Chilango Kodi Chimaphatikizaponji?
M’KUSONYEZA chikondi chake, Yehova amalanga anthu ake. (Miyambo 3:11, 12) Amawapatsa malangizo amene amawongolera malingaliro olakwa ndi amene amaumba maganizo awo ndi njira ya khalidwe. Kwa Aisrayeli m’nthaŵi ya Mose, chilango chinaphatikizapo kudzionera ndi maso zisonyezero za ukulu wa Mulungu. Panali zisonyezero za mphamvu yosayerekezeka pamene Yehova anapereka chiweruzo pa milungu yonse ya Aigupto, kuwonjola anthu ake, ndi kuwononga gulu lankhondo la Aigupto pa Nyanja Yofiira. Panali ziweruzo zochititsa mantha zoperekedwa pa Aisrayeli osamvera. Ndipo panali kugaŵiridwa kwa chakudya ndi madzi kozizwitsa limodzi ndi maphunziro a kufunika kwa kulabadira ndi kugwiritsira ntchito zinthu zonse zimene Yehova amanena. Chilango chonsechi chinagwira ntchito yowachititsa kukhala odzichepetsa ndi kukhomereza pa iwo kufunika kwa kuwopa Yehova koyenera, koti kusonyezedwe ndi chikhulupiriro ndi kumvera.—Deuteronomo 8:3-5; 11:2-7.
Kaŵirikaŵiri chilango cha Yehova chimadza kudzera mwa oimira ake, anthu aundindo oikidwa moyenerera. Mwisrayeli amene anaimba mlandu mkazi wake monama wa kusakhala namwali panthaŵi ya ukwati anafunikira kulangidwa ndi akulu amene anatumikira monga oweruza.—Deuteronomo 22:13-19.
Kufunika kwa Kulanga Ana Athu
Makolo amaimira Yehova pamene alanga ana awo moyenerera. Ndipo ana ayenera kuona chilangocho monga chisonyezero cha chikondi cha makolo, cholinganizidwira kuchirikiza ubwino wawo wosatha. (Miyambo 1:8; 4:1, 13; 6:20-23; 13:1, 24; 15:5; 22:15; 23:13, 14; Aefeso 6:4) Kodi njira yopambana koposa yophunzitsira ndi iti?
Ndiyo inuyo. Chitsanzo chanu. Inu ndinu chitsanzo cha mwana wanu. Amamvetsera kwambiri zimene mumachita kuposa zimene mumanena. Amamva mawu anu, komano amatsanzira machitidwe anu. Mwana wanu ali wotsanzira. Chotero, kodi mukufuna kuti akhale wotani? Wachikondi, wokoma mtima, wooloŵa manja, wochita zinthu mosamala, wanzeru, waluso, wophunzira wa Yesu, wolambira wa Yehova? Chilichonse chimene mungafune kuti akhale, inuyo khalani chimenecho. Chotero, kwa makolo Achikristu, kulanga ana kumaphatikizapo kuwathandiza ndi kuwaphunzitsa kukhala ophunzira enieni a Yesu Kristu.
Chifukwa chake, phunzitsani mwana wanu kuyambira paukhanda, pamene ubongo wake ukukula mofulumira, ukumaloŵetsa chidziŵitso ndi malingaliro m’maganizo ndi mumtima. Koma ngati zaka za kuumbika zofunika zimenezo zapyola kale ndipo mwana wanuyo sanaphunzitsidwe umunthu waumulungu, nchiyani chingachitidwe? Musataye mtima. Kusintha kungachitikebe ndipo kukuchitika kwa mamiliyoni ambiri, achichepere ndi achikulire omwe, mwa mphamvu ya Mulungu. ‘Vulani munthu wakale pamodzi ndi ntchito zake,’ amatero Mawu a Mulungu, ‘ndipo valani watsopano, amene alikukonzeka watsopano, kuti akhale nacho chizindikiritso, monga mwa chifaniziro cha Iye amene anamlenga iye.’—Akolose 3:9, 10.