Mboni za Yehova Padziko Lonse—Nigeria
NIGERIA ali ngati wosomekedwa pangodya ya mmunsi mwa chitunda chakumadzulo cha Afirika. Wokhala pa Gulf of Guinea, iye ali kumpoto pang’ono kwa equator ndipo ali ndi nzika zoposa 88 miliyoni.a
Mkati mwa zaka zautumiki ziŵiri zapitazo, ofesi ya nthambi ya Watch Tower Society ya Nigeria yapereka chisamaliro chapadera kwa achichepere. Kufufuza kwa m’mipingo ya Mboni za Yehova kunasonyeza kuti 80 peresenti ya awo omwe anayamba kulalikira mbiri yabwino mu Nigeria mkati mwa 1992 anali pakati pa misinkhu ya zaka 10 ndi 20. Pa awo obatizidwa mkati mwa chakacho, 63 peresenti anali a msinkhu wa gulu limenelo.
Achichepere Akalimira Upainiya
Achichepere ambiri akuloŵa ntchito yolalikira yanthaŵi yonse monga apainiya. Mpainiya wina wotchedwa Hannah akuti: “Pamene ndinali pafupi kumaliza sukulu, ndinakachezera amene anali pa Sukulu Yautumiki Waupainiya, kumene ndinakumana ndi alongo okalamba aŵiri. Ndinalingalira kuti, ‘Ngati aŵiri aja angachite upainiya, nchifukwa ninji sindingatero?’
“Motero nditamaliza sukulu, ndinakhala mpainiya. Pambuyo pa miyezi itatu ndinakumana ndi Josephine wa zaka zakubadwa 26, wolambira matsenga. Iye anati: ‘Inu Mboni za Yehova ndinu anthu oipa. Simumakondwerera Krisimasi kapena kugwiritsira ntchito njirisi.’ Ndinayankha kuti ngati akandilola kuphunzira naye Baibulo, akadziŵa chifukwa chake sitimachita zinthu zimenezo. Iye anandipempha kupitanso. Posapita nthaŵi anayamba kufika pamisonkhano ndipo anapanga masinthidwe ambiri m’moyo wake. Mu December 1990 anabatizidwa. Chiyambire August 1991, Josephine wakhala mpainiya. Pamene analoŵa Sukulu Yautumiki Waupainiya chaka chatha, anandidziŵikitsa kwa a m’kalasi anzake monga amayi wake wauzimu!”
Vidiyo ndi Nyumba Yaufumu
Imodzi ya mavidiyo ojambulidwa a Sosaite inathandiza mpingo waung’ono kugula malo a Nyumba ya Ufumu. Pofunafuna kogula malo, abale anayi anafikira Onojie, nyakwaŵa wa dera limenelo. Iye anawapatsa puloti pa 20,000 naira ($1,025, U.S.). Mpingowo sukanatha kulipira ndalama zimenezo, popeza kuti panali ofalitsa 17 okha olipirira ntchitoyo. Onojie ameneyo ananena kuti akalingalira za malo ena.
Pambuyo pa miyezi ingapo, mmodzi wa akulu a mpingowo anakacheza kunyumba kwa Onojie. Onojie anali kuonerera vidiyo ya kulongedwa unyakwaŵa kwake. Mkuluyo anati: “Ndili ndi vidiyo imene ndingakonde kuti muione. Imatchedwa kuti Jehovah’s Witnesses—The Organization Behind the Name.”
Pambuyo pake, mkuluyo anafunsa zimene Onojieyo analingalira ponena za vidiyoyo. “Ndinaonerera kanemayo kasanu konse,” anatero Onojie. Mkuluyo anakumbutsa Onojie za Nyumba Zaufumu zimene anaona m’vidiyo ndi kulongosola kuti mpingo wakumaloko unafuna kumanga yofanana ndi zimenezo. Ndiyeno mkuluyo anafunsa ngati mpingo ukanagula malo oyandikana ndi puloti yake yaing’ono. Onojie anayankha kuti: “Usiku wapitawu nditatha kuonerera vidiyo ija, ndinalingalira chinthu chimodzimodzicho.” Atatero, anapima mamita asanu ndi imodzi a malo oyandikana ndi malo a mpingo. “Mungatenge ameneŵa,” iye anatero. “M’litali mungatenge monga momwe mufunira. Konzetsani zikalata, ndipo ndidzazisaina.”
[Mawu a M’munsi]
a Kuti mudziŵe zowonjezereka, onani Kalenda ya Mboni za Yehova ya 1994.
[Bokosi patsamba 9]
ZIŴERENGERO ZA DZIKOLO
Chaka Chautumiki cha 1993
CHIŴERENGERO CHAPAMWAMBA CHA OCHITIRA UMBONI: 174,582
KUGAŴA: Mboni 1 pa anthu 507
OFIKA PACHIKUMBUTSO: 473,245
AVAREJI YA OFALITSA AUPAINIYA: 19,777
AVAREJI YA MAPHUNZIRO A BAIBULO: 242,028
CHIŴERENGERO CHA OBATIZIDWA: 8,888
CHIŴERENGERO CHA MIPINGO: 3,289
OFESI YA NTHAMBI: BENIN CITY, BOMA LA EDO