Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 11/15 tsamba 8-9
  • Mboni za Yehova Padziko Lonse—Poland

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mboni za Yehova Padziko Lonse—Poland
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Olimba Mtima pa Kuvumbula Chinyengo
  • ‘Ndi Zipatso Zawo’
  • Mboni za Yehova Padziko Lonse—Thailand
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Mboni za Yehova Padziko Lonse—Lipabuliki la Philippines
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Mboni za Yehova Padziko Lonse—India
    Nsanja ya Olonda—1995
Nsanja ya Olonda—1994
w94 11/15 tsamba 8-9

Mboni za Yehova Padziko Lonse​—Poland

M’CHILIMWE cha mu 1989, maboma Akomyunizimu kuyambira ku Baltic mpaka ku Black Sea anayamba kugwa. Pamene Iron Curtain inali kung’ambidwa pakati, mitundu ya ku Eastern Europe inayamba kufunafuna njira zawo zochitira zinthu. Pakati pawo panali Poland, dziko la zitunda, zidikha, ndi mapiri amakolokoto.a

Anthu Achipolishi amagwira ntchito zolimba, ndipo Poland watulutsa ena a akatswiri otchuka m’dziko ojambula zithunzi ndi asayansi. Komabe, zoposa zimenezo, tsopano pali gulu lomakulakula la olengeza mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu.

Olimba Mtima pa Kuvumbula Chinyengo

M’Poland muli anthu ochuluka ofuna kuphunzira choonadi cha Baibulo. Koma ena amalepheretsedwa ndi achibale kapena anansi. Mwachitsanzo, kumalo apafupi ndi Wrocław, mkazi wokondwerera analeka kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova pamene banja ndi mabwenzi ake anamvutitsa. Komabe, mwana wake wachitsikana anaŵerenga mpambo wa nkhani za Nsanja ya Olonda zovumbula chipembedzo chonyenga. Zimenezi zinadzutsa chikondwerero chake pa choonadi.

Pambuyo pophunzira Baibulo kwa miyezi isanu ndi umodzi, wachichepereyu anasankha kuleka kugwirizana kulikonse ndi chipembedzo chonyenga. Iye anafikira mtsogoleri wachipembedzo wa tchalitchi chake kuti amuuze za chosankha chake. Iye anauza mtsikanayo kuti ayenera kulemba izi: “Ine, K​—​— P​—​—, ndakana chikhulupiriro cha Chikatolika.”

Pa Sande yotsatira, mawuŵa anaŵerengedwa m’tchalitchi. Agogo aamuna a msungwanayo anakomoka, ndipo agogo ake aakazi analira misozi. Komabe, ziŵalo zina za tchalitchi zinakondwera naziti: “Aha, tsopano papezeka munthu wolimba mtima wokhoza kunena kuti muli chinyengo chochuluka m’tchalitchi chathu.” Wachichepere wolimbika mtima ameneyu tsopano ndi mlongo wauzimu wobatizidwa ndipo wayambitsa maphunziro a Baibulo asanu ndi aŵiri m’mudzi wawo.

‘Ndi Zipatso Zawo’

Magazini a Kujawy i Pomorze a mlungu ndi mlungu anafalitsa lipoti lakuti “Mudzawazindikira ndi Zipatso Zawo.” M’mawu ake ena, nkhaniyo inati alambiri a m’Dziko Lachikristu “kwenikweni sakusamalira mwamphamvu miyezo yachipembedzo yomwe ailandira. Iwo akusiyana kotheratu ndi Mboni za Yehova zomwe zimachita mogwirizana ndi zimene zimanena, ndipo zimanena zimene Baibulo limalamula.”

Litasiyanitsa kaonekedwe ka Mboni ndi ka Akristu a dzina, lipotilo linapitiriza kuti: “Otchulidwa pambuyowa mwachionekere sakudziŵa, ndipo kaŵirikaŵiri samagwiritsira ntchito ziphunzitso zofunika ndi miyezo ya chikhulupiriro chawo. . . . Mwa mkhalidwe wawo, Mboni za Yehova zimasonyeza mgwirizano wa mawu awo ndi zochita zawo, motero zikumatsimikizira kuti sizili ‘aneneri onyenga,’ m’malo mwake, zingazindikiridwe ndi zipatso zawo. ‘Kodi atchera mphesa paminga, kapena nkhuyu pamtula?’ (Mateyu 7:15-20).”

Mkazi wina analemba kalata ku magazini a Przyjaciółka a mlungu ndi mlungu, akumadandaula kuti mwana wake wamwamuna anasiya Tchalitchi cha Katolika nakhala mmodzi wa Mboni za Yehova. Kodi mkonzi anapereka uphungu wotani? “Ngati mwana wanuyo wagwirizana ndi Mboni za Yehova, naphunzira chikhulupiriro chawo ndi kuchilandira, chili chosankha chake, ndipo chiyenera kuŵerengeredwa ndi kulemekezedwa. . . . Gulu lachipembedzo limeneli nlodziŵika ndi mikhalidwe yambiri ya mayanjano yabwino ndi yokhumbirika, yonga ngati umodzi wawo wapadera ndi kugwirizana kwenikweni, kuona mtima kwakukulu ndi kulondola mosamalitsa malamulo ovomerezeka a chitaganya, ndiyeno, kukhoza kwawo kukhala ndi moyo wogwirizana ndi choonadi chawo, akumachita kwenikweni mikhalidwe imene amaiphunzitsa. Imeneyi ndiyo mikhalidwe yamtengo wapatali.”

[Mawu a M’munsi]

a Kuti mupeze chidziŵitso chowonjezereka, onani Kalenda ya Mboni za Yehova ya 1994.

[Bokosi patsamba 9]

ZIŴERENGERO ZA DZIKOLO

Chaka Chautumiki cha 1993

CHIŴERENGERO CHAPAMWAMBA CHA OCHITIRA UMBONI: 113,551

KUGAŴA: Mboni 1 kwa 339

OFIKA PA CHIKUMBUTSO: 235,642

AVAREJI YA OFALITSA AUPAINIYA: 7,961

AVAREJI YA MAPHUNZIRO A BAIBULO: 79,131

CHIŴERENGERO CHA OBATIZIDWA: 8,164

CHIŴERENGERO CHA MIPINGO: 1,397

OFESI YA NTHAMBI: Nadarzyn

[Chithunzi patsamba 9]

Ofesi ya nthambi ya Poland mu Lodz mu 1948

[Chithunzi patsamba 9]

Ntchito ya zikwangwani, June 1948, mu East Prussia wakale

[Chithunzi patsamba 9]

Ziŵalo 72 za a pa Beteli ya Poland, January 1993

[Chithunzi patsamba 9]

Nthambi yatsopano mu Nadarzyn

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena