Omaliza Maphunziro a Gileadi Ofunitsitsa Kufalitsa Mbiri Yabwino
“NCHINTHU chabwino koposa chimene sitinachilingalirepo.” Umu ndimmene Anders ndi Amalia Groth anaonera maphunziro awo aumishonale. Iwo anasonyeza malingaliro a omaliza maphunziro 48 onse a kalasi la 97 la Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower pamene anawonjezera kuti: “Maphunziro a Gileadi atisonkhezera ndi kutikonzekeretsa, chotero tili ofunitsitsa kupita ku magawo athu atsopano.”
Tikhoza kuona chisangalalo chimenechi pamene ophunzirawo akukambapo ponena za programu ya kumaliza maphunziro; anthu 6,420 anasonkhana pachochitikacho pa September 4, 1994.
“Theodore Jaracz wa Bungwe Lolamulira anatsegulira programuyo mwa kukamba nkhani yakuti ‘Kuphunzitsidwa ndi Yehova,’” anatero David Abel ndi mkazi wake, Kelli. “Mfundo imene sitidzaiŵala konse ndi imene Mbale Jaracz anatchula pamene anati: ‘Tiyenera kuzindikira kuchepa kwathu poyerekezera ndi Yehova,’ nachitira fanizo zimenezo ndi phunziro lamphamvu limene lili pa Yobu machaputala 38 ndi 39. Mbale Jaracz anatchula molunjika kuti pamene kuli kwakuti tawonjezera chidziŵitso chathu cha Baibulo kupyolera m’Sukulu ya Gileadi, sitikudziŵa mayankho a mafunso onse. Tiyenera kupitirizabe kuphunzira Mawu a Mulungu.”
Ndiyeno Christian ndi Angele Coffy anati: “Tinachita chidwi ndi nkhani imene Max Larson anakamba yakuti ‘Kodi Ubwino wa Maziko Abwino Ngwotani?’ Tinakonda kutiyerekezera kwake ndi nyumba imene imafunikira maziko akuya m’nthaka yolimba kuti ikhalebe yolimba ngakhale kutachitika chivomezi. Mwa kuphunzira mwakhama, tingakulitse unansi wolimba ndi Yehova ndipo tingazike chikhulupiriro chathu pa chidziŵitso chakuya kwambiri kwakuti tingachirimike m’nthaŵi zovuta.”
“Nkhani imene Milton Henschel, pulezidenti wa sukuluyo anakamba, yamutu wakuti ‘M’Minda Mwayera Kufikira Kumweta,’ tidzaikumbukira kwa nthaŵi yaitali,” anatero Gary ndi Lynn Elfers. “Lemba lalikulu la nkhaniyo, Yohane 4:35-38, linagogomezera mwaŵi umene tili nawo wa kuloŵa m’munda umene mbewu zake zinafesedwamo kale ndi antchito apapitapo. Limeneli lidzatisonkhezera kugwira ntchito mofulumira.” Akuvomereza zimenezo, Jan ndi Sirpa Vaahtola anati: “Mbale Henschel anakulitsa chiyembekezo chathu cha kumweta kumene kuli patsogolopa mwa kupereka lipoti latsopano la kumaiko a Baltic States. Chiwonjezeko ku Estonia chinali 51 peresenti, ku Latvia 106 peresenti, ndipo ku Lithuania 51 peresenti. Ha, zimenezo nzosangalatsa chotani nanga! Abale kumeneko akupempha Mbuye kutumiza antchito owonjezereka. Tinakondwa kwambiri kumva zimenezi, pakuti gawo lathu ndi Estonia!”
“Ndiyeno panatsatira Joel Adams ndi mutu wakuti ‘Dalirani Yehova,’” anakumbukira motero Kevin ndi Evelyn Cortina. “Iye anatilangiza kuti sitiyenera kulingalira kuti nthaŵi zina tingadalire Yehova ndi kuti nthaŵi zina tingadalire pa kulingalira kwathu. M’gawo lathu tidzakumana ndi mavuto ambiri—athanzi, achakudya, achinenero, amiyambo, ndi ena otero. Zonsezo zidzafuna kuti tidalire Yehova.”
Kenako panatsatira Gerrit Lösch, chiŵalo cha Bungwe Lolamulira, amene anakamba nkhani yamutu wakuti “Pitirizanibe Kusonyeza Chifundo cha Yehova.” Alen ndi Ann Marie Gokavi anati: “Iye ananena kuti kusonyeza chifundo kwa amishonale anzathu ndi awo amene timauza mbiri yabwino ndiko umboni wa uchikulire Wachikristu. Magawo akumaiko akunja amafuna kudzimana, koma ngati palibe chifundo, ndiye kuti kudzimana kwathu kudzakhala kosaphula kanthu.” (Mateyu 9:13) Peter ndi Fleur Hupston anawonjezera kuti: “Mbale Lösch anati tiyeneranso kuchitira chifundo abale ndi alongo athu, tikumawayang’ana kupyolera mu [binoculars] yotembenuzidwa, titero kunena kwake, kuti zophophonya zawo zichepetsedwe m’malo mwa kukulitsidwa.”
“Jack Redford, mmodzi wa alangizi athu a Gileadi anatsatira ndi nkhani yamutu wakuti ‘Kodi Mungalabadire Chidzudzulo?’” anakumbukira motero Mickey ndi Sherry Minsky. “Iye anasonyeza kuti kunyada kumachititsa kulabadira chidzudzulo kukhala kovuta ndi kuti ngati timaipidwa msanga ndi uphungu, sitidzapeza mapindu ake. Ndiyeno anapereka malingaliro ogwira ntchito onena za kulabadira chidzudzulo ozikidwa pa Maliro 3:27-31.” Charles ndi Joan Held anawonjezera kuti: “Nthaŵi zambiri sitimaona zolakwa zathu; chifukwa chake, tiyenera kuona chidzudzulo monga njira yotsegulira maso athu kuti tione zimene sitinali kudziŵa. Chidzudzulo kapena uphungu wochokera kwa Yehova uli umboni wa chikondi chake kwa ife.”
“Mlangizi winanso, Ulysses Glass, anakamba nkhani yamutu wakuti ‘Pezani Nzeru Yeniyeni Imene Imatsogolera ku Moyo.’ Iye anafunsa kuti: ‘Kodi mudzachitanji ndi zimene mwaphunzira?’” anatero Kenneth ndi Lisbeth Ardkäll. “Ndiyeno anapereka fanizo lotengedwa pa Miyambo 30:24-26 lonena za mbira ndi mmene Yehova anaikonzekeretsera kaamba ka moyo. Komabe, ifeyo sitimakhala anzeru mwachibadwa, chotero tifunikira kuyesetsa kuti tiipeze nzeruyo. Yehova watipatsa zonse zimene tifunikira kuti tichite zimenezo. Tidzachita zochuluka malinga ngati tayandikira kwa Yehova ndi kwa wina ndi mnzake m’chikondi.”
Nkhani Yaikulu
“Mbale Karl F. Klein, chiŵalo cha Bungwe Lolamulira, anapenda nafe mwaumoyo Salmo la 19 m’nkhani yake yakuti ‘Ngale Pakati pa Ngale Zina,’” anatero Jay ndi Gwen Abraczinskas. “Iye anasonyeza kuyamikira kwakukulu kumene wamasalmo Davide anali nako pa Yehova ndi kukonda kwake Mawu a Mulungu.” “Mbale Klein anagaŵa salmolo patatu,” anatero Keith ndi Donna Hornback. “Mbali 1 (mavesi 1-6) imasonyeza kuyamikira kwa Davide chilengedwe cha Mulungu, mbali 2 (mavesi 7-10) imasonyeza kuyamikira malamulo a Mulungu, ndipo mbali 3 (mavesi 11-14) imatikumbutsa kuti, mofanana ndi Davide, tifunikira kukhala ndi unansi wabwino ndi Yehova.”
“Tinakonda kwambiri mfundo yakuti kuwopa Yehova kuli kofunika ngati titi tipeŵe choipa. Kumeneku kumatisonkhezera kuchita chabwino pamaso pake,” anatero David ndi Raylene Long. Frank ndi Vibeke Madsen anavomereza zimenezo. “Ndemanga za Mbale Klein ponena za mmene zikumbutso za Yehova, malamulo, ndi ziweruzo zake zilili zopindulitsa zinafotokoza bwino mwachidule zimene tinaphunzira ku Gileadi,” iwo anatero. “Zimenezo zinatichititsa kukhala otsimikizadi kumamatira ku Mawu a Mulungu mtsogolo ndi kuwaona monga nkhokwe ya ngale.”
Pambuyo pa nkhani yaikulu, ophunzirawo analandira madipuloma awo, ndipo magawo awo akumaiko akunja analengezedwa. Pambuyo popuma kaamba ka chakudya, onse anasonkhananso kaamba ka gawo lamasana. Omaliza maphunzirowo anayankha mafunso ofunsidwa pa Phunziro lachidule la Nsanja ya Olonda.
“Ndiyeno panatsatira programu ya ophunzira yakuti ‘Ophunzitsidwa Kukhala Olengeza Ufumu pa Dziko Lonse Lapansi,’” anakumbukira motero Bob ndi Shannon Lakatos. “Mbali yoyamba inali ya zokumana nazo zimene ophunzira anali nazo mu utumiki wakumunda m’miyezi isanu ya maphunziro. Inagogomezera mmene mafunso angagwiritsidwire ntchito mwaluso mu utumiki wathu. Mbali ya kufunsa inasonyeza njira zabwino zolimbanirana ndi mavuto ndi mikhalidwe yachilendo ya moyo wa umishonale. Masilaidi ambali zitatu, onena za Costa Rica, India, ndi Malaŵi, anatipatsa chithunzi cha gulu la Yehova la padziko lonse.”
“Seŵero limene linatsatira lakuti Khalani a Teokrase, Osati Akudziko, linasonyeza chiyambukiro choipa chimene achibale athu akudziko, odzigangira, angakhale nacho,” anatero Jesse ndi Michelle Duncan. “Linasonyeza kuti Akristu ayenera kuzindikira zitsogozo ndi malangizo a Teokrase kukhala zofunikira ndi zopindulitsa,” anawonjezera motero Wenzel ndi Kelly Koula.
Nyimbo yomaliza ndi pemphero zinafikitsa kumapeto programu yosangalatsayo. Pamene omaliza maphunziro anachoka ndi chiyembekezo cha kupita ku magawo awo akumaiko akunja 18, malingaliro awo anasonyezedwa bwino lomwe ndi mawu otsazika otsatirawa a Tommi ndi Jael Kauko: “Tikufunitsitsa kupita kugawo lathu ndi kukagwiritsira ntchito zimene taphunzira. Talandira zochuluka kwambiri—tsopano ndi nthaŵi yathu ya kupatsa.”
[Chithunzi patsamba 26]
Kalasi la 97 la Omaliza Maphunziro a Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower
M’ndandanda pansipa, mizera ikuŵerengedwa kuyambira kutsogolo kumka kumbuyo, ndipo maina andandalikidwa kuyambira kulamanzere kumka kulamanja mumzera uliwonse.
(1) Hong, J.; Hong, D.; Groth, A.; Cortina, E.; Lakatos, S.; Hornback, D.; Acevedo, L.; Coffy, A. (2) Elfers, L.; Gokavi, A.; Ardkäll, L.; Abraczinskas, G.; Knott, K.; Lizer, T.; Abel, K.; Abel, D. (3) Duncan, M.; Gokavi, A.; Held, J.; Hupston, F.; Lakatos, B.; Long, R.; Minsky, S.; Acevedo, E. (4) Ardkäll, K.; Kauko, J.; Vaahtola, S.; Cortina, K.; Carson, N.; Minsky, M.; Lizer, G.; Koula, K. (5) Duncan, J.; Abraczinskas, J.; Vaahtola, J.; Madsen, F.; Madsen, V.; Long, D.; Carson, C.; Elfers, G. (6) Kauko, T.; Hupston, P.; Held, C.; Groth, A.; Hornback, K.; Koula, W.; Knott, D.; Coffy, C.