Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 2/15 tsamba 23-26
  • Dominican Republic—Wotsegukabe pa Kutumbidwa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dominican Republic—Wotsegukabe pa Kutumbidwa
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Timitu
  • Kutumba kwa Mtundu Wina
  • Madalitso a Kuyesayesa Kufikira Anthu
  • Kulabadira Kwabwino kwa Achichepere
  • “Ozonda Malo” Ochokera Kumaiko Ena
Nsanja ya Olonda—1995
w95 2/15 tsamba 23-26

Dominican Republic​—Wotsegukabe pa Kutumbidwa

CHRISTOPHER COLUMBUS, monga mnyamata wamba analoŵa m’moyo woyenda panyanja umene potsirizira pake unamchititsa kutumba zisumbu zimene lerolino zimadziŵika kukhala West Indies. Mu December 1492, ngalawa yake yaikulu, Santa María, inatulukira pagombe la kumpoto kwa chisumbu cha Española, chodziŵika lerolino monga chisumbu cha Hispaniola, chopangidwa ndi Haiti ndi Dominican Republic. Kumeneko Columbus anakhazikitsako malo oyamba okhalako Azungu, linga lomangidwa mofulumira, ndipo analitcha La Navidad. Chisumbu chimenechi chinakhala phata la maulendo ake okazonda malo ena.

Columbus anapeza kuti chisumbucho chinakhalidwa ndi anthu amene mwachionekere anali okongola, odalirika ndi olandira alendo, Aindiya Achitaino. Panali oyerekezeredwa kukhala 100,000 a iwo panthaŵiyo. Komabe, chifukwa cha nkhanza za olanda dziko, amene cholinga chawo chachikulu chinali cha kupeza golidi, chiŵerengero cha nzikazo chinachepa mofulumira. Podzafika 1570 kukunenedwa kuti panali Aindiya Achitaino pafupifupi 500 okha amene anatsala.

Lerolino, Dominican Republic ali ndi anthu a mafuko ambiri ndi maonekedwe, amene makolo awo anasamukira kuno. Ngakhale kuti zili choncho, iwo amaonekera kukhala ali ndi mikhalidwe yambiri yabwino kwambiri ya Ataino, makamaka pokhala anthu aubwenzi ndi osathamangira zinthu. Zimenezi, limodzi ndi kukhulupirira Mulungu koona ndi kulemekeza Baibulo, zachititsa ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa ya Mboni za Yehova kukhala yopambana kwambiri m’dzikoli.

Kutumba kwa Mtundu Wina

Amishonale oyamba a Watch Tower, Lennart ndi Virginia Johnson, anafika mu Dominican Republic mkati mwa nyengo ya Trujillo wotsenderezayo. Mowakondweretsa, anapeza kuti ambiri analabadira uthenga wawo wa Baibulo mwamsanga ndiponso moyanja. Komabe, zimenezi zinali zosakondweretsa akuluakulu aboma ndi alangizi awo achipembedzo. Posapita nthaŵi chizunzo chachikulu chinabuka, ndipo chikhulupiriro cha Mboni Zachidominikani zoyambirira zimenezo chinayesedwa kwakukulu. Kufikira lerolino, kudalirika kwawo ndi chikhulupiriro​—kufikiradi pa imfa​—zimasimbidwa kwambiri.

Mboni za Yehova, zimene tsopano zili 16,000 m’dzikoli, nzodziŵika bwino. Papitapo, masiteshoni a wailesi yakanema asanu anasonyeza vidiyo yakuti Jehovah’s Witnesses​—The Organization Behind the Namea m’dziko monsemu.

Zimenezi zinadziŵikitsa kwambiri ntchito ya Mboni osati m’mizinda yaikulu mokha komanso m’matauni aang’ono ndi kumadera ena a kumidzi. Chotsatirapo chake, iwo analinganiza mkupiti wapadera wofikira anthu ndi kupereka mbiri yabwino ya Ufumu kumadera ameneŵa.

Madalitso a Kuyesayesa Kufikira Anthu

Mboni zambiri zachichepere zanyonga, ndi zachangu zinadzipereka kuthera nyengo za miyezi iŵiri zikumalalikira kumadera akutali ameneŵa. Zoyesayesa zawo zinafupidwa kwambiri. M’dera lina Mboni zina ziŵiri zinapeza chikondwerero chachikulu. Popeza kuti inali nthaŵi ya kuchita Chikumbutso cha imfa ya Yesu, zinapanga makonzedwe ake ndi kuitana anthu. Holo inadzala tho, ndipo anachititsa msonkhanowo. Pamene unatha, anadabwa kwambiri kupeza kuti, panali gulu linanso lalikulu la anthu kunja kwa holoyo ali kuyembekezera kuloŵa. Chotero anawapempha kuti aloŵe ndi kubwerezanso programuyo. Tsopano m’deralo muli mpingo.

Mkhalidwe woolowa manja ndi waubwenzi wa anthuwo kaŵirikaŵiri umawasonkhezera kuuza ziŵalo za banja lawo ndi ena za choonadi cha Baibulo chimene akuphunzira. Wophunzira Baibulo wina anasangalala kwambiri pamene anayenerera kukhala ndi phande mu utumiki wa kunyumba ndi nyumba. Iye anali kuchititsa kale maphunziro a Baibulo asanu m’malo amene amakhala, komano iye anali wachimwemwe kukhala ndi phande lokulirapo mu utumiki.

Pokhala ndi gawo lalikulu limene silimafoledwa mwakaŵirikaŵiri ndi ofalitsa Ufumu, pamakhala kuyesayesa kulalikira anthu oyenda pa basi ndi awo amene amadza kumizinda kudzachita malonda kapena kudzagula zinthu. Zimenezi zadzetsa zotulukapo zosangalatsa, monga momwe kwasonyezedwera ndi chokumana nacho china cha m’kalata imene inalandiridwa ndi ofesi yanthambi. Kalatayo inali yochokera kwa amuna aŵiri okhala kumudzi, amene anapempha phunziro la Baibulo. Pamene Mboni ina inawafikira, inapeza kuti “amuna” amenewo anali a zaka 10 ndi 11. Koma kodi ndimotani mmene iwo anadziŵira za makonzedwe a phunziro la Baibulo? Aha, mwamuna wina wa m’mudzimo anafika kumalikulu kudzachita malonda. Iyeyo anakumana ndi Mboni ina pa khwalala, imene inampatsa trakiti ndi kumpempha kumchititsa phunziro la Baibulo la panyumba laulere. Atabwerera kumudzi kwawo, mwamunayo anapatsa trakitilo msungwana wina wa zaka 12 wakomweko ndi kumuuza za makonzedwe a phunziro la Baibulo. Nayenso msungwanayo anauza nkhaniyo kwa anyamata aŵiri, amene analemba kalata nthaŵi yomweyo. Phunziro la Baibulo linayambidwa kwa anyamatawo, msungwanayo, mwamunayo, ndi ana ake aŵiri.

Kulabadira Kwabwino kwa Achichepere

Ndithudi, achichepere, amene akulira m’choonadi ndi ena omwe, akuonekera kukhala akuona kulambira kwawo Mulungu mwamphamvu. Mwachitsanzo, Tamar ndi mng’ono wake Keila anabatizidwa pausinkhu wa zaka 10 ndipo analoŵa mu utumiki wanthaŵi yonse wa upainiya pausinkhu wa zaka 11. Wendy Carolina anali ndi zaka 12 pamene anasonyeza kudzipatulira kwake mwa ubatizo, ndipo zaka ziŵiri pambuyo pake, mu 1985, anayamba upainiya wokhazikika. Lerolino ndi mphunzitsi wogwira mtima, adakasangalalabe ndi utumiki wanthaŵi yonse. Jovanny wachichepere, wobatizidwa pausinkhu wa zaka 10 ndi amene anakhala mpainiya wokhazikika pausinkhu wa zaka 11, akuchititsa maphunziro a Baibulo apanyumba anayi. Pamene Rey wa zaka khumi anapeza kuti wogulitsa mabuku akale wina anali ndi kabuku kofalitsidwa ndi Mboni za Yehova, Rey anapempha amake kuti amgulire. Anakaŵerenga kuyambira kuchikuto kufikira kuchikuto. Potsirizira pake kufunafuna kwake mabuku ena owonjezereka ofotokoza Baibulo kunamchititsa kufikira ofesi yanthambi. Lerolino akusangalala ndi utumiki wanthaŵi yonse, ndipo mayi wake akutumikiranso Mulungu.

Kodi nchiyani chimene chathandiza achichepere ameneŵa ndi enanso kuzindikira kufunika kwa zinthu zauzimu? M’zochitika zambiri chitsogozo choyenera cha makolo chinachita mbali yaikulu. Zimenezi zinali choncho kwa Josué, amene makolo ake Achikristu ali aphunzitsi a kusukulu. Pamene woyang’anira woyendayenda anapereka lingaliro lakuti makolowo ayese kuthandiza mwina mwake mwana wawo mmodzi yekha kuloŵa mu utumiki wanthaŵi yonse, iwo anapereka chisamaliro pa Josué. Pokhala wophunzira wochita bwino koposa, Josué analipiriridwa ndi boma kuti akaphunzire za uinjiniya. Patapita chaka chimodzi ndi theka ali pa yunivesite, anavomera pempho la kukagwirizana nawo mu ntchito yomanga kumalo a malikulu a Mboni za Yehova ku Dominican Republic. Makolo ake anasonyeza chikhutiro chachikulu chifukwa cha kupereka mwana wawo mu utumiki wa Yehova.

“Ozonda Malo” Ochokera Kumaiko Ena

Mawu a Yesu akuti “Zotuta zichulukadi koma antchito ali oŵerengeka” angagwiritsiridwedi ntchito m’munda wakuno. (Mateyu 9:37) Kufunika kwakukulu ndi kulabadira kwabwino kwasonkhezera Mboni zochokera m’maiko ena kudzakhala ndi phande m’kuzonda gawoli kuti apeze chuma chenicheni chamakono​—ofunafuna choonadi oona mtima.

Pali mabanja a Mboni ochokera ku Puerto Rico woyandikana naye amene anapeza chikhutiro chenicheni pa kutumikira m’madera osiyanasiyana a Dominican Republic. Mutu wina wabanja anati: “Kukhala wokhoza kunena za chikhulupiriro chako ndi chiyembekezo kwa anthu omvetsera kumapangitsadi choonadi kukhala chamoyo!” Atamva za kusoŵa kumene kuli kuno, Cecilia wa ku Sweden ndi Nia wa ku United States anagwirizana ndi achichepere ena angapo amene ali atumiki anthaŵi yonse kudzagwira ntchito kunoko. Iwo akutumikira mkati mwa dzikoli kumene malo ali okwera ndi a mphepo yabwino. Mofananamo, m’mapiri okutidwa ndi mitengo ya pine, mabanja ena aŵiri a ku Canada anagwirizana ndi banja lina Lachidominikani limene linali litabwerera kwawo kuchokera ku United States. Ameneŵa ali ziŵalo za mpingo wina waung’ono ndipo akhoza kufikira anthu amene sanafikiridwepo ndi Mboni za Yehova kwa zaka zofika ku khumi.

Alfredo ndi Lourdes ndi ana awo asanu anabwerera kwawo kuchokera ku New York City ndipo amasonkhana ndi mpingo wina waung’ono mu imodzi ya matauni ena a kugombe okongola a alendo odzaona malo. Iwo akusangalala ndi kukhala okhoza kukhala ndi phande m’kufunafuna anthu oona mtima ndi kuthandiza mpingowo kukula. Roland, wodziŵa kugwiritsira ntchito kompyuta wa ku Austria, ndi mkazi wake, Yuta, asamukira kumbali yakummwera ya dzikoli yotentha ndi yosapita mphepo kwambiri. Anali ndi chisangalalo cha kuona mpingo watsopano ukupangidwa kuyambira pamene anafika. M’tauni ina yoyandikana nayo, kagulu ka alongo atatu ochita upainiya ndi banja lina lochokera ku California anasimba kuti anali ndi mapempho ambirimbiri ofuna maphunziro a Baibulo kwakuti sakanatha kuchititsa onsewo. Chotero analimbikitsa okondwererawo kufika pamisonkhano pa Nyumba Yaufumu yakumaloko ndi kulembetsa maina awo pampambo wa oyembekezera maphunziro a Baibulo. Mlongo wake wamng’ono wa Yuta, Stefan akutumikira mokhulupirika ndi mpingo wina waung’ono m’tauni yokongola ya Samaná, kumpoto koma chakummaŵa. M’zaka ziŵiri zokha, chiŵerengero cha ofalitsa Ufumu kumeneko chaŵirikiza kaŵiri.

Chikondi ndi changu zosonyezedwa ndi ameneŵa ndi enanso amene afika kudzathandiza zikuyamikiridwadi. Avomereza kuyang’anizana ndi zitokoso osati chabe za kukakhalanso m’dziko latsopano lokhala ndi makhalidwe ndi miyambo ina komanso, m’zochitika zambiri, za kuphunzira chinenero chatsopano kuti asamalire zosoŵa zauzimu za anthu onga nkhosa. Zoyesayesa zawo zachititsa anthu akumaloko kulabadira moyanja.

Mabanja ena Achidominikani asiya moyo wopeza bwino wa m’mizinda yaikulu ndipo asamukira m’madera akumidzi. Onsewa akufupidwa mokulira ndi chisangalalo cha kutumba chuma chenicheni cha ofunafuna choonadi oona mtima.

Ofunafuna chuma a m’zaka za zana la 15 anabweretsa ukapolo ndi mavuto osaneneka kwa nzika za Ataino, osati madalitso. Ngakhale Columbus mwiniyo sanapindule ndi chuma cha Dziko Latsopano limeneli. Pomalizira pake anagwidwa ndi kuchotsedwa pachisumbu chimene anatumba nabwezeretsedwa ku Spain muunyolo.

Lerolino mtundu wina wa kuzonda malo ukuchitika, ndipo chuma chamtengo woposerapo chikupezeka. Anthu a Yehova ali otanganitsidwa kufunafuna anthu oona mtima amene amalabadira mbiri yabwino ya Ufumu. Chotulukapo chake nchakuti makamu omakulakulabe akusangalala ndi chimasuko chimene chingaperekedwe ndi Mawu a Mulungu okha. (Yohane 8:32) Iwo akuyembekezera nthaŵiyo pamene dziko limeneli la mapiri, mathithi okongola, magombe okongola, ndi mapanga osangalatsa lidzakhala, osati chabe chisumbu cha paradaiso, koma mbali ya dziko latsopano yokuta dziko lonse lapansi.​—2 Petro 3:13.

[Mawu a M’munsi]

a Yotulutsidwa ndi Watch Tower Bible and Tract Society.

[Mapu patsamba 24]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Dominican Republic

[Zithunzi pamasamba 24, 25]

Achichepere apeza zinthu zauzimu zofunika mwa kulondola utumiki wanthaŵi yonse

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena