Amayamikira makonzedwe achikondi a Watch Tower Society pomtumizanso ku Japan kuchokera ku Guam, kumene anatumikira monga mmishonale ndi mwamuna wake. “Nthaŵi zonse ndinaona kuti sindinali kuchita zochuluka kuthandiza makolo anga chifukwa ndinali ku Guam,” iye akutero. “Mphwanga, Joanne, anawasamalira m’nyumba yomwe ino. Chotero pamene mwaŵiwo unatseguka, ndinakondwera. Kukhala wofunikira kunoko kwandithandiza chiyambire imfa yadzidzidzi ya mwamuna wanga.”
Akali Antchito Achipambano
Ngakhale kuti amishonalewo amamva ziyambukiro za ukalamba, amakana kutaya mzimu wawo wa umishonale. (Salmo 90:10; Aroma 5:12) Jerry ndi Yoshi Toma, amene anali pakati pa omaliza maphunziro a Gileadi oyamba kubwera ku Japan, amapitabe m’gawo la mabizinesi m’tauni ya Shibuya. “Pamene tinafika panyumba yosanja zipinda ziŵiri yomwe inali pano mu 1949, tinapita kukamsasa ndi kamsasa. Tsopano Tokyo wasintha kukhala likulu. Takalamba tsopano ndipo sitingachite zochuluka monga tinkachitira. Koma titabwerako kokalalikira, timakhala otsitsimulidwa kwambiri,” akutero Yoshi.
Lillian Samson wakhala mmishonale m’Japan kwa zaka 40 ndipo amakonda kwambiri utumiki wake. “Tsopano ndikuthandiza mkazi wina wazaka 80 amene anaphunzira ndi mnzanga, Adeline Nako, amene anabwerera ku Hawaii kukasamalira amake odwala. Posachedwapa mkaziyo anakhala wofalitsa Ufumu atagonjetsa vuto la kulambira makolo akufa. Iye anapita kukachisi nakauza mkazi wa wansembe kuti, ‘Ndatembenuka kukhala Mkristu!’” Pokhala ndi zosangalatsa zotero m’moyo wake, Lillian sanachite chisoni ndi tsiku limene anasiya ntchito yolembedwa pausinkhu wa zaka 19 kuyamba upainiya.
Ruth Ulrich ndi Martha Hess, amene achitira pamodzi umishonale kwa zaka zoposa 45, agwira ntchito kuchokera panyumba ya amishonale imeneyi kwa zaka 35. Amadziŵika kwambiri m’gawolo. Tsiku lina woyang’anira dera anapempha Martha: “Kodi ndingabwereke nkhope yako kupita nayo kunyumba ndi nyumba?” Anthu anadziŵa nkhope ya Martha ndipo anatenga magazini kwa iye, pamene woyang’anira dera anavutika kuyambitsa makambitsirano.
Ruth ali ndi mkazi wina panjira yake ya magazini yemwe sakhoza kuŵerenga chifukwa cha matenda. Chikhalirechobe, mkaziyo amalandirabe magazini ndipotu analandira buku la chikuto cholimba la Mankind’s Search for God. Ruth anakayikira ngati angapitirize kupereka magaziniwo popeza kunaoneka kuti sanali kuŵerengedwa ndi aliyense. Ndiyeno tsiku lina mwamuna wa mkaziyo anafika kwa Ruth ali ndi buku la Search, nati: “Bukuli nlabwino kwabasi! Ndaliŵerenga lonse kaŵiri.” Ruth anayambitsa phunziro la Baibulo kwa iye ndi mkazi wake.
Nyumba ya amishonale yokha imakopa anthu okondwerera. Tsiku lina madzulo, mnyamata wina anafika panyumbapo nati: “Ndimamva kuti ngati ndabwera kuno, ndingathandizidwe kuphunzira Baibulo.” Phunziro la Baibulo linayambitsidwa kwa iye. Monga wophika m’lesitilanti Yachitchaina, anagwira ntchito ndi mkazi wina amene anali wochotsedwa kwa zaka zambiri. Magazini ogaŵiridwa pamene wofalitsa anafika pa lesitilanti anali kupezeka m’khichini. Wophika wachichepereyo anawakonda ndipo anayamba kufunsa mafunso yemwe kale anali Mboni. Pokhala wosakhoza kuyankha, anamuuza kupita ku nyumba ya amishonale. Tsopano akutumikira monga mtumiki wotumikira ndi mpainiya. M’kupita kwa nthaŵi, mkazi wochotsedwayo anabwezeretsedwa, ndipo potsirizira pake nayenso anakhala mpainiya wokhazikika.
Amishonale onse okhala m’nyumbayo amayamikira zimene Yehova wawachitira. Anachokera ku Australia, Canada, Hawaii, Switzerland, ndi United States, ndipo 11 anali a m’kalasi la 11 kapena makalasi oyambirira a sukulu ya amishonale ya Gileadi. Aona kupita patsogolo kwa ntchito ya Ufumu m’Japan ndipo amagwirizana ndi malingaliro a Mfumu Davide, yemwe anati: “Ndinali mwana ndipo ndakalamba: ndipo sindinapenya wolungama wasiyidwa, kapena mbumba zake zilinkupempha chakudya.” (Salmo 37:25) Amishonale ameneŵa ngotsimikiza mtima kusapuma pantchito koma kupitirizabe kutumikira Yehova, kusonyeza chiyamikiro kaamba ka chisamaliro cha Mulungu chachikondi.