Ngakhale Kuti Ali Othaŵa Kwawo, Ali Achimwemwe Kutumikira Mulungu
NKHONDO, njala, masoka, ndi zipwirikiti. Kwa anthu ena mawu ameneŵa angokhala mitu ya nkhani. Kwa ena ambiri zimenezi zili mbali ya moyo watsiku ndi tsiku. Pokhala gulu la Akristu la padziko lonse, Mboni za Yehova zimazindikira kuti nthaŵi iliyonse pamene nkhondo iulika kapena pamene tsoka lichitika, ena a gulu lawo laubale angavutike. Ndipo pamene anthu afunikira kuthaŵa, abale athu angafunikirenso kuchita chimodzimodzi.
Kwazaka zambiri Mboni m’maiko ambiri a mu Afirika zapirira zokumana nazo zotero. Ambiri a iwo analongedza kanthu kena kalikonse kamene akanatha kunyamula ndi kuthaŵira kwinakwake. Ngakhale kuti oŵerengeka akhala ndi zoyendera, mwinamwake njinga, unyinji wa iwo anakakamizika kuyenda kwanthaŵi yaitali—kwa masiku, ngakhale milungu—kuti akafike kumalo kumene akupita.
Malo amodzi otero anali tauni ina yaing’ono yotchedwa Mboki, mu Central African Republic. Kwazaka zambiri, amuna ndi akazi, aang’ono ndi achikulire, adza m’zikwi zambiri. Pakati pawo panali abale ndi alongo athu Achikristu ambiri, limodzi ndi anthu okondwerera. Zoonadi, Akristu anzawo ku ofesi ya nthambi ya Watch Tower Society ku Bangui, likulu la Central African Republic, anafunitsitsa kukumana ndi othaŵa kwawo ameneŵa kuti awathandize. Kasanu, woimira anatumizidwa ndi ndalama, chakudya, zovala, ndi mankhwala, zoperekedwa mooloŵa manja ndi Mboni za mu Bangui, wokhala pautali wa mtunda wa pafupifupi makilomita 1,130. Ngakhale kuti awo amene anapereka thandizo looloŵa manja limeneli analibe ndalama zambiri, iwo anali achimwemwe kuchita zimene akanatha.
Kufika ku Mboki
Abale a ku ofesi ya nthambi anafuna kuona kanthu kena kamene kangachitidwe ndi mmene othaŵa kwawo amenewo angathandizidwire mwauzimu. Chotero mkazi wanga ndi ine tinayamba ulendo pa Land Cruiser yamphamvu, limodzi ndi Symphorien, mpainiya wapadera, ndi mkazi wake. Symphorien anadziŵa bwino msewuwo, ndipo amalankhula Chizande, chinenero cha othaŵa kwawo a ku Mboki. Panatenga masiku anayi otopetsa kukafika kumeneko.
Ulendo wa makilomita pafupifupi 400 otsirizira tinapyola dera lokongola la tizitunda ndi mitengo yaikulu ya mulambe. Tinadutsa timidzi ta apo ndi apo. Pa mtunda umenewu wa msewu, mkazi wanga anaŵerenga milatho yokwanira 50—yambiri ya iyo yokhala mumkhalidwe woipa, ina yosawolokeka. Tinakonza milatho ina ndi mitengo ndi mitanda yakale, kuika giyala ya mphamvu ya galimotolo, kupemphera, ndi kudutsapo mosamala. Ngati pamalopo panali pafupi ndi mudzi waung’ono, achichepere ankathamanga kudzatithandiza—ndi kulipidwa ndalama pang’ono. Tinadabwa kuona kuti iwo anakhoza kupeza zidutswa za matabwa pansi pa mlatho m’maudzu ndi m’zitsamba zowirira zapafupi. Zinatipangitsa kudabwa ngati zimenezi zinachotsedwa mwadala ndi kusungidwa mmenemo kaamba ka makasitomala ozifuna.
Pa nthaŵi zitatu tinakana thandizo la achicheperewo, pakuti milathoyo inaonekera kukhala yangozi kwambiri kuwolokapo. Chotero tinayendetsa galimotolo m’tchire, kuloŵa m’khwaŵa, kuwomboka pamiyala, kukweranso chitunda, ndi kubwereranso mu msewu. Tinali okondwa chotani nanga kuti imeneyi inali nyengo yachilimwe, mwinamwake sitikanapeza njira yoyendera ulendowo, kusiyapo mwinamwake ndi helikopitala!
Kodi Mboki akakhala wotani? Kaŵirikaŵiri funso limeneli linkafika m’maganizo pamene tinali kuyenda ndi galimoto mu “piste” yosatha imeneyi, liwu Lachifrenchi logwiritsiridwa ntchito mu Central African Republic kutanthauza msewu kapena njira ya mchenga, ya nsangalabwi, ndi ya miyala ndi njerwa zophwanyika—ndi mokumbika mwambirimbiri.
Patsiku lachinayi, cha kumasana, Symphorien analoza tinyumba tina taudzu tozingidwa ndi mitengo ya papaya ndi minda ya chinangwa. “Voilà! Apa mpamene Mboki amayambira,” ananena mokweza mawu. Tinadabwa kwambiri ndi zimene tinaona. “Mboki? Nanga msasawo uli kuti?” tinafunsa motero, pakuti zimene tinaona sizinali msasa, koma nyumba zokhazokha zokhala patalipatali. Izo zinali nyumba zazing’ono komano zaudongo zofoleredwa ndi udzu. Panalinso mitengo ndi zitsamba paliponse. Anthu amabzala mbewu pafupi ndi nyumba zawo. Mboki sanali mtundu wa msasa umene tinayembekezera kuona; anali mudzi waukulu, wa makilomita pafupifupi 35 utali wake.
Kukumana ndi Abale
Abale a ku Mboki anadziŵa kuti tinali kubwera, ngakhale kuti analingalira kuti ulendo wathu ukatitengera masiku asanu. Pamene anamva kulira kwa galimoto lathu, anadza akumathamanga. Amuna, akazi, ndi ana anatuluka m’nyumba zawo ndi m’midzi mothamanga ndiponso kuchokera kuminda yawo kudzatipatsa moni. Aliyense anali kumwetulira, kuseka, kugwirana nafe chanza, nthaŵi zina kangapo konse. Anatipatsa moni atanyamula makanda awo. Onse anafuna kutilonjera, ndipo anatilandiradi ndi manja aŵiri.
Panthaŵiyo panalibe zambiri zochita kwa mkazi wanga ndi ine chifukwa cha chinenero. Tinayesa kulankhula Chifrenchi pang’ono, Chisango pang’ono, Chingelezi pang’ono, ndi Chiluya. Abale athu ochuluka amalankhula, kuŵerenga, ndi kulemba Chizande. Symphorien anafunikira kutanthauzira, akumafotokoza chifuno cha kufika kwathu.
Tinapitiriza ndi ulendowo kwa makilomita angapo ndi kufika pa Nyumba Yaufumu. Iyo inali “tchalitchi” choyamba kumangidwa ndi othaŵa kwawo achipembedzo ku Mboki. Abale ambiri ndi ana awo ndi okondwerera anafika kudzatipatsa moni. Ngakhale ana ena apafupi anafika ndi abalewo kudzatipatsa moni.
Abale athu anali atatikonzera nyumba ziŵiri zazing’ono, alendo awofe. Zinali zaudongo kwenikweni. Ndowa za madzi abwino zinaikidwamo ndipo zinali kutiyembekezera. Tinali titabweretsa chakudya chathu ndi madzi akumwa, tikumayembekezera kukumana ndi mkhalidwe wovuta ndi kuti tisalemetse abale athu. Pamene tinali kutsitsa katundu pa galimoto, msungwana wina wachichepere anafika nafunsa kuti tingakonde nkhuku yophikidwa motani usikuwo, yowotcha kapena ya msuzi? Sitinayembekezere zimenezo ndipo tinafunsa kuti anali atalinganiza kuidyera ndi chiyani. Yankho lake: chinangwa kapena mbwani. Chotero tinasankha nkhuku ya msuzi. Njala yathu yaikuluyo inathetsedweratu usikuwo. Koma iwo anapitirizabe kutidyetsa tsiku lililonse—masana ndi madzulo. Sitinkatha kukhululupirira—othaŵa kwawo kutidyetsa ndi kutisamalira, ngakhale kuti iwo eniwo analibe zambiri.
Mpingo Waung’ono Wachimwemwe
Ndife pano, kumalo akutalitali chotere komabe pakati pa abale athu 21. Aŵiri okha ndiwo anadza kuno atabatizidwa kale. Ena onse anali anthu okondwerera pamene anadza kuno. Iwo anapitiriza kuphunzira ndipo anabatizidwa m’zaka ziŵiri zapitazo. Enanso anayi anabatizidwa mumtsinje wina wapafupi mkati mwa ulendo wathu.
Chitsanzo chimodzi chapadera ndicho Faustino. Asanadze ku Mboki, anaphunzira ziphunzitso zoyambirira za choonadi cha Baibulo kwa bwenzi lake. Faustino anayamikira zimene anali kuphunzira. Posakhalitsa iye ndi bwenzi lake anayamba kulalikira kwa ena, komano anakumana ndi chitsutso ndipo anaikidwa m’ndende chifukwa cha “kubutsa msokonezo mwa anthu” ndi chipembedzo chawo. Pamene anali m’ndende, bwenzi lake la Faustino linagonja chifukwa cha mantha ndipo linamasulidwa. Miyezi iŵiri pambuyo pake mlandu wa Faustino unazengedwa. Komabe, kunali kwachionekere kuti zinenezo zoikidwa pa iye zinali zopanda maziko, chotero anamasulidwa. Pamene nkhondo inaulika kudera la kwawo, Faustino anathaŵira ku Central African Republic, kumene anakumana ndi abale amene anapitiriza nawo phunziro lake la Baibulo. Anabatizidwa m’July 1991, ndipo mu 1992 analoŵa mu utumiki wanthaŵi yonse monga mpainiya wokhazikika.
Mpingo waung’ono wachimwemwe ndi waubwenziwo ku Mboki tsopano uli ndi mpainiya wapadera mmodzi ndi ofalitsa 21. Abale olankhula Chingelezi aŵiri amatumikira monga akulu ndipo ali okhoza kulankhulana bwino ndi ofesi ya nthambi ya ku Bangui. Tinayembekezera abale athu othaŵa kwawo amenewo kukhala ali mu mkhalidwe wowopsa ndi wothetsa nzeru, koma sizinali choncho. Ngakhale kuti anali osauka mwakuthupi, palibe amene anali kudandaula, kuvutika mtima, kapena kung’ung’udza. Kuyambira pamene anafika abalewo amanga nyumba zawo ndipo ayamba kubzala chakudya ndi kuŵeta nkhuku. Ali ndi zinthu zochepa kuposa zimene anali nazo, koma iwo ali moyo ndipo ali ndi Akristu anzawo.
Popeza kuti pali othaŵa kwawo ofikira chiŵerengero cha pakati pa 17,000 ndi 20,000 ku Mboki, ndipo ena adakafikabe mwezi uliwonse, abale athu ali ndi munda waukulu wa utumiki wawo. Tinamka nawo kukalalikira, kumene kunali kokondweretsadi. Kaŵirikaŵiri iwo amagwiritsira ntchito Baibulo Lachizande, ndipo limeneli lili ndi dzina la Mulungu m’Malemba Achihebri ndipo m’malo angapo m’Malemba Achigiriki Achikristu. Kwa anthu ameneŵa, Mulungu sali “Mboli” chabe (“Mulungu” m’Chizande) komanso “Yekova,” monga momwe amatchulira dzina laumwini la Mulungu. “Mboli Yekova” ndiwo mawu ozoloŵereka. Matembenuzidwe a Aprotestanti m’zinenero zina zambiri za mu Afirika samatsatira kalembedwe kolondola kameneka; mmalomwake, amalemba “Nzapa,” “Nzambe,” mmalo mwa “Yehova” kapena maina ena a mu Afirika a Mulungu.
Mogwirizana ndi ulosi wa Yesu, mbiri yabwino ya Ufumu ikulalikidwa padziko lonse, ngakhale ku Mboki. (Mateyu 24:14) Mpingowo tsopano ukugaŵiridwa Mabaibulo, mabuku, magazini, timabuku, ndi matrakiti m’zinenero zonse zimene umafuna. Mwinamwake mtsogolomu, zofalitsidwa zambiri zidzakhala zopezeka m’chinenero cha Chizande.
Kuyembekezera Mudzi Wachikhalire
Madzulo a tsiku loyamba, tinasonyeza programu ya masilaidi ya Sosaite yakuti “Ofika Pamsonkhano Wachigawo Achimwemwe Kummaŵa kwa Ulaya Atamanda Yehova.” Usiku wotsatira programu yake inali yakuti “Kubweretsa Ochuluka ku Chilungamo m’Nthaŵi Yamapeto.” Masilaidiwo anaonetsedwa pabwalo, pafupi ndi Nyumba Yaufumu, thambo lili lopanda mitambo mwezi uli ngwee. Ha, unali mkhalidwe wokondweretsa chotani nanga! Mazana a anthu anafika kudzaona masilaidi ameneŵa, ndipo abale athu anali achimwemwe ndi onyadira kupereka kanthu kena kapadera kwa anthuwo.
Pamene Lolemba linafika, tinakonzekera ulendo wathu wobwerera. Ukakhalanso ulendo wamasiku anayi pamisewu imodzimodziyo ndi kuwoloka milatho 50 imodzimodziyo. Mlongo wina anaumirira kutiphikira chakudya cha paulendo—nkhuku zina ziŵiri, zowotchedwa kale ndi zothiridwa adyo. Zinanunkhira bwino kwambiri m’maola a mmaŵawo mu Land Cruiser. Masana tinaima pathengo pena kuti tikhwasule nkhuku yowotchayo pamene tinali kuganiza za abale athu ku Mboki. Ngakhale kuti ali oumirizika kukhala othaŵa kwawo, akupitiriza kutumikira Yehova mokhulupirika, akumayembekezera mudzi wachikhalire wa mtendere m’dziko lapansi latsopano lolonjezedwa la Mulungu. (2 Petro 3:13.)—Yoperekedwa.