Kodi Kupima Matenda Kumeneko Nkoyenera kwa Inu?
Watch Tower Society simapereka chivomerezo kapena chosankha kwa munthu aliyense pa machitachita azamankhwala ndi kupima. Komabe, ngati machitachita akutiakuti ali ndi mbali zina zimene zili zokayikitsa polingalira malamulo amkhalidwe a Baibulo, iwo ayenera kupendedwa bwino. Pamenepo munthu aliyense angathe kuona zimene zikuloŵetsedwamo ndi kusankha chimene angachite.
Abale Okondedwa: Ndikupempha lingaliro lanu. [Wochiritsa winawake] akuonekera kukhala akupambana kwambiri, komano njira imene akugwiritsira ntchito ikundikayikitsa. . . . Iye amadziŵa chimene chalakwika mwa kupima. Ndiyeno kuti adziŵe mtundu wa mankhwala kapena za mlingo wake umene ayenera kugwiritsira ntchito, amaika botolo la mankhwala moyandikana ndi khungu pafupi ndi mwanabere kapena chiŵalo chilichonse. Amayesa kukokera pansi mkono wotukulidwa wa wodwalayo. Mtundu wa mankhwalawo kapena mlingo wake umadziŵidwa ndi mphamvu imene amagwiritsira ntchito kukokera pansi mkonowo. Lingaliro lake nlakuti ma electron, mofanana ndi mphamvu yamagetsi, amatuluka m’mankhwala kudzera pachitsekero chachitsulo cha botolo kuloŵa m’mbali ina yathupi, ndi kuilimbitsa. Kodi kumeneku kuli ngati kulotera madzi?
KALATA imeneyi yochokera ku Oregon, U.S.A., njonena za mchitidwe umene ena amagwiritsira ntchito kudziŵira nkhani za zakudya zomanga thupi, malingaliro, kupenda zikumbukiro, ndi kuthetsa zikayikiro za moyo watsiku ndi tsiku. Komabe, mosasamala kanthu za kufala kwa mchitidwewo, kodi zikayikiro za wolembayo nzoyenera?
Thanzi—Pamtengo Wotani?
Kuyambira mu nthaŵi zakale, anthu ayesayesa kuti adziŵe chifukwa chake amadwala ndi mmene angachirire. Aisrayeli anali ndi mwaŵi chifukwa chakuti anadziŵa kuti anali ochimwa, ndipo anali ndi malamulo ochokera kwa Mulungu amene anawathandiza kusayambukiridwa ndi matenda ambiri kapena kusawawanditsa. (Levitiko 5:2; 11:39, 40; 13:1-4; 15:4-12; Deuteronomo 23:12-14) Chikhalirechobe, anthu a Mulungu anafunafuna thandizo kwa asing’anga odziŵa a m’tsiku lawo.—Yesaya 1:6; 38:21; Marko 2:17; 5:25, 26; Luka 10:34; Akolose 4:14.
Nzosiyana chotani nanga ndi anthu a ku Babulo ndi Igupto wakale! “Madokotala” awo anali ndi mankhwala otengedwa m’zinthu zozoloŵereka, komabe ambiri a “machiritso” awo tsopano angatchedwe kuti achinyengo. Zolembedwa zina Zachiigupto za malembo azojambulidwa zikusimba za sing’anga wina amene anali kuchiritsa khungu ndi msanganizo wa mankhwala wonyansa wa maso a nkhumba, antimony, red ocher, ndi uchi. Msanganizo umenewu unkathiridwa m’khutu la munthu wodwalayo! Umboni wina wakale umasimba kuti machiritso ameneŵa “analidi abwino kwambiri.” Mkhalidwe wake wachilendo kapena wachinsinsi ungakhaledi utakulitsa chikoka chake.
Kaŵirikaŵiri Ababulo ndi Aaigupto anapembedzera mphamvu zamatsenga.a Wansembe yemwe analinso sing’anga ankafunsa wodwala kupumira mu mphuno za nkhosa, akumakhulupirira kuti mphamvu inayake, kapena nyonga inayake, ikatuluka mwa wodwalayo ndi kuloŵa m’cholengedwa chinacho ndi kupereka mphamvu inayake. Nkhosayo inkaphedwa, ndipo chiwindi chake chinkalingaliridwa kuti chidzasonyeza nthenda ya wodwalayo kapena zamtsogolo mwake.—Yesaya 47:1, 9-13; Ezekieli 21:21.
Ndithudi, sing’anga wowopa Mulungu mu Israyeli wakale sakanagwiritsira ntchito michitidwe yolambira mizimu. Mulungu analamula mwanzeru kuti: “Asapezeke mwa inu munthu . . . wosamalira mitambo, kapena wosamalira kulira kwa mbalame, kapena wanyanga. . . . Popeza aliyense wakuchita izi Yehova anyansidwa naye.” (Deuteronomo 18:10-12; Levitiko 19:26; 20:27) Ndimo mmene zililinso kwa atumiki Achikristu a Mulungu lerolino. Kusamala nkoyenerera.
M’zaka zaposachedwapa anthu ambiri atembenukira ku “njira zina” zopimira ndi machiritso. Kwakukulukulu mbali imeneyi ndiyo chosankha cha munthu mwini. (Mateyu 7:1; yerekezerani ndi Aroma 14:3, 4.) Zoonadi, kukakhala kochititsa chisoni ngati Mkristu aliyense afikira kukhala wodziloŵetsa kwambiri m’nkhani zoutsa mkangano za machiritso kwakuti zimenezi zikuphimba utumiki, umene uli njira yokha yopulumutsiradi miyoyo. (1 Timoteo 4:16) Baibulo silimanena kuti m’dziko latsopano matenda adzachiritsidwa ndipo thanzi langwiro likumapezedwa kupyolera m’zamankhwala, m’mankhwala azitsamba, zakudya, kapena njira zochiritsa malingaliro ndi thupi. Kwenikweni, kuchiritsa kokwanira kudzadzetsedwa kokha mwanjira ya chikhululukiro cha machimo pamaziko a nsembe ya dipo ya Yesu.—Yesaya 33:24; Chivumbulutso 22:1, 2.
Kodi ndi Mphamvu Zotani Zimene Zimaloŵetsedwamo?
Kodi nchiyani chimene Mkristu angafune kulingalira popanga chosankha chake ponena za mchitidwe wa kupima mnyewa kotchulidwa m’kalata yotsegulira nkhaniyi?
Njira zina zopimira nyonga kapena mchitidwe wa minyewa zili mbali ya machiritso abwino a masiku onse, ndipo ndi oŵerengeka amene akakayikira za kuyenera kwake. Mwachitsanzo, nthenda ya poliyo ingafooketse minyewa, ndipo njira yake yochiritsa ingaphatikizepo imene imatchedwa kuti kinesiology—“kupima minyewa ndi kayendedwe ka minyewa.” Kinesiology yotero imagwiritsidwanso ntchito m’njira yochiritsira odwala sitiroko. Anthu ochuluka angamvetsetse kuyenera kwa kuchiritsa kotero.
Koma bwanji za kupima minyewako kofotokozedwa m’kalata ya m’chiyambi cha nkhaniyi? Mtundu umenewu wa “kinesiology” wagwiritsiridwa ntchito poyesayesa kudziŵa kaya ngati zakudya zakutizakuti, mankhwala azitsamba, kapena mavitameni akutiakuti angathandize kapena kuvulaza munthuyo. Monga momwe zimachitidwira, munthuyo amanyamula mkono wake, ndipo wochiritsayo amaukanikizira pansi kuti aone mphamvu ya minyewa. Kenako wodwalayo amaika chakudya kapena kanthu kena m’kamwa mwake, pamimba pake, kapena m’dzanja mwake. Ndiyeno minyewa ya mkonowo imayesedwanso. Kukunenedwa kuti ngati afunikira chakudyacho, mkono wake udzasonyeza kukhala wamphamvu; ngati chili choipa kwa iye, minyewa yake idzakhala yofooka.b
Ena amene ayesa zimenezi akukhulupirira kuti zimagwira ntchito ndi kuti chiyambukiro chimachokera mu mphamvu zimene zili m’thupi. Amalingalira kuti pali zinthu zambiri zimene sayansi yamakono singathe kuzifotokoza komabe zimene zimagwira ntchito kapena zimene zingaonedwe. Motero, iwo amanena kuti mwina pangakhale ngalande za mphamvuzo kapena kuloŵerana pakati pa mphamvuzo ndi zinthu, ngakhale kuti madokotala sanatulukirebe kapena kuvomereza zimenezi.
Komanso, buku lotchedwa Applied Kinesiology likuti: “Nthaŵi zina [mabuku] amaphunzitsa kuti zinthu za mpangidwe wamadzi, zonga chakudya chomanga thupi, zimayesedwa mwa kuika chinthucho m’manja ndi kupima minyewa. Palibe umboni umene umapereka lingaliro lililonse la kudalirika kwa mtundu umenewu wa kupima. . . . Mkhalidwe wa maganizo wa kulingalira kukhala wodziŵa zinthu ungakhale wamphamvu kwambiri kwakuti maganizo olakwa a sing’angayo angamdodometse kupeza chidziŵitso cholondola mu mchitidwe wa kupima.” “Wopima amene ali wodziŵa kwambiri kupenda minyewa ndi manja angapangitse mnyewa wa wodwalayo kuonekera kukhala ngati wofooka kapena ngati wamphamvu mosavuta ndi luntha lake mwa kungosintha . . . kupimako pang’ono chabe.”
Chenjerani!
Komabe, kupima minyewa kwina kumaposa pamenepo. Talingalirani za kumene kumatchedwa “kupimidwira wina.” Kumeneku kungachitidwe kaamba ka munthu wokalamba kapena mwana amene ali wofooka kosakhoza kupimidwa. Pamene wopimidwira winayo amakhudza khanda, dokotala amapima mkono wa wopimidwira winayo. Zimenezi zagwiritsiridwa ntchito ngakhale kuziŵeto zapanyumba; mkono wa wopimidwira winayo umapimidwa atauika pa galu wa mtundu wa collie, German shepherd, kapena ziŵeto zina zodwala.
Sikuli kwa ife kuweruza machitidwe otero, komano mungafunse kuti, ‘Kodi mphamvu zathupi nzimene zimachititsa ziyambukiro zimenezi?’ Asayansi apereka umboni wa kukhalapo kwa mitsitsi ya dongosolo la m’chilengedwe, microwave, ndi mitundu yosiyanasiyana ya electromagnetic radiation. Komabe, kodi zolengedwa zonse, ngakhale makanda ndi ziŵeto za panyumba, zili ndi mphamvu mkati mwake zimene zingatuluke ndi kupimika kaamba ka munthu wina? Ababulo analingalira kuti mphamvuzo zingatuluke ndi kuyambukira nkhosa. Inu mungadzifunse kuti, ‘Kodi ndimakhulupirira kuti kanthu kena kofananako kangachitike pakati pa anthu kapena nyama lerolino? Kapena kodi ziyambukirozo zingakhale ndi mafotokozedwe ena?’
Ochiritsa ena amanena kuti amatha kupima “mphamvu” za munthu ndi zipangizo zonga masipuling’i achitsulo kapena ma pendulum. Zimenezi zikunenedwa kuti zimayendayenda pamene “dera la mphamvu” za wochiritsayo liloŵerana ndi la wodwala. Wochiritsa wina yemwenso ali mlembi pankhaniyi, amene panthaŵi ina anali wofufuza wasayansi, nthaŵi zina amapima matenda ndi pendulum. Iye akunenetsanso kuti angathe kuona “dera la mphamvu za munthu” kapena cheza cha mitundu yosiyanasiyana chimene akuti chimazinga munthu. Iye akunena kuti amagwiritsira ntchito “masomphenya amkati” kusuzumirira m’thupi kuti aone zotupa, maselo amwazi, kapena ma microbe, ndi kuona zakale.c
Monga momwe kwasonyezedwera poyamba, kupima mphamvu mwa njira ya nyonga ya mkono kwagwiritsiridwa ntchito kupimira malingaliro. Buku lina lofalitsidwa kwambiri linati: “Ngati mufuna kuphatikizapo kupima pang’ono malingaliro panthaŵi imodzimodziyo, funsani momveketsa mawu kuti ‘Kodi muli ndi vuto?’ ndi kupimanso. Kaŵirikaŵiri zimenezi zimafooketsa mkono ngati chakudya chili choipa.” Ena amagwiritsira ntchito kupima kotero “kuti adziŵe nyengo yeniyeni imene kuvulala kwakuthupi, kwa malingaliro kapena kwauzimu” kunachitika. Kumagwiritsidwanso ntchito kupangira zosankha ‘zovomerezeka kapena zosavomerezeka’ pa nkhani zatsiku ndi tsiku.
Mwachionekere, ambiri a amene amachita kupima kotero (kinesiology) anganene kuti mchitidwe wawo umasiyana ndi zimene zangosimbidwa kumene, kuti palibe kulambira mizimu kumene kumaphatikizidwamo, kapena kuti samapima malingaliro. Komabe, kodi zimene amachitazo nzozikidwabe pa kukhulupirira mphamvu zimene zimakhala mwa munthu aliyense zimene zingapimidwe kapena kuonedwa kokha ndi anthu ena akutiakuti onena kuti ali ndi mphamvu zinazake?
Akristu samaona nkhani zotero mopepuka. Mulungu analangiza Israyeli kuti: “Tsiku lokhala mwezi ndi sabata, kumema masonkhano, sindingalole mphulupulu ndi masonkhano.” (Yesaya 1:13) Pamene mtundu umenewo unakhala wampatuko, unali ‘kuombeza ula, nuchita zanyanga.’ (2 Mafumu 17:17; 2 Mbiri 33:1-6) Mwachionekere iwo anafunafuna kudziŵa zinthu mwa kuchita madzoma apadera, ndiyeno ananena “zopanda pake.”—Zekariya 10:2.
Kupima minyewa kwina kungakhale kosalakwa, kochitidwa popanda kuvulaza wodwalayo kapena dokotala. Komabe, mwachionekere, kwina kungakhale ndi mbali zopanda pake kapena zachilendo, monga ngati masomphenya a kuona zamkati, cheza chachilendo, ndi kugwiritsiridwa ntchito kwa pendulum. Akristu sayenera kugwiritsira ntchito mphamvu zopanda pake. Iwo sayenera ngakhale kuyesa zinthu zotero, pakuti iwo alibe chidwi ndi zakuya za Satana. (Chivumbulutso 2:24) M’malo mwake, pali chifukwa chabwino chosonyezera kusamala ponena za kanthu kalikonse kamene kakuonekera kukhala kogwirizana ndi mchitidwe wa kulambira mizimu, umene Mawu a Mulungu amatsutsa.—Agalatiya 5:19-21.
Zimene wochiritsa amachita zili thayo lake, ndipo sicholinga chathu kupenda ndi kupereka chigamulo pa zonena za aliyense kapena njira. Ngakhale ngati mulingalira kuti zina za michitidwe imeneyi zimaphatikizapo mphamvu zopanda pake, nkoonekera bwino kuti ambiri amene anaziyesa anatero mosadziŵa konse, alibe ganizo la kuloŵa m’kulambira mizimu. Zingangochitika kuti zinali chisonyezero cha chikhumbo chawo chachikulu chakuti akhale ndi thanzi labwino. Chikhalirechobe, ena amene akhala ophatikizidwa m’machitachita otero pambuyo pake aona kuti mapindu alionse othekera akuthupi sanali ofunikira kudziloŵetsa mu upandu wauzimuwo.
Kachiŵirinso, munthu aliyense ayenera kusankha zimene angachite ponena za nkhani zaumwini zotero. Komabe, Akristu ayenera kukumbukira uphungu wa Mulungu wakuti: “Wachibwana akhulupirira mawu onse; koma wochenjera asamalira mayendedwe ake.” (Miyambo 14:15) Zili chimodzimodzinso ndi machiritso.
Satana ali wofunitsitsa kucheukitsa atumiki a Mulungu pa kulambira koona. Mdyerekezi angakondwere ngati angachite motero mwa kuchititsa Akristu kukhala ndi chidwi ndi zinthu zina. Iye akakhaladi wokondwa kwambiri ngati iwo akhala ndi chidwi ndi zinthu zimene zili, kapena zimene zikuonekera kukhala machitidwe achilendo amene angawaloŵetse m’kulambira mizimu.—1 Petro 5:8.
Ngakhale kuti Akristu sali pansi pa Chilamulo cha Mose, maganizo a Yehova Mulungu kulinga ku machitachita a matsenga sanasinthe. Monga momwe kwasonyezedwera poyambirirapo, Mulungu analamula Aisrayeli kuti “wosamalira mitambo, kapena wosamalira kulira kwa mbalame, kapena wanyanga. Kapena wotsirika” sanafunikire kupezeka pakati pawo. “Aliyense wakuchita izi Yehova anyansidwa naye; . . . Mukhale angwiro ndi Yehova.”—Deuteronomo 18:10-13.
Pamenepa nkwanzeru chotani nanga kwa Akristu lerolino kuvalabe ‘zida zonse za Mulungu . . . chifukwa chakuti tikulimbana . . . ndi magulu a mizimu oipa a m’miyamba’!—Aefeso 6:11, 12, NW.
[Mawu a M’munsi]
a Lerolino anthu ambiri akali kupitabe kukaonana ndi ashamani, asing’anga, kapena ochiritsa ena ofanana nawo. Mshamani ndiye “wansembe amene amagwiritsira ntchito matsenga kaamba ka chifuno cha kuchiritsa odwala, kuombezera zobisika, ndi kulamulira zochitika.” Sing’anga, kapena mshamani, angasanganize pamodzi mankhwala azitsamba ndi michitidwe ya kulambira mizimu (akumapembedzera mphamvu zachinsinsi). Mkristu wosamala ndi wokhulupirika akapeŵa kuloŵa m’kulambira mizimu kotero, ngakhale ngati kuonekera kukhala kukumachiritsa.—2 Akorinto 2:11; Chivumbulutso 2:24; 21:8; 22:15.
b Awa ndi mafotokozedwe achisawawa, koma michitidwe yakupimako ingakhale yosiyanasiyana. Mwachitsanzo, wodwalayo angapemphedwe kupanikizitsa pamodzi chala chake chamanthu ndi chamkombaphala, ndipo wochiritsayo namayesa kuzikanula.
c Iye akulemba kuti: “Kodi ndimotani mmene zochitika zoonekera kukhala zozizwitsa zimenezi zimachitikira? . . . Njira imene ndimagwiritsira ntchito imatchedwa kuika manja, kuchiritsa ndi chikhulupiriro, kapena kuchiritsa kwauzimu. Sili njira yachilendo konse, koma ndiyo yolongosoka kwambiri . . . Aliyense ali ndi dera la mphamvu kapena cheza chimene chimamzinga ndipo chimatulukira m’thupi. Dera la mphamvu limeneli nlogwirizanitsidwa kwambiri ndi thanzi. . . . High Sense Perception ndiyo mtundu wa ‘kuona’ mu umene umaona chithunzithunzi chake m’maganizo ako popanda kugwiritsira ntchito maso ako anthaŵi zonse. Sikuyerekezera. Nthaŵi zina kumatchedwa kuti clairvoyance.”