Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 6/15 tsamba 23-27
  • “Kusodza” m’Madzi a Fiji

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Kusodza” m’Madzi a Fiji
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • “Kusodza” m’Mudzi Wachifiji
  • “Kusodza” Mwanjira Yachipoleneziya
  • Kusinthira ku Chitaganya cha Amwenye
Nsanja ya Olonda—1994
w94 6/15 tsamba 23-27

“Kusodza” m’Madzi a Fiji

FIJI​—dzinalo limakumbutsa munthu zithunzi za paradaiso wa ku South Seas. Madzi oonekera mobiriŵira, matanthwe akorali, makhwatha a ngole omagwedezeka ndi mphepo, mapiri obiriŵira, nsomba za m’madera otentha, zipatso zosiyanasiyana ndi maluŵa. Mungapeze zonsezi zochuluka pa gulu la zisumbu 300 limeneli lokhala pa mtunda wa pafupifupi makilomita 1,800 kumpoto kwa New Zealand mu South Pacific. Chifukwa chake, mungavomereze kuti Fiji angakhale chokhumba cha aliyense cha paradaiso wa m’dera lotentha.

Komabe, Fiji ndi wokondweretsanso koposa kukongola kwake kwachilengedwe. Inde, monga momwedi palili kusiyanasiyana kwa nsomba za m’matanthwe akorali, kusiyanasiyanako kumapezekanso pamtunda. Mwinamwake kusiyanasiyana kwa mafuko osakanikirana a Fiji kuli kosafanana ndi kwina kulikonse mu South Pacific. Magulu aŵiri aakulu koposa pakati pa nzika zake pafupifupi 750,000 ndiwo nzika Zachifiji, zimene zili Zachimelaneziya, ndi Amwenye obadwira mu Fiji, mbadwa za antchito obweretsedwa kuchokera ku India mkati mwa nthaŵi ya utsamunda wa Britain. Komanso pali Abanaba, Atchaina, Azungu, Agilbert, Arotuma, Atuvalu, ndi ena.

M’chitaganya chimenechi cha miyambo yosiyanasiyana, Mboni za Yehova zili zotanganitsidwa ndi ntchito ya “kusodza.” (Marko 1:17) Kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu nkovuta m’chitaganya cha anthu osiyasiyana chotere. Choyamba, pali zopinga za chinenero ndi mwambo zoti zilakidwe. Ngakhale kuti Chingelezi chili chinenero chogwiritsiridwa ntchito, nthaŵi zambiri Chifiji, Chihindi, Chirotuma, kapena zinenero zina zimagwiritsiridwa ntchito.

Mafikidwe osiyanasiyana ayeneranso kugwiritsiridwa ntchito pocheza ndi awo amene akulira m’zipembedzo zosiyanasiyana. Nzika zochuluka Zachifiji ndi anthu ena okhala pa zisumbupo ali azipembedzo Zachikristu zosiyanasiyana. Anthu Achimwenye apangidwa ndi Ahindu, Asilamu, ndi Asikh, Ahindu akumakhala ochuluka. Matchalitchi ndi ambiri m’matauni ndi m’midzi, koma pa zisumbu ziŵiri zazikulu koposa za Fiji, akachisi ambiri a Ahindu ndi misikiti ya Asilamu nzosiyana ndi zina.

Mboni zambiri zakumaloko zakula zikumalankhula zinenero zake zazikulu zitatu​—Chingelezi, Chifiji, ndi Chihindi. Kukhala ndi luso limeneli nkothandiza kwambiri mu ntchito ya “kusodza.” Nthaŵi zina anthu amadabwa kumva Mfiji akulankhula Chihindi mosadodoma ndipo Mhindu akulankhula Chifiji mosadodoma. Pokhala ndi kusiyana m’miyambo, m’chipembedzo, ndi m’chinenero kumene kuyenera kulakidwa, pamafunikira kafikidwe kosinthasintha kuti munthu akhale ‘woyanjana nawo uthenga wabwino.’​—1 Akorinto 9:23.

“Kusodza” m’Mudzi Wachifiji

Nzika Zachifiji ndi zaubwenzi, ndipo ndi anthu ochereza alendo. Nkovuta kuyerekezera kuti zaka zoposa pang’ono zana zapitazo, nkhondo zamafuko zinali zambiri. Kwenikweni, pa nthaŵi ya kufika koyamba kwa Azungu, Fiji anali kudziŵika monga Cannibal Islands (Zisumbu za Odya Anthu). Potsirizira pake, pamene mfumu yaikulu inayamba kulamulira ndi kutembenuka, kumenyana ndi kudya anthu kunatha. Kusiyana mafuko kunangotsalira m’zinenero zimene zimapezeka m’madera osiyanasiyana, ngakhale kuti chinenero cha Chibaua chimadziŵidwa m’madera ambiri.

Kuwonjezera pa Suva, malikuluwo, mu Fiji monse muli matauni ambiri. Afiji ambiri amakhala kumidzi yoyang’aniridwa ndi turaga ni koro, kapena nyakwaŵa. Poloŵa m’mudzi ‘kukasodza,’ ndi mwambo wake kufikira mwamuna ameneyu kuti mupemphe chilolezo cha kufikira bure zosiyanasiyana kapena nyumba za m’mudzimo. Ndi mwakamodzikamodzi chabe pamene pempholo limakanidwa, kaŵirikaŵiri, chifukwa cha kutsutsa Mboni za Yehova kochitidwa ndi atsogoleri ena achipembedzo a m’mudzimo. Kodi kufikira nyumba ya Mfiji kumakhala kotani?

Pamene tiloŵa mu bure, timakhala pansi mwachimwenye. Mawu oyamba okambidwa, mosamala ogwiritsiridwa ntchito kusonkhezera chikondwerero cha Akumadzulo, otanganitsidwawo ali osafunika kunoko. Aliyense wakudza kudzakamba za Mulungu amalandiridwa. Atapemphedwa, mwininyumba amanyamuka mwamsanga ndipo, ndi mawu akuti “tulou” (pepani), amapita pa shelefu ndi kutenga Baibulo Lachifiji ndi kuŵerenga mokondwa mavesi osiyanasiyana amene mtumiki wochezayo amatchula. Komabe, mkhalidwe wa kuchereza ndi waulemu Wachifiji umapereka vuto la mtundu wina. Kuzindikira kwabwino ndi luso zimafunika kuti eninyumba aloŵetsedwe m’makambitsirano, kuwalimbikitsa kutsatira kalingaliridwe kamene kakulondoledwa, kapena kuwathandiza kuona kufunika kwa kuyerekezera zikhulupiriro za iwo eni ndi ziphunzitso za Baibulo.

Kaŵirikaŵiri eninyumba Achifiji amakondwera kukambitsirana nkhani za chiphunzitso koposa kukambitsirana nkhani za mikhalidwe ya m’chitaganya. Kwenikweni, ambiri a Mboni za Yehova zoposa 1,400 zokangalikazo mu Fiji anakondweretsedwa ndi choonadi cha Baibulo chifukwa cha kukambitsirana pamafunso onga akuti, Kodi helo ndi malo amtundu wotani? Kodi ndani amene amapita kumwamba? ndi lakuti Kodi dzikoli lidzawonongedwa? Komabe, kuti munthuwe ubwererenso kwa anthu osonyeza chikondwerero, umafunikira kukhala wokhoza kusintha ndi wakhama. Pamene ubwererako panthaŵi imene munapangana, kaŵirikaŵiri umapeza kuti mwininyumbayo wapita ku teitei (kumunda) kapena kwina kwake. Ayi, sikuti sayamikira kufikako koma kungoti kaonedwe kawo ka nthaŵi ndi kena. Ndithudi, kwa Mboni za kumaloko, zimenezi si zachilendo. Izo zimachita khama mwa kufikanso panthaŵi ina. Kulibe maina a misewu kapena manambala a nyumba oyenera kulembedwa, chotero munthu afunikira kukumbukira bwino pamene afikanso panyumbapo.

“Kusodza” Mwanjira Yachipoleneziya

Tsopano, tiyeni ‘tikasodze’ ndi mtumiki woyendayenda, kapena woyang’anira dera, pamene akuchezera mpingo wina waung’ono mu Rotuma. Chiungwe chimenechi cha tizisumbu totumphuka chifukwa cha mavolokano chili pa mtunda wa makilomita 500 kumpoto kwa Fiji. Kuti tifikeko, tikuuluka ndi ndege ya mipando 19. Chisumbu chachikulu ndi chadera laukulu wa makilomita 50 chabe m’mbali zonse zinayi, chokhala ndi anthu pafupifupi 3,000. Msewu wamchenga umadutsa m’mbali mwa gombe, ukumagwirizanitsa midzi 20. Rotuma amayang’aniridwa ndi Fiji koma ali ndi mwambo wina ndi chinenero. Pokhala ndi chiyambi cha Chipoleneziya, anthu ake ndi osiyana maonekedwe ndi Afiji Achimelaneziya. Ponena za chipembedzo, ambiri a iwo ndi Aroma Katolika kapena a Methodist.

Pamene ndegeyo ikutsika ndi kuzungulira kuti itere, tikuona msipu wobiriŵira wa pa chisumbupo. Makhwatha aakulu a ngole onga nthenga akuoneka paliponse. Pali khamu lalikulu lodzachingamira otuluka m’ndege ya kamodzi pa mlungu. Pakati pawo pali kagulu ka Mboni. Tikulonjeredwa mwachikondi, ndipo madende a ngole angapo aakulu obiriŵira okhala ndi “maso” otsegulidwa akuperekedwa kwa ife kuti tiphe ludzu.

Titayenda pang’ono, tikufika pamalo athu okhala. Chakudya chophikidwa muuvuni ya dothi chakonzedwa. Nyama ya nkhumba yowotcha, nkhuku, nsomba zokazingidwa, nkhanu, ndi mbewu ya chomera chakumaloko chonga mtsitsi, taro, zikuikidwa patsogolo pathu. Ha, ndi phwando lotani nanga, ndipo ndi mkhalidwe wonga wa paradaiso chotani nanga umenewu pansi pa mitengo ya ngole!

Tsiku lotsatira tikufikira anthu a m’midzi, yotchedwa ho’aga m’Chirotuma. Pamene tikuyandikira nyumba yoyamba, kankhumba kamene kathaŵa m’khola lina kakudutsa mothamanga, kakumalira pamene kakupita. Mwininyumba wationa tikufika ndipo akutsegula chitseko ndi kumwetulira, akutipatsa moni wakuti “Noya!” m’Chirotuma, ndiyeno akutipempha kuti tikhale pansi. Nsengwa ya nthochi zakupsa ikuikidwa patsogolo pathu, ndipo tikupemphedwanso kumwa zakumwa za m’madende obiriŵira a ngole. Kuchereza alendo kumadza poyamba mu Rotuma.

Kuno kulibe okayikira kukhalapo kwa Mulungu kapena achisinthiko. Aliyense amakhulupirira Baibulo. Nkhani zonga chifuno cha Mulungu kaamba ka dziko lapansi zimasonkhezera chidwi chawo mosavuta. Mwininyumba akudabwa kudziŵa kuti dziko lapansi silidzawonongedwa koma lidzakhalidwa ndi anthu olungama amene adzakhalapo kosatha. (Salmo 37:29) Iye akutsatira mosamalitsa pamene mavesi a Baibulo amene amafotokoza mfundo imeneyi akuŵerengedwa, ndipo akulandira mokondwera buku lofokotoza Baibulo limene tikugaŵira. Pamene tikukonzekera kuchoka, iye akutithokoza chifukwa cha kufikako ndipo akutipatsa thumba lapulasitiki lodzala nthochi zakupsa zimene tingadye m’njira. Kunotu munthu akhoza kunenepa pamene akulalikira!

Kusinthira ku Chitaganya cha Amwenye

Ngakhale kuti maiko ena ambiri a zisumbu za ku South Pacific nawonso ndi amafuko ambirimbiri, Fiji ndi wapadera pa nkhani imeneyi. Limodzi ndi miyambo ya Chimelaneziya, ya Chimaikroneziya, ndi ya Chipoleneziya pali wina wotengedwa ku Asia. Pakati pa 1879 ndi 1916, antchito ochita nawo pangano a ku India anabweretsedwa kudzagwira ntchito m’minda ya nzimbe. Makonzedwe ameneŵa, otchedwa girmit (pangano), anachititsa zikwizikwi za Amwenye kudza ku Fiji. Mbadwa za antchito ameneŵa zimapanga mbali yaikulu ya anthu a dzikolo. Iwo asungabe mwambo wawo, chinenero, ndi chipembedzo.

Ku mbali yotetezereka ya chisumbu chachikulu cha Fiji kuli mzinda wa Lautoka. Umenewu ndiwo phata la indasitale ya nzimbe ya Fiji ndipo ndiko kwawo kwa mbali yaikulu ya anthu Achimwenye a m’dzikolo. Ziŵalo za mipingo itatu ya Mboni za Yehova kuno zifunikira kukhala zokhoza kusintha kwambiri m’ntchito yawo ya “kusodza.” Pofikira nyumba ndi nyumba, munthu afunikira kukhala wokonzekera kusintha mitu ya nkhani zikumadalira pa fuko ndi chipembedzo cha mwininyumba. Tiyeni tigwirizane ndi kagulu ka Mboni zakumaloko pamene zikufikira nyumba zokhalirana patalipatali pakati pa minda ya nzimbe kunja pang’ono kwa Lautoka.

Pamene tikuyandikira nyumba yoyamba, tikuona nsungwi zazitali zomangiriridwa tinsalu tofiira kunsonga zoimikidwa pangodya yakutsogolo ya mpanda wa nyumbayo. Zimenezi zikudziŵikitsa banjalo kukhala Lachihindu. Nyumba zambiri za Ahindu nzokongoletsedwa ndi zithunzithunzi za milungu yawo. Ambiri ali ndi mulungu wawo wokondedwa, monga ngati Krishna, ndipo kaŵirikaŵiri pamakhala kakachisi.a

Ahindu ambiri amakhulupirira kuti zipembedzo zonse ndi zabwino ndipo zangokhala njira zosiyanasiyana za kulambira. Motero, mwininyumba angamvetsere mwaulemu, kulandira buku, kupereka zoziziritsa kukhosi, ndi kulingalira kuti wachita mbali yake. Kuti mudzutse mafunso oloŵetsa eninyumba m’makambitsirano atanthauzo, kaŵirikaŵiri kumakhala kothandiza kudziŵa mbiri zina zimene zili mbali ya zikhulupiriro zawo. Mwachitsanzo, podziŵa kuti zina za mbiri zawo zimasonyeza kuti milungu yawo imachita zinthu zimene anthu ambiri angakayikire, tingafunse kuti: “Kodi mungavomereze mkazi (mwamuna) wanu kuchita khalidwe lotero?” Kaŵirikaŵiri yankho limakhala lakuti: “Ayi, kutalitali!” Ndiyeno, munthuyo angafunsidwe kuti: “Chabwino, kodi mulungu ayenera kuchita motero?” Kaŵirikaŵiri makambitsirano otero amatsegula mipata yosonyezera kufunika kwa Baibulo.

Chikhulupiriro cha kubadwanso kwa moyo, mbali ina ya Chihindu, chili nkhani yokondeka yokambitsirana. Mkazi wina Wachihindu wophunzira amene anali atangotayikiridwa ndi atate wake mu imfa anafunsidwa kuti: “Kodi mungakonde kudzaonanso atate wanu monga momwe analili poyamba?” Iye anayankha kuti: “Inde, zimenezo zingakhale zokondweretsa.” Malinga ndi yankho lakelo ndi kukambitsirana kotsatira, kunali kwachionekere kuti sanali wokhutiritsidwa ndi chikhulupiriro chakuti atate wake tsopano anali amoyo mu mpangidwe wina ndipo sadzawadziŵanso. Koma chiphunzitso cha Baibulo chokondweretsacho cha chiukiriro chinakhudza mtima wake.

Ahindu ena ali ndi mafunso ndipo akufunafuna mayankho okhutiritsa. Pamene Mboni inafika pa nyumba ina ya Mhindu, mwamunayo anafunsa kuti: “Kodi mulungu wanu dzina lake ndani?” Mboniyo inamuŵerengera Salmo 83:18 ndi kufotokoza kuti dzina la Mulungu ndilo Yehova ndi kuti pa Aroma 10:13 pamati kuti tipeze chipulumutso tiyenera kuitana pa dzina limenelo. Mwamunayo anachita chidwi ndipo anafuna kudziŵa zambiri. Kwenikweni, anali wofunitsitsa kudziŵa. Anafotokoza kuti atate wake, amene anali odzipereka kwambiri ku fano lawo la banja, anadwala atalilambira ndiyeno pambuyo pake kufa pasanapite nthaŵi. Chinthu chimodzimodzicho chinachitika kwa mkulu wake. Tsono iye anawonjezera kuti: “Fano limenelo likutibweretsera imfa, osati moyo. Chotero payenera kukhala kanthu kena koipa pa kulambiridwa kwake. Mwinamwake Mulungu ameneyu, Yehova, angatithandize kupeza njira ya ku moyo.” Chotero iye, mkazi wake, ndi ana ake aŵiri anayambitsidwa phunziro la Baibulo. Anapita patsogolo mofulumira ndipo posapita nthaŵi anabatizidwa. Iwo aleka kulambira mafano awo ndipo tsopano akuyenda m’njira ya Yehova, Mulungu wa moyo.

Kenako tikufika panyumba ya banja Lachisilamu. Mzimu wochereza wofananawo ukusonyezedwa, ndipo posapita nthaŵi takhala pansi titagwiriza zakumwa zoziziritsa kukhosi m’manja. Sitikuona zithunzithunzi zachipembedzo m’makoma kusiyapo vesi lolembedwa Mchiluya loikidwa m’feremu yaing’ono. Tikutchula kuti pali kugwirizana kodziŵika pakati pa Baibulo ndi Koran, ndiko kuti khololo Abrahamu, ndi kuti Mulungu analonjeza Abrahamu kuti kupyolera m’mbewu yake mitundu yonse ikadalitsidwa. Lonjezo limeneli liyenera kukwaniritsidwa mwa Yesu Kristu, Mwana Wake. Asilamu ena amakana lingaliro lakuti Mulungu ali ndi mwana. Motero, tikufotokoza kuti monga momwe munthu woyamba, Adamu, amatchedwera kuti mwana wa Mulungu chifukwa cha kulengedwa kwake ndi Mulungu, mofananamo, Yesu ali Mwana wa Mulungu. Mulungu safunikira mkazi weniweni woti abale ana otero. Chifukwa chakuti Asilamu samakhulupirira chiphunzitso cha Utatu, tikugwiritsira ntchito maziko odziŵika ameneŵa kusonyeza kuti Yehova Mulungu ndiye yekha wamkulukulu.

Pofika tsopano lino ndi masana, ndipo ziŵalo za kagulu kathu zikubwerera kumsewu, kuchokera kuminda ya nzimbe, kudzayembekezera basi yomka ku tauni. Ngakhale kuti ndi otopa pang’ono, onse ali osangalala ndi ntchito ya “kusodza” ya mmaŵayo. Zoyesayesa zopangidwa kusinthira kumikhalidwe yosiyanasiyana ndi zikhulupiriro zimene akumana nazo zinali zoyenerera.

Madzi a Fiji ndi matanthwe ali ndi mitundu yambiri ya nsomba. Kuti akhale wachipambano, gonedau (msodzi) Wachifiji amafunikira kukhala waluso pa ntchito yake. Zili chimodzimodzinso ndi ntchito ya “kusodza” imene Yesu Kristu anagaŵira ophunzira ake. Akristu amene ali “asodzi a anthu” ayenera kukhala aluso, akumasintha ulaliki wawo ndi zigomeko kuti zigwirizane ndi zikhulupiriro zosiyanasiyana za anthu. (Mateyu 4:19) Zimenezi zili zofunikadi ku Fiji. Ndipo zotulukapo zake zimaonekera pa misonkhano ya chaka ndi chaka ya Mboni za Yehova, pamene Afiji, Amwenye, Arotuma, ndi anthu a mafuko ena osanganikirana amalambira Yehova Mulungu mu umodzi. Inde, dalitso lake lili pa ntchito ya “kusodza” m’madzi a Fiji.

[Mawu a M’munsi]

a Onani buku lakuti Mankind’s Search for God, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc., masamba 115-17.

[Mapu patsamba 23]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Viti Levu

Vanua Levu

Suva

Lautoka

Nandi

0 100 km

0 100 mi

18°

180°

[Chithunzi patsamba 24]

“Bure,” kapena nyumba ya m’mudzimo

[Chithunzi patsamba 24]

Kachisi wa Ahindu mu Fiji

[Zithunzi patsamba 25]

“Kusodza” anthu kwachipambano mu Fiji

[Mawu a Chithunzi patsamba 24]

Ofesi ya Alendo ya Fiji

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena